• CHAKA CHOBADWA 1944

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1964

  • MBIRI YAKE Kale anali m’gulu la zigawenga zoukira boma ndipo sankakhulupirira zoti kuli Mulungu koma wakhala akutumikira Yehova kwa zaka 50 zapitazi.

NTHAWI yomwe ndinali wachinyamata ndinkakhumudwa kwambiri ndi zinthu zoipa zimene anthu achipembedzo ankachita. Sindinkamvetsa chifukwa chimene Mulungu sakuthetsera umphawi ndiponso zinthu zopanda chilungamo m’dzikoli. Anthu ambiri opita kutchalitchi sachita zimene Baibulo limaphunzitsa. Kenako ndinangoganiza zosiya kukhulupirira Mulungu ndipo ndinkaona kuti kusintha maboma andale n’kumene kungathetse mavuto m’dzikoli.

Mu 1962, ndinkakonda kuwerenga magazini ya Galamukani! Ndipo mu 1963, ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova. Zimene ndinaphunzira zinandifika pamtima. Ndinaphunzira kuti si Mulungu amene amayambitsa zoipa zimene anthu azipembedzo amachita. Ndinaphunziranso kuti Mulungu wakonzera anthu tsogolo labwino.  Patangotha miyezi iwiri kuchokera pamene ndinayamba kuphunzira, ndinayamba kuuza anthu ena kuti Ufumu wa Mulungu udzalowa m’malo mwa maboma andale. Ndinabatizidwa mu 1964 ndipo kenako ndinayamba upainiya wapadera mu 1966. Ndimaona kuti kuphunzira za Yehova kwanditeteza kwambiri. Anzanga ambiri amene ndinkaukira nawo boma anafa kapena anathawira kudziko lina. Ndimathokoza kwambiri Yehova chifukwa poyamba sindinkakhulupirira zoti kuli Mulungu koma tsopano ndili ndi chiyembekezo chenicheni chimene iye walonjeza.

M’bale Crispín akuchititsa lemba latsiku ku Beteli