Ankalalikira Mosamala

M’bale wina dzina lake Rafael Pared anakhala wofalitsa mu 1957 pamene anali ndi zaka 18. Panopa akutumikira ku Beteli limodzi ndi mkazi wake, Francia. Iye akukumbukira  kuti akapita kolalikira apolisi osavala yunifomu ankamutsatira. Apolisiwo ankafunitsitsa kumanga m’baleyu ndi anzake. Rafael anati: “Nthawi zina, tinkawazemba podutsa m’njira zing’onozing’ono ndiponso kudumpha mipanda.” Mlongo wina dzina lake Andrea Almánzar anafotokoza zimene iye ndiponso anthu ena ankachita kuti asamangidwe. Anati: “Tinkachita zinthu mosamala. Tikakhala mu utumiki tinkalalikira kunyumba ina kenako n’kudumpha nyumba 10 tisanakalalikire kunyumba ina.”

Bani Inachotsedwa

Mu 1959, Trujillo anali atalamulira zaka pafupifupi 30, koma zinthu zinayamba kusintha pa nkhani ya ndale. Pa June 14, 1959, anthu a ku Domincan Republic omwe ankakhala kumayiko ena analowa m’dzikoli n’cholinga choti ayesenso kulanda boma. Anthuwo analephera ndipo ena anaphedwa, pomwe ena anamangidwa. Ngakhale zinali choncho, adani ambiri a Trujillo anaona kuti boma lake likhoza kulandidwa ndipo anayamba kulimbana naye kwambiri.

Kwa zaka zambiri, tchalitchi cha Katolika chinkagwirizana ndi boma la Trujillo. Koma pa January 25, 1960, akuluakulu a tchalitchichi analemba kalata yodzudzula boma chifukwa chophwanya ufulu wa anthu. Katswiri wa mbiri yakale wa ku Dominican Republic dzina lake Bernardo Vega anafotokoza kuti: “Tchalitchi cha Katolika chinakakamizika kudzudzula boma la Trujillo. Chinatero chifukwa cha zimene zinachitika mu June 1959 komanso nkhanza zimene bomali linachitira anthu oukira komanso anthu ena amene ankadana nalo.”

Ntchito ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa kwa zaka zambiri. Koma mu May 1960, Trujillo anachita zinthu zodabwitsa pamene anachotsa lamulo loletsa a Mboni. Anachita zimenezi atasemphana maganizo ndi akuluakulu a tchalitchi cha Katolika.