Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 DOMINICAN REPUBLIC

Ofalitsa Akuwonjezereka

Ofalitsa Akuwonjezereka

A Mboni za Yehova Ali ndi Mbiri Yabwino

A Mboni za Yehova akwanitsa zaka pafupifupi 70 ku Dominican Republic. Anthu ambiri amayamikira a Mboni za Yehova. Nthawi zina anthu amapeza abale n’kupempha mabuku athu. Si zachilendo kumva anthu akunena mawu oti: “Anthu a chipembedzo ichi amandisangalatsa” kapena akuti “Anthu inu mumachitadi zimene Baibulo limanena.”

Chitsanzo pa nkhaniyi ndi zimene zinachitikira m’bale wina amene anapereka malo ake kuti pamangidwe Nyumba ya Ufumu. M’baleyu atapita kuboma kuti akalembetse malowo, anapeza kuti munthu wina analembetsa kale kubomako kuti malowo ndi ake. Munthuyo ankanena kuti m’baleyo ndi wakuba. Nkhaniyi inapita kukhoti ndipo inali yovuta kwambiri chifukwa munthuyo anali ndi mapepala osonyeza kuti malowo ndi ake.

Pa nthawi ina, oweruza milandu anafunsa loya wa m’baleyo kuti afotokoze bwinobwino za munthu yemwe ankamuimira. Loyayo anafotokoza kuti iye ankaimira Mboni za Yehova. Kenako woweruzayo anati: “Ngati ndi choncho ndiye kuti a Mboni za Yehovawo akunena zoona. Ndimawadziwa bwino ndipo amachita zinthu mwachilungamo. Sangachite zinthu mwachinyengo kuti alande munthu malo ake.”

Nkhaniyi itafika kukhoti zinadziwika kuti munthuyo anachita zinthu mwachinyengo ndipo woweruzayo anagamula mokomera m’baleyo. Loya yemwe ankaimira m’baleyo anati: “Si zachilendo kuti mlanduwu wayenda chonchi. M’makhoti onse m’dziko lino, a Mboni za Yehova amalemekezedwa kwambiri.”

 Akungoyembekezera Nthawi

Silikudziwa kuti ndi anthu angati m’tsogolomu amene angaphunzire za Yehova. Panopo abale akugwira mwakhama ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, mu 2013 abale analalikira maola oposa 11 miliyoni ndipo anachititsa maphunziro a Baibulo okwana 71,922. N’zosangalatsanso kuti abale 9,776 anachita upainiya. Mu August chaka chomwecho panali ofalitsa okwana 35,331 amene ankalalikira. Zikuonetsa kuti chiwerengero cha ofalitsa chikhoza kukwera chifukwa anthu 127,716 anafika pa mwambo wa Chikumbutso.

Ntchito yolalikira ku Dominican Republic inayambika Lamlungu lina mu April 1945, pamene Lennart and Virginia anafika m’dzikolo. A Mboni za Yehova amayamikira kwambiri zimene zinachitikazo. Amathokoza kwambiri abale oyambirira amene ankalalikira mwakhama. Iwo amayamikiranso kwambiri mwayi wochitira “umboni mokwanira za ufumu wa Mulungu.” (Mac. 28:23) Akungoyembekezera nthawi imene anthu onse pachilumbapo ndiponso padziko lonse adzaimbe kuti: “Yehova wakhala mfumu! Dziko lapansi likondwere ndipo zilumba zambiri zisangalale.”—Sal. 97:1.