Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu

Martín Paredes

Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu
  • CHAKA CHOBADWA 1976

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1991

  • MBIRI YAKE Martin anaphunzira za Yehova nthawi yomwe ankachita maphunziro aunsembe. Kuyambira nthawi imeneyi iye wathandiza anthu ambiri kuti azitumikira Yehova.

NDINAKULIRA m’banja lachikatolika lokonda kupemphera kwambiri ndipo makolo anga ankafunitsitsa kuti ndidzakhale wansembe. Ndiyeno ndili ndi zaka 12 ndinachita maphunziro atatu ndipo ndinaphunzitsidwa ndi ansembe osiyanasiyana. Mu 1990, ndili ndi zaka 14, ndinaitanidwa kuti ndikachite maphunziro pasukulu inayake yapamwamba kwambiri yophunzitsa za unsembe.

Zinkandiyendera kwambiri moti anandiuza kuti ngati ndingapitirize kuchita khama ndidzakhala bishopu. Koma ndinakhumudwa chifukwa m’malo mophunzira Baibulo tinkaphunzira nzeru za anthu. Ansembenso anali achiwerewere moti ankafuna kuti agone nane. Zimenezi zinkandipangitsa kufuna kusiya kutumikira Mulungu.

Tsiku lina munthu wina wogwira ntchito pasukulupo anapatsidwa buku la Achichepere Akufunsa ndi amishonale. Ndinabwereka  bukulo ndipo ndinaliwerenga lonse. Kenako ndinadziuza kuti: “Izi ndi zimene ndinkafuna.” Ndinachoka pasukulupo ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova kenako ndinayambanso kufika pamisonkhano. Ndiyeno mu July, 1991, patha miyezi 8 ndinabatizidwa. Kenako ndinayamba kuchita upainiya ndipo ndinakwatira Maria yemwe analinso mpainiya. Kuyambira mu 2006, takhala tikutumikira limodzi monga apainiya apadera. Sindifunanso zosiya kutumikira Mulungu ndipo ndikusangalala kuthandiza anthu kudziwa bwino Mulungu.