Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 DOMINICAN REPUBLIC

Kodi Mutu Ndi Ndani?

Kodi Mutu Ndi Ndani?

“Gulu Lawo Likhala Lopanda Mutu”

Pa July 13, 1957, mkulu wina wa apolisi dzina lake Colón analembera kalata nduna ina. M’kalatayo anati: “Mwambi wina umati: ‘Kupha njoka n’kudula mutu.’ Choncho kuti tithane ndi gulu la Mboni za Yehova tiyenera kuthamangitsa amishonale awo. Tikachita zimenezi, gulu lawo likhala lopanda mutu ndipo popanda mutuwu, a Mboniwo athera pomwepo.”

Pasanapite nthawi, nduna yoona za chitetezo inalamula kuti amishonale 10 amene anatsala achoke m’dzikoli. Pa July 21, 1957, M’bale Roy Brandt analembera kalata pulezidenti yopempha kuti akumane naye. Mawu ena a m’kalatayo anati: “Zimene anthu ena akuchita m’dzikoli podana ndi dzina la Yehova Mulungu ndi zofanana ndi zimene anthu ena ankachita atauzidwa zabodza zokhudza atumwi a Yesu.” Kenako M’bale Brandt anauza Pulezidenti Trujillo kuti awerenge chaputala 2 mpaka 6 cha Machitidwe ndipo anati: “Malangizo osapita m’mbali amene Woweruza Gamaliyeli anapereka ndi othandizanso kwambiri masiku ano.” Kenako m’baleyu analemba mawu a pa Machitidwe 5:38 ndi 39  m’zilembo zikuluzikulu kuti: “ALEKENI AMUNA AMENEWA CHIFUKWA NGATI NTCHITO IYI IKUCHOKERA KWA MULUNGU, MUKHOZA KUPEZEKA KUTI MUKULIMBANA NDI MULUNGU.” Koma izi sizinaphule kanthu. Pa August 3, 1957, amishonale anatengedwa kupita kubwalo la ndege kuti achoke m’dzikolo.

‘Yesu Ndi Mutu’

DM’bale Donald Nowills anayamba kuyang’anira ntchito kunthambi ali ndi zaka 20 zokha

Kodi zinawathera bwanji abale ndi alongo popeza amishonale onse anathamangitsidwa? Kodi analidi opanda mutu monga mmene mkulu wa apolisi uja ananenera? Ayi, chifukwa Yesu ndi ‘mutu wa thupi, lomwe ndi mpingo.’ (Akol. 1:18) Choncho si zoona kuti anthu a Yehova ku Dominican Republic anali opanda mutu. M’malomwake, Yehova ndi gulu lake anapitiriza kuwasamalira.

Amishonale atachoka, m’bale wina dzina lake Donald Nowills anapatsidwa udindo woyang’anira ntchito kunthambi.  Iye anali ndi zaka 20 zokha ndipo anali atabatizidwa zaka 4 zokha m’mbuyomu. Ngakhale kuti anakhala woyang’anira dera kwa miyezi ingapo, ntchito imene anapatsidwa kunthambi inali yachilendo kwa iye. M’bale Nowills anali ndi ofesi yaing’ono m’nyumba yake. Nyumbayo inali yamatabwa ndi malata ndipo pansi panalibe simenti. Inali kudera loipa lotchedwa Gualey mumzinda umene unali likulu la dzikoli. Iye limodzi ndi M’bale Félix Marte ankapanga fotokope magazini a Nsanja ya Olonda n’kumapereka kwa abale m’dziko lonseli.

Fotokope ya Nsanja ya Olonda ya mu 1958

Pa nthawiyo, M’bale Enrigue Glass anali kundende ndipo mkazi wake dzina lake Mary ankathandiza M’bale Nowills. Mary anati: “Ndinkaweruka kuntchito 5 koloko madzulo ndipo kenako ndinkapita ku ofesi ya M’bale Nowills kuti ndikatayipe Nsanja ya Olonda. Ndiyeno M’bale Nowills ankapanga fotokope magaziniyi pogwiritsa ntchito makina. Tikamaliza, mlongo wina wochokera ku Santiago ankatenga magaziniwa.  Mlongoyu tinkangomutchula kuti ‘mngelo’ n’cholinga choti anthu asadziwe dzina lake lenileni. Iye ankawaika m’chitini cha mafuta chachikulu. Kenako ankawafunditsa nsalu pamwamba pake n’kuikapo chinangwa, mbatata kapena zakudya zina. Ndiyeno pamwamba pake ankayalapo chiguduli. Akatero, ankakwera basi n’kupita kumpoto kwa dzikoli n’kukapereka magazini imodzi pa mpingo uliwonse. Abale ndi alongo ankabwerekana magaziniyi kuti aphunzire monga banja.”

Mary anati: “Tinkafunika kuchita zinthu mosamala kwambiri. Apolisi anali paliponse ndipo ankafunitsitsa kudziwa kumene tinkapanga fotokope Nsanja ya Olonda. Koma analephera chifukwa Yehova ankatiteteza.