Anapeza Choonadi

Juana Ventura anayamba kuphunzira Baibulo nthawi yomwe ntchito yathu inaletsedwa ku Dominican Republic ndipo anabatizidwa mu 1960 mumtsinje wa Ozama. Nthawi ina m’busa wa tchalitchi china ku Santo Domingo ankafuna kuti Juana amangidwe poganizira kuti mlongoyo ankaba anthu a tchalitchi chake. Pofuna kutsutsa zimene Juana ankaphunzitsa, m’busayo anamuitanitsa kutchalitchiko kuti akamufunse mafunso.

Juana anati: “Anandifunsa mafunso atatu. Loyamba linali loti, ‘N’chifukwa chiyani simuvota?’ Lachiwiri linali lakuti, ‘N’chifukwa chiyani simumenya nawo nkhondo?’ Lina linali lakuti, ‘N’chifukwa chiyani mumatchedwa Mboni za Yehova?’ Ndinkayankha pogwiritsa  ntchito Baibulo ndipo anthu a m’tchalitchimo ankatsegulanso Mabaibulo awo. Iwo ankadabwa poona zimene Baibulo limaphunzitsa. Ndipo ambiri anaona kuti apeza choonadi. Gulu lonse la anthu a m’tchalitchimo linayamba kuphunzira Baibulo ndipo anthu 252 anabatizidwa.” Zimenezi zinachititsa kuti ntchito yolalikira iyambe kuyenda bwino ku Santo Domingo.

A Mboni za Yehova Akhazikika

Panali mavuto osiyanasiyana azandale Trujillo ataphedwa. Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1963, linafotokoza kuti: ‘Asilikali ankalondera m’misewu ndipo kunkachitikanso zionetsero ndi ziwawa.’ Komabe ntchito yolalikira inkayenda bwino moti chakumapeto kwa 1963, ofalitsa analipo 1,155.

M’bale Nathan Knorr, wochokera kulikulu lathu atafika ku Dominican Republic mu 1962, anakonza zogula malo kuti pamangidwe ofesi ya nthambi. Malowo anagulidwa ndipo panamangidwa nyumba yansanjika ndiponso Nyumba ya Ufumu. Loweruka pa October 12, 1963, Frederick Franz anatsegulira ofesi ya nthambi yatsopano. Zinali zoonekeratu kuti a Mboni za Yehova akhazikika m’dziko la Dominicani Republic. Posakhalitsa Harry ndi Paquita Duffield, omwe anali amishonale omaliza kuthamangitsidwa m’dziko la Cuba, anafikanso.

Ofalitsa Ankawonjezeka Ngakhale Panali Mavuto Azandale

Pa April 24, 1965, mavuto azandale anayamba m’dzikolo komabe anthu a Yehova zinthu zinkawayendera. Pofika mu 1970, panali ofalitsa 3,378 ndiponso mipingo 63. Kuwonjezereka kwa chiwerengerochi  kunasonyeza kuti ofalitsa anawonjezeka ndi 50 peresenti pa zaka 5 zokha. Buku Lapachaka La Mboni za Yehova la 1972 linati: “Anthu osiyanasiyana anaphunzira za Yehova. Ena anali amakaniko, alimi, madalaivala, akatswiri owerengera ndalama, amisiri, akalipentala, maloya, madokotala ndiponso anthu omwe kale anali andale.”