Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 DOMINICAN REPUBLIC

Gawo la Chikiliyo cha ku Haiti

Gawo la Chikiliyo cha ku Haiti

Kutsegulira Gawo la Chikiliyo cha ku Haiti

Ntchito yolalikira yakhala ikuyenda bwino m’gawo la anthu olankhula Chisipanishi. Koma posachedwapa anthu olankhula zilankhulo zina akhala akufika m’dzikoli ndipo akumvetsera uthenga wa m’Baibulo. Dziko la Haiti linachita malire ndi dziko la Dominican Republic ndipo anthu ambiri akumeneko amalankhula Chikiliyo. Ngakhale kuti mayiko awiriwa sagwirizana kwenikweni, anthu ambiri a ku Haiti amapita ku Dominican Republic kukagwira ntchito ndipo chiwerengero chawo chakhala chikukwera pa zaka zapitazi.

Kwa zaka zambiri anthu olankhula Chikiliyo cha ku Haiti omwe ankaphunzira Baibulo, ankasonkhana m’mipingo ya Chisipanishi. Ndiyeno mu 1993, Bungwe Lolamulira linapempha nthambi ya ku Guadeloupe kuti itumize apainiya apadera olankhula Chikiliyo cha ku Haiti kukathandiza ku Dominican Republic. Barnabé ndi Germaine Biabiany linali banja loyamba pa mabanja atatu amene anavomera kusamukira kumeneko. Barnabé anati: “Poyamba tinali ndi timabuku tiwiri ta m’Chikiliyo. Mabuku ena onse anali a Chifulenchi ndipo tinkafunika kuwamasulira m’Chikiliyo cha ku Haiti.”

Mu January 1996, mumzinda wa Higüey munali ofalitsa 9 ndipo mumzinda wa Santo Domingo analimo 10. Ofalitsa a m’timagulu tam’mizinda iwiriyi  ankafunitsitsa kuthandiza anthu olankhula Chikiliyo cha ku Haiti. Kenako timaguluti tinakhala mipingo. Koma posakhalitsa mipingoyo inathetsedwa chifukwa zinkaoneka kuti anthu ambiri ankaphunzira Chisipanishi ndipo ankapitanso kumipingo ya Chisipanishi. Barnabé ananenanso kuti: “Tinakambirana ndi abale a m’Dipatimenti ya Utumiki kunthambi ndipo anatiuza kuti tiyenera kusiya kaye kulalikira m’gawo la anthu olankhula Chikiliyo cha ku Haiti.”

Zinthu Zinasintha M’gawo la Chikiliyo

Mu 2003, Bungwe Lolamulira linatumiza Dong ndi Gladys Bark omwe anali apainiya apadera kuti akalalikire m’gawo la anthu olankhula Chikiliyo ku Dominican Republic. Kwa zaka ziwiri ankalalikira mumzinda wa Higüey ndipo zinthu zinayamba kusintha. Pa June 1, 2005, mpingo wa Chikiliyo cha ku Haiti unakhazikitsidwa. Amishonale monga Dong Bark, Barnabé Biabiany ndiponso Steven Rogers ankalalikira mwakhama pothandiza anthu achilankhulocho m’dziko lonse la Dominican Republic.

Zinthu zinkayendadi moti mipingo yambiri inakhazikitsidwa. Pa September 1, 2006, panakhazikitsidwa dera loyamba la mipingo ya Chikiliyo. Panali mipingo 7 ndi timagulu tiwiri ndipo Barnabé Biabiany anali woyang’anira dera wake.

M’zaka zotsatira, amishonale ambiri ankatumizidwa kukalalikira ku Dominican Republic kukalalikira m’gawo la Chikiliyo. Abale ambiri ochokera ku Canada, Europe ndi ku United States anasamukira ku Dominican Republic kuti akathandize. Kagulu ka abale odziwa Chikiliyo kanauzidwa kuti kakaphunzitse abale a m’dzikolo ndiponso ochokera mayiko ena chilankhulochi.

Anthu ambiri akaona anthu olankhula Chikiliyo amaganiza kuti ndi a Mboni za Yehova

 Anthu ambiri ku Dominican Republic akuphunzira Chikiliyo ndipo zimenezi zikuthandiza kwambiri kuti anthu ochokera ku Haiti aziphunzira Baibulo. Chilankhulochi chathandizanso kwambiri ofalitsa a ku Dominican Republic kuti azimasukirana ndi anthu a ku Haiti akamawalalikira. Masiku ano anthu akangoona anthu a m’dzikolo akulankhula Chikiliyo cha ku Haiti amangodziwiratu kuti ndi a Mboni za Yehova.

Kuganizira anthu achikhalidwe china n’kothandiza kwambiri. Chitsanzo ndi mlongo wina ku Dominican Republic yemwe ndi mpainiya. Iye anachita nawo maphunziro apadera a chilankhulo cha Chikiliyo. Tsiku lina analalikira banja lina lochokera ku Haiti. Atapitanso anayamba kuphunzira nawo Baibulo. Mlongoyu anati: “Nditafika ndinakisa mkazi wa munthu wa ku Haiti patsaya mogwirizana ndi chikhalidwe cha azimayi a ku Dominican Republic. Mayiyo anayamba kulira. Nditamufunsa ananena kuti: ‘Pa zaka zonse zimene ndakhala kuno, aka n’koyamba kulandira moni wachonchi.’”

Yehova wakhala akudalitsa khama la abale ndipo chiwerengero cha ofalitsa chikuwonjezereka kwambiri. Pofika pa September 1, 2009, panali mipingo 23 ya Chikiliyo ndi timagulu 20 ndipo dera linanso linakhazikitsidwa. Chiwerengero cha anthu opezeka pa Chikumbutso mu 2011 chikusonyezanso kuti ofalitsa apitiriza kuwonjezereka. Mwachitsanzo, ofalitsa 11 m’tauni yaing’ono ya Río Limpio anasangalala kuona anthu 594 atafika pa Chikumbutso. Nthawi ina panakonzedwa zoti mwambo wa Chikumbutso ukachitikire m’tauni ya Las  Yayas de Viajama. M’tauniyi munalibe wofalitsa aliyense koma anthu 170 anafika pa Chikumbutso. Mu September 2011, panali mipingo 33 ndiponso timagulu 21 m’gawo la Chikiliyo. Mu 2012 panakhazikitsidwanso dera lina lachitatu.

Nthambi za ku Dominican Republic ndi Haiti zathandiza kwambiri abale olankhula Chikiliyo. Makalasi 5 a Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira ndiponso makalasi 4 a Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja akhala akuchitika m’Chikiliyo cha ku Haiti.

Akuphunzira Chikiliyo cha ku Haiti