Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 DOMINICAN REPUBLIC

Ndinazindikira Cholinga cha Moyo

José Estévez

Ndinazindikira Cholinga cha Moyo
  • CHAKA CHOBADWA 1968

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1989

  • MBIRI YAKE Ali mnyamata ankafunafuna moyo wabwino moti anaganiza zosamukira kutauni. Kutauniko n’kumene anaphunzira za Yehova ndipo wakhala akulalikira mwakhama za Ufumu wa Mulungu.

José anasamukira ku Santo Domingo ali ndi zaka 11 ndipo ankabulasha nsapato komanso kugulitsa zakudya kuti azipeza zinthu zofunika pa moyo. Pa nthawiyi ankadziwika monga mnyamata wolimbikira ntchito. Patapita nthawi mchimwene wake yemwe anali wa Mboni za Yehova anamupempha kuti azikagwira ntchito kunyumba kwake. Tsiku lina anaona buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi patebulo. Analitenga ndipo analiwerenga usiku wonse. Zimene anawerengazo zinamuthandiza kuzindikira cholinga cha moyo.

Ndiyeno tsiku lina Lamlungu anapita ku Nyumba ya Ufumu n’kukanena kuti nayenso ndi wa Mboni za Yehova. Anauza abale kuti iye waphunzira zoti ayenera kumasonkhana ndiponso kulalikira. Anawauzanso kuti m’buku limene anawerenga anaphunzira zinthu zimene Akhristu sayenera kuchita  ndipo anawatsimikizira kuti iye sachita zinthu zimene Baibulo limaletsa. Patatha masiku 15, José anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Ndiyeno patatha miyezi 6 iye anabatizidwa ali ndi zaka 21.

Popeza ntchito yomwe José ankagwira inkamuchititsa kuti azijomba kumisonkhano, anapeza ntchito ina ngakhale kuti inali ya malipiro ochepa. Ntchitoyi inamuthandiza kuti azipezeka pa misonkhano yonse ndiponso anayamba kuchita upainiya wokhazikika. Kenako anakwatira n’kukhala ndi ana awiri ndipo anasiya upainiya.

José ankafunitsitsa kuphunzitsa ana ake mfundo za m’Baibulo. Pamene mkazi wake anali woyembekezera, José ankawerenga mokweza Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Ankachita izi pofuna kuti mwana wake wosabadwayo azimvetsera. Pamene mwana wake woyamba dzina lake Noé ankabadwa, José anali atawerenga buku lonse. Anachitanso chimodzimodzi pamene mkazi wakeyo ankayembekezera kubadwa kwa mwana wawo wachiwiri dzina lake Neftalí.

Kenako José anakhala manijala pa kampani inayake ndipo ankalandira ndalama zambiri zedi kuposa ntchito yomwe ankagwira kale. Mu 2008, mwana wake wina ali ndi zaka 10 wina 13, iye anasiya ntchito n’kuyamba kuchita upainiya wokhazikika pamodzi ndi ana ake ndiponso mkazi wake. Popeza anali atasiya kugwira ntchito, onse pabanjapo anagwirizana kuti azikhala moyo wosalira zambiri. Onse pamodzi amachititsa maphunziro a Baibulo okwana 30 pamwezi. Yesu amatitsimikizira kuti tikamaika zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu pamalo oyamba Yehova adzatidalitsa. (Mat. 6:33) José ndi banja lake akhulupirira kwambiri mawuwa ndipo aonadi kuti Yehova amakwaniritsa zimene wanena.