Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 DOMINICAN REPUBLIC

Anazunzidwa Koopsa

Anazunzidwa Koopsa

“Onse Adzaphedwa”

M’bale Borbonio Aybar anabatizidwa nthawi ya bani pa January 19, 1955. Atangobatizidwa ankaphunzitsa Baibulo anthu ambiri ku Monte Adentro ndi ku Santiago. Ufulu utaperekedwa mu 1956, anthu ena amene ankawaphunzitsa komanso mkazi wake anabatizidwa.

Chapakati pa mwezi wa July mu 1957, akuluakulu a boma anakumana mumzinda wa Salcedo kuti akambirane zolimbana ndi Mboni. M’bale Aybar anati: “Francisco Prats-Ramírez ndi amene ankatsogolera pa zokambiranazi. Iye anati: ‘Onse adzaphedwa posachedwapa.’” Pofika pa July 19, 1957, apolisi anagwira a Mboni onse ku Blanco Arriba, ku El Jobo, ku Los Cacaos ndi ku Monte Adentro.

M’baleyu anati: “Ndinali m’gulu la anthu amene anagwidwa. Anatitengera kulikulu la asilikali ku Salcedo. Titangofika, mkulu wa asilikali dzina lake Saladín anandimenya. Maso ake anali atatuluka chifukwa cha ukali ndipo anatiopseza kwambiri. Kenako ananena kuti abale akhale pamzere wawo alongo pamzere wawo. Asilikali anayamba kumenya abale mateche ndi nkhonya pomwe alongo ankawakwapula ndi ndodo ndipo aliyense ankanena kuti: ‘Inetu ndi Mkatolika ndipo ndimapha.’”

“Ndawerenga Baibulo ndipo ndadziwa kuti Yehova ndi Mulungudi”

M’bale Aybar anauzidwa kuti alipire chindapusa komanso akhale kundende miyezi itatu. M’baleyu anati: “Nthawi ina tili kundendeko mkulu wina wa asilikali dzina lake Santos Mélido Marte anabwera kudzationa. Iye anati: ‘Ndawerenga Baibulo ndipo ndadziwa kuti Yehova ndi Mulungudi. Anthu inu simunalakwe chilichonse ndipo simuyenera kukhala m’ndende muno. Koma sindingathe kukumasulani chifukwa amene achititsa kuti  mumangidwe ndi mabishopu achikatolika. Amene angathandize kuti mumasulidwe ndi mabishopu omwewo kapena a pulezidenti.’”

“Kodi Ndiwe Bwana Wawo?”

Anthu ena amene anamangidwa anali mwana wa Mlongo Fidelia Jiménez ndiponso ana a mng’ono wake. Mlongoyu ndi amene anaphunzitsa onsewa. Mlongo Fidelia sanagwidwe koma anangodzipereka kuti amangidwe n’cholinga choti azikalimbikitsa anzake kundendeko. Ndiyeno tsiku lina kunafika mkulu wina wa asilikali dzina lake Ludovino Fernández. Iye ankadziwika kwambiri chifukwa cha matama komanso nkhanza. Atafika anaitanitsa mlongoyu n’kumufunsa kuti, “Kodi iwe Ndiwe Bwana Wawo?”

Fidelia anayankha kuti: “Ayi. Mabwana ndi inuyo.”

Ndiyeno Fernández anati: “Okhe, koma ndiwe m’busa eti?”

Fidelia anati: “Ayinso. M’busa wathu ndi Yesu.”

Kenako Fernández anafunsa kuti: “Kodi iwe si amene wachititsa kuti anthu onsewa amangidwe? Iweyo ndi amene unkawaphunzitsa. Ukukana, ukuvomera?”

Fidelia anati: “Ndikukana. Anthuwa amangidwa chifukwa cha Baibulo. Iwo amachita zimene aphunzira m’Baibulo.”

Ali pomwepo, abale awiri amene anamangidwanso anadutsa. Abalewo anali Pedro Germán ndi Negro Jiménez. Negro anali pachibale ndi Fidelia. Pa nthawiyo ankawachotsa kuselo yaokha kupita nawo kumaselo amene kunali anthu ena. Malaya a Negro anali magazi okhaokha ndipo diso la Pedro linali litatupa kwambiri. Fidelia ataona zimenezi, anafunsa mkulu wa asilikaliyo kuti: “Koma zoona anthu abwino, oona mtima komanso oopa Mulungu mukuwachita zimenezi?” Fernández ataona  kuti Fidelia sakuchita mantha anauza anthu kuti abwerere naye kuselo yake.

Atumiki a Yehova okhulupirika anakhalabe olimba mtima pamene ankazunzidwa. Ngakhale akuluakulu a boma ankadziwanso zimenezi. Mwachitsanzo, pa July 31, 1957, munthu wina waudindo waukulu mu ofesi ya pulezidenti analembera kalata nduna ina ya mu ofesiyo kuti: “Boma linakhazikitsa lamulo loti gulu lachipembedzo lotchedwa Mboni za Yehova si lololeka ndipo siliyenera kugwira ntchito zake m’dziko lino. Koma a Mboni ambiri akupitirizabe kugwira ntchito yawo mosabwerera m’mbuyo.”