Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

Dominican Republic

Dominican Republic

MU 1492, Christopher Columbus anapita m’mayiko ena amene ankaona kuti akhoza kupezako chuma ndi zinthu zina zabwino. Pa mayikowa, panali chilumba china chimene iye anachipatsa dzina loti La Isla Española kapena kuti Hispaniola. Panopa, mbali yaikulu ya chilumbachi ili m’dziko la Dominican Republic. Masiku ano, anthu ambiri a m’dzikoli atulukira zinthu zina zofunika kwambiri. Iwo aphunzira zoti dziko latsopano likubwera ndipo mudzakhala chilungamo chifukwa lizidzalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu. (2 Pet. 3:13) Werengani nkhani yosangalatsa ya anthu amtima wabwino amene anaphunzira zinthu zimenezi.

M'CHIGAWO ICHI

Mfundo Zachidule Zokhudza Dominican Republic

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zachidule zokhudza dzikoli komanso anthu ake.

Ntchito Inayambika

Kodi amishonale oyambirira anayamba liti kuphunzitsa anthu Baibulo ku Dominican Republic?

“Tidzawapeza”

Pablo González anapeza anthu amene ankawafufuza patatha zaka 13.

Anamangidwa Ndipo Ntchito Yolalikira Inaletsedwa

Kodi n’chiyani chinathandiza anthu ena a Mboni za Yehova kuti apirire mavuto oopsa amene ankakumana nawo kundende?

Ntchito Yolalikira Inapitirirabe

Polemba maola ndi maulendo obwereza, ofalitsa ankangolemba zinthu monga kabichi ndi spinachi.

Ufulu Wosayembekezereka Kenako N’kuletsedwanso

Ntchito ya a Mboni za Yehova inaletsedwa kwa zaka 6 kenako mu 1956 anapatsidwa ufulu kwa miyezi 11 yokha.

Ubwenzi wa Trujillo ndi Tchalitchi cha Katolika

Akuluakulu a Katolika ankaikira kumbuyo ulamuliro wa Trujillo kwa nthawi yaitali koma anasintha maganizo n’kupepesa anthu a ku Dominican Republic.

Anazunzidwa Koopsa

A Mboni anaukiridwa koopsa koma sanabwerere m’mbuyo.

Kodi Mutu Ndi Ndani?

Ankagwiritsa ntchito makina opanga fotokope, chitini cha mafuta, saka ndi chinangwa pothandiza kuti abale azilandira magazini pa nthawi ya bani.

Tikanatha Kumangidwa Nthawi Iliyonse

Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ku Domincan Republic analetsedwa kusonkhana, sanasiye koma ankasamala kwambiri kuti anthu asadziwe.

Sanasiye Kulalikira Ndipo Analandira Ufulu

Kwa zaka zambiri, ntchito ya Mboni za Yehova ku Dominican Republic inali yoletsedwa. Koma munthu amene ankaganiza kuti sangawathandize anachotsa baniyo.

“Ndinkamenya Nkhondo Ngati Mkango”

Luis Eduardo Montás, anayesa kawiri kuti aphe pulezidenti. Pamene ankayesa kachitatu, anapeza mwayi wophunzira Baibulo.

“Ufumu wa Mulungu Si Nkhambakamwa”

Efraín De La Cruz anatsekeredwa m’ndende 7 ndiponso kumenyedwa koopsa chifukwa cholalikira uthenga wabwino. N’chiyani chinamuthandiza kuti azilalikira mwakhama kwa zaka zoposa 60?

“Sindidzasiya Kukhala wa Mboni za Yehova”

Wansembe anauza Mary Glass kuti apenga akawerenga Baibulo. Koma analiwerengabe ndipo anazindikira chifukwa chake wansembe uja sankafuna kuti aliwerenge.

Ufulu Wolalikira

Trujillo ataphedwa, amishonale ambiri anafika ndipo pang’ono ndi pang’ono anthu anasiya kudana ndi Mboni za Yehova.

A Mboni za Yehova Akhazikika

Ntchito yolalikira inkayenda bwino ngakhale panali mavuto azandale. Kodi n’chiyani chinasonyeza kuti a Mboni za Yehova akhazikika ku Dominican Republic?

Panafunika Olalikira Ufumu Ambiri

Nkhani yokhudza Mboni za Yehova ku Dominican Republic singakhale yosangalatsa ngati sitingafotokoze za anthu amene anamvera pempho loti adzalalikire m’dzikoli.

A Mboni za Yehova Amathandizana

Chimphepo chitawononga ku Dominican Republic mu 1998, a Mboni za Yehova anathandizana kwambiri ndipo izi zinalemekeza Yehova Mulungu.

Panafunika Kumanga Malo Ena Olambirira

Kodi a Mboni za Yehova anatani ataona kuti malo ochitira misonkhano akuchepa ndipo pakufunika abale oyenerera kuti azitsogolera?

Gawo la Chikiliyo cha ku Haiti

A Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino kwa anthu olankhula Chikiliyo cha ku Haiti. Panopa kuli mipingo yambiri ndipo anthu ambiri akuphunzira chilankhulochi.

Ku Haiti Kunachitika Chivomezi

Ku Haiti kutachitika chivomezi mu 2010, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Dominican Republic inapereka chithandizo chambiri. Abale ambiri anapitanso kukathandiza.

Ofalitsa Akuwonjezereka

Ntchito yolalikira ku Dominican Republic inayambika mu 1945. Abale akungoyembekezera kuti zinthu zikhala bwanji mtsogolo.

Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri

Nthawi imene Leonardo Amor anali mumzinda wa La Vega, palibe amene ankafuna kuphunzira Baibulo. Koma kenako mitima ya anthu ambiri inadzasintha.

Anthu 22 Anasiya Tchalitchi Chawo

Anthu ankanena kuti zimene a Mboni za Yehova ankaphunzitsa zinali za jabulosi komanso zosokoneza. Koma a Mboniwo ankagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso mofika pa mtima.

Sankakhulupirira Zoti Kuli Mulungu Kenako Anayamba Kumutumikira

Juan Crispín sankakhulupirira zoti kuli Mulungu ndipo ankaona kuti kusintha maboma andale n’kumene kungathetse mavuto m’dzikoli. Kodi n’chiyani chomwe chinamusintha maganizo kuti ayambe kutumikira Mulungu?

Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo

José Pérez anali munthu wa Chinenero Chamanja woyamba kukhala wa Mboni ku Dominican Republic. Kodi ndi nthawi iti imene anayamba kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo?

Ndinazindikira Cholinga cha Moyo

José Estévez ndiponso banja lake anazindikira cholinga cha moyo. Kodi atsimikizira bwanji kuti Yehova amakwaniritsadi mawu ake?

Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu

Ngakhale kuti Martín Paredes ankaphunzira za unsembe anakhumudwa ndipo ankafuna kusiya kutumikira Mulungu. Kodi buku limene anabwereka linamuthandiza bwanji?