• MAYIKO 29

  • KULI ANTHU 40,208,390

  • OFALITSA 97,583

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 64,675

Ankagawira Timaphukusi Tamabuku

Zimakhala zovuta kuti anthu akalalikire m’zilumba zina ku Micronesia. Ndiyeno abale ndi alongo a ku Marshall Islands ananyamuka ulendo wa masabata awiri. Ulendowu unali wa pa boti. Iwo anachoka kuchilumba cha Majuro, n’kukafika kuzilumba zina ziwiri.

Kuti ntchito yawo iyende bwino, abalewa asananyamuke anakonza  timaphukusi tamabuku. M’kaphukusi kalikonse ankaikamo magazini 4 ndi timabuku tiwiri. Anachita izi podziwa kuti zidzakhala zovuta kubwererako. Ndiyeno akapeza munthu wofuna kuphunzira, ankamusiyira kaphukusiko kuti akatsala azigawira anzake kapena achibale ake. Pa masabata awiriwo, abale ndi alongowa anagawira timabuku 531 magazini 756 ndi mabuku 7.

“Tikuthokoza Chifukwa Chotikumbukira”

Mu February 2014, alongo 5 ndi m’bale mmodzi a ku Papua New Guinea ananyamuka ulendo wa masiku 10 kupita kuchilumba china. Kumeneko anapeza anthu ambiri ofuna kuphunzira ndipo tikaphatikiza magazini ndi mabuku amene anagawira anakwana 1,064. Mlongo wina dzina lake Relvie anati: “Tsiku loyamba tinalalikira mpaka m’ma 3 koloko madzulo ndipo madzi anatithera. Tinalakhula kwambiri moti mkamwa mwathu munali gwa ndipo nsagwada zinkatipweteka. Ndiyeno ndikulankhula ndi mtsikana wina, ndinkafuna kuwerenga lemba koma ndinalephera chifukwa cha ludzu. Nthawi yomweyo mtsikanayo anandipatsa madzi.”

Ndiyeno usiku womaliza m’mudzi wina, tinachita msonkhano. Panafika anthu a m’mudzimo ndipo panali atsogoleri azipembedzo. Relvie anati: “Ndinkamva ngati ndine Sitefano ndipo ndili pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Kusiyana kwake kunali koti anthu amene tinali nawo ankasangalala nafe.” Ofalitsa 6 aja atamaliza kulankhula, mphunzitsi wamkulu wa Sande Sukulu ya chipembedzo cha Lutheran anaimirira  n’kuthokoza mayi ake aakulu omwe anali m’gulu la ofalitsawo. Pothokozapo ananena kuti: “Mwachita bwino kwambiri. Muli ngati mkazi wachisamariya amene anapita kwa achibale ake kukawauza zinthu zabwino zimene anamva kwa Yesu. Tikuthokoza kwambiri chifukwa chotikumbukira.”

Kodi Ana Ang’ono Angalalikire?

Kiribati: eariki ndi Tueti

Pachilumba cha Tarawa m’dera la Kiribati, pali kamnyamata ka zaka 7 dzina lake Teariki. Tsiku lina kankalalikira ndi bambo ake dzina lawo a Tueti. Atafika panyumba ina anapeza anthu 10 a zaka za m’ma 20. Bambowo atawalalikira, m’modzi wa anthuwo anati: “Anthu inu mumakonda kulalikira ndi tiana. N’chifukwa chiyani mumawavutitsa chonchi? Kodi ana ang’ono angalalikire?”

Tueti anayankha kuti: “Kapena mukufuna kuti akulalikireni? Bwanji ineyo ndituluke ndiyeno mumve zimene angakuuzeni.” Onse anayankha kuti: “Tatulukani tione.”

Tueti atatuluka, mwanayo anafunsa anthuwo kuti: “Kodi mumalidziwa dzina la Mulungu?”

M’modzi wa anthuwo anayankha kuti: “Ndi Yesu!” Ndipo wina anayankha kuti “Mulungu.” Wina anayankha kuti: “Ambuye.”

Ndiyeno mwanayo anati: “Tiyeni tione zimene Baibulo limanena. Tiwerenge Yesaya 42:5.” Atawerenga limodzi anawafunsa kuti: “Kodi lembali likunena za ndani?”

Mtsikana wina anayankha kuti: “Likunena za Mulungu.” Ndiyeno mwanayo anati: “Ee Mulungu woona. Ndiyeno kodi Mulungu woonayo akutiuza zotani pa vesi 8? Apa akuti ‘Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli,  ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense.’ Tsopano mwaliona dzina la Mulungu?”

Onse anayankha pamodzi kuti, “Ee. Ndi Yehova.”

Mwanayo ataona kuti aliyense akuchita chidwi anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa ubwino wogwiritsa ntchito dzina la Mulungu lakuti Yehova? Kuti tipeze yankho, tiyeni tiwerenge Machitidwe 2:21. Lembali likuti, ‘Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.’ Ndiyeno lembali lati ubwino wake ndi wotani?”

Mtsikana wina pagululo anati, “Kuti tidzapulumuke.”

Pa nthawiyi bambo a Teariki analowa ndipo anafunsa anthuwo kuti: “Mwaona bwanji? Kodi ana ang’ono sangalalikire? Kodi n’kulakwa kuti tiziyenda nawo  polalikira?” Onse pagululo anavomereza kuti anawo amadziwa zinthu ndipo m’pomveka kuti azilalikira. Kenako bambowo anati: “Inunso mukanaphunzira Baibulo ngati mmene Teariki wachitira, bwenzi mukulalikira bwinobwino.”

Uthenga Wabwino Unafika Kumidzi ya Kumapiri

M’bale wina dzina lake Jean-Pierre amagwira ntchito pa ofesi ya omasulira mabuku ku Port-Vila ku Vanuatu. Mu November 2013, iye anayenda ulendo wa pa ndege kupita pachilumba china kukachita msonkhano wadera. Atangotsika ndege, anthu ochokera kum’mwera kwa chilumbachi anafika n’kumupempha mabuku. Iye anagawira magazini onse amene anatenga. Kenako mtsogoleri wa chipembedzo wina anafika kudzapemphanso mabuku. Anapemphanso kuti iye apite kumudzi wawo ndipo anati: “Kulitu njala ya Mawu a Mulungu. Mubwere mudzatiyankhe mafunso athu.” Msonkhanowo utatha, Jean-Pierre anauyamba ulendo wopita kumudziwo ndipo unali pamwamba penipeni pa phiri. Atafika analandiridwa bwino kwambiri n’kukambirana nawo kapepala ka Uthenga Wabwino Nambala 38 konena zoti akufa adzauka. Panali anthu pafupifupi 30 ndipo anawauza kuti aziona m’Mabaibulo awo zimene iye akuwerenga. Anthuwo anali anjaladi moti zokambiranazi zinatenga maola 7. Wachikulire wina wa zaka 70 anati: “Ine chibadwire sindinamvepo mfundo zomveka chonchi zokhudza akufa.”

Jean-Pierre anagona komweko m’chipinda chimodzi ndi wansembe. Podzuka m’mawa, anapeza kuti wansembeyo akuwerenga magazini. Ndiyeno Jean-Pierre anamufunsa kuti: “Mukuwerenga za chiyani?” Iye anayankha mosangalala kuti akuwerenga za Ufumu wa Mulungu. Anavomereza zoti Ufumu wa Mulungu sunali  m’mitima ya Afarisi amene Yesu ankalankhula nawo pa Luka 17:21. Ndiyeno anapitiriza kuti zimene tchalitchi chake chimanena, zoti Ufumu wa Mulungu umakhala m’mitima ya anthu, si zoona. Jean-Pierre atabwerera ku Port-Vila anapitiriza kukambirana pa foni ndi anthu amene anawapezawo. Abale atatu a mpingo wapafupi anadzipereka kuti akachite Chikumbutso pachilumbachi ndipo kunasonkhana anthu 109.

Vanuatu