Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Europe

Europe
  • MAYIKO 47

  • KULI ANTHU 741,311,996

  • OFALITSA 1,611,036

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 847,343

Ana Asukulu Anapita Kukaona Nyumba ya Ufumu

Finland: Ana a sitandade 4 ali m’Nyumba ya Ufumu

Ku Finland kuli mtsikana wina wa sitandade 4 dzina lake Ines. Iye atazindikira kuti m’kalasi yawo adzaphunzira zokhudza a Mboni za Yehova, anapempha zoti anzakewo adzapite kukaona Nyumba ya Ufumu. Anawo ndiponso aphunzitsi awo anagwirizana nazo.

Mlungu wotsatira ana 38 anapalasa njinga zawo mtunda wa  makilomita 5 kupita ku Nyumba ya Ufumu. Pa ulendowu panali aphunzitsi awiri ndiponso ahedi a pasukuluyo. Abale awiri ndiponso alongo atatu ndi amene anawalandira pa Nyumba ya Ufumu. Pamene ankapuma, anawo ankafunsa mafunso osiyanasiyana monga akuti: “Mukakumana muno mumatani?” Ataona laibulale anafunsa kuti: “Nanga umo mumatani?” Ataona lemba lachaka la pa Mateyu 6:10 anafunsa kuti: “Bwanji mwalemba samu yogawa pakhoma yoti 6 kugawa ndi 10?”

Popeza kusukulu amaletsa kuzunzana, abalewo anawaonetsa vidiyo ya pa jw.org yofotokoza za ana omwe amazunza anzawo. Abalewo anafotokozanso mbali zambiri za webusaiti yathu kenako anawaikira nyimbo ya Ufumu. Anawo anakhala pa Nyumba ya Ufumuyo kwa ola lathunthu.

Anawa ndiponso aphunzitsi awo anasangalala kwambiri ndi ulendowo. Ahedi anasangalala ndi webusaiti yathu ndipo anaona kuti ikhoza kuthandiza kwambiri pophunzitsa ana zokhudza chipembedzo. Anasangalalanso atamva kuti ana ena akhoza kubwera kudzaona Nyumba ya Ufumuyo. Tsiku lotsatira mphunzitsi wa kalasi ina anapempha kuti ana a m’kalasi yake akaonenso Nyumba ya Ufumu.

Anapeza Chuma Kumtaya

Mayi wina wa ku Romania, dzina lake Cristina, sanapite kusukulu. Iye ndi wosauka kwambiri moti ntchito yake ndi yotoleza mabotolo kumtaya. Tsiku lina akutoleza anaona kabuku ka zithunzi zokongola komanso ka anthu osangalala. Ataona ankadziuza kuti: “N’kuthekatu kuti kwinakwake anthu amasangalala chonchi.” Iye ankafunitsitsa kudziwa zimene zili m’kabukuko. Ndiye anapempha munthu wina kuti amuwerengere. Atamva  zoti ndi ka Mawu a Mulungu anadandaula kwambiri. Ankaona kuti si nzeru kutaya choncho mabuku onena za Mulungu. Mayiyu anapitiriza kutola timabuku, timapepala ndiponso magazini athu. Zina zinkakhala zabwinobwino koma zina zinkakhala zong’ambika. Kenako iye anaphunzira kuwerenga n’cholinga choti azidziwerengera yekha mabukuwo.

 Pa nthawi ina, a Mboni za Yehova anamupeza ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo. Iye anasangalala kudziwa kuti Yehova anamukoka pogwiritsa ntchito timabuku timene anthu ena anataya. Iye amapezeka pa misonkhano ndipo amasangalala ndi zimene amaphunzira. Chimene chimamusangalatsa kwambiri n’chakuti panopa amapeza mabuku, timabuku ndiponso magazini anyuwani. Sachita kukatoleza kumtaya. Apatu tingati Cristina anapeza chuma kumtaya.

Phunziro la Baibulo la M’nkhalango

Germany: Margret akuchititsa phunziro la Baibulo kunkhalango

Mlongo wina ku Germany dzina lake Margret, ankakonda kukayenda kunkhalango ndi galu wake. Iye anati: “Ndimakonda kulankhula ndi anthu amene ndakumana nawo. Ngati akufuna kuti ticheze ndimayamba kuwalalikira.”

Tsiku lina anakumana ndi mayi wina wa zaka za m’ma 70, alinso ndi galu wake. Margret anayamba kucheza naye. Mayiyo anasangalala kwambiri ndipo anauza mlongoyo kuti amapemphera ndiponso amawerenga Baibulo tsiku lililonse. Ndiyeno tsiku lililonse ankakumana ndi kukambirana zinthu zokhudza Mulungu. Nthawi ina mayiyo anafunsa Margret kuti: “Kodi zinatheka bwanji kuti mudziwe Baibulo chonchi?” Margret anamuuza kuti: “Ndine wa Mboni.”

Nthawi zonse Margret ankapempha mayiyo kuti aziphunzira naye Baibulo kunyumba kwake koma ankakana. Koma ankachezabe kunkhalangoko. Patapita miyezi yambiri Margret anapemphanso mayi uja kuti  aziphunzira naye Baibulo. Iye anafotokoza kuti amaopa kuphunzira chifukwa mwamuna wake amadana ndi a Mboni za Yehova.

Tsiku lina Margret anapita kunkhalango kuja, atatenga Baibulo ndiponso buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ndiyeno atakumana ndi mayi uja Margret anafunsa kuti: “Kodi mungakonde kuphunzira Baibulo munkhalango muno osati kunyumba?” Mayiyo anavomera kwinaku misozi ili mbwembwembwe. Iye amabwera kudzaphunzira Baibulo m’nkhalangomo kwa masiku 6 pa mlungu. Ngati sikunache bwino, Margret amatenga ambulera ndi tochi kuti ziwathandize.

Povomera Anapukusa Mutu

Ku Bulgaria kuli mlongo wina dzina lake Delphine. Mlongoyu ankaphunzira ndi mayi wina dzina lake Irina. Mayiyu ankasangalala ndi zimene ankaphunzira ndipo sankajomba ku misonkhano. Koma mwamuna wake sankafuna kuti aziphunzira ndi a Mboni. Choncho mwamunayo anaganiza zosamuka ndi mkazi wakeyo kupita ku Sweden. Zitatero, Delphine sankakumananso ndi a Mboni. Ndiyeno alongo awiri a ku Sweden, omwe akuchita upainiya, anamupeza. Mayina a apainiyawo ndi Alexandra ndi Rebecca. Iwo ataona kuti mayiyo sadziwa Chiswidishi, anagwiritsa ntchito kabuku kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse. Anauza Irina kuti awerenge uthengawo m’Chibugariya. Kenako anamufunsa ngati akufuna mabuku m’chilankhulo chakecho. Atatero, Irina anapukusa mutu kwambiri. Izi zinachititsa kuti alongowo angouyambapo poganiza kuti akukana.

Kenako Alexandra anakumbukira zoti mlongo wina wa ku Sweden dzina lake Linda, amene ankatumikira  ku Bulgaria, adzafika pakangodutsa milungu yochepa. Ndiyeno anaganiza kuti mwina Irina adzasintha maganizo akadzamva uthenga wa m’Baibulo m’chilankhulo chake. Linda atafika, Alexandra anamupempha kuti apitire limodzi kwa Irina. Mayiyu anauza Linda kuti ankapempha Yehova tsiku lililonse kuti amuthandize kupitiriza phunziro lake. Anati nthawi iliyonse ankayenda ndi buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Iye ankafuna kuti aonetse a Mboni alionse amene angakumane nawo koma sankawapeza. Irina anasangalala kwambiri kulandira mabuku ena a Chibugariya.

Ndiyeno Linda anafunsa Alexandra kuti: “Kodi n’chiyani chinakuchititsa kuganiza kuti safuna kuphunzira?” Alexandra anayankha kuti: “Titamufunsa anapukusa mutu.” Ndiyeno Linda anayamba kumwetulira n’kunena kuti: “Ukaona anthu a ku Bulgaria akugwedezera mutu ndiye kuti akukana koma ngati akupukusa mutu ndiye kuti akuvomera.” Panopa Irina akupitiriza phunziro lake ndi Delphine m’Chibugariya. Phunziroli limachitika pa sikayipi.

Bambo Anapereka Chitsanzo Chabwino

Ku Spain kuli mtsikana wina dzina lake Jemima ndipo bambo ake dzina lawo ndi Domingo. Iye anayamba kuphunzira Baibulo ali wamng’ono koma zinthu zinasintha atafika zaka 7. Mayi ake ananena kuti safuna kukhala wa Mboni za Yehova ndipo anathetsa banja. Ndiyeno atafika zaka 13, Jemima anasiya kusonkhana ndipo sankafuna kuti bambo ake azimuuza zokhudza Yehova.

Pamene ankakula, mtsikanayu analowa m’magulu andale komanso magulu ena n’cholinga choti boma lizichitira chilungamo anthu wamba. Nthawi ina  atasowa ntchito, bambo ake anamupempha kuti azigwira naye ntchito yopenta.

Tsiku lina akugwira ntchitoyi, bambo akewo anamupempha kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo. Iye anakana n’kunena kuti akadzafuna adzawauza. Pogwira ntchitoyi, bambowo ankakonda kumvetsera nkhani za m’magazini pomwe mtsikanayo ankakonda kumvetsera nyimbo za pop.

Domingo anakwatiranso ndipo mu November 2012 anaitanidwa ku Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Akhristu Apabanja. Jemima anadabwa kumva kuti bambo ake akusiya zonse kuti apite kusukulu ndipo akamaliza maphunzirowo adzalolera kupita kulikonse kumene angatumizidwe. Apa anadziwa kuti bambo akewo amakonda kwambiri kutumikira Mulungu ndipo anafuna kudziwa zimene zinawathandiza kukhala ndi mtima umenewo.

Jemima anasiya kumvetsera nyimbo za pop n’kuyamba kumvetsera nkhani za m’magazini zimene bambo ake ankakonda zija. Iye anayambanso kuwafunsa mafunso osiyanasiyana. Tsiku lina bambo akewo ali pamakwerero, Jemima anawauza kuti: “Paja ndinanena kuti ndikadzafuna kuphunzira ndidzakuuzani eti? Panopa ndikufuna.”

Domingo anasangalala kwambiri kumva zimenezi. Mu January 2013, anayamba kuphunzira kawiri pa mlungu. Domingo ndi mkazi wake anapita kusukulu ija mu April koma ankaphunzirabe ndi mtsikanayo kudzera pa sikayipi. Jemima anapita kumwambo womaliza maphunziro ndipo anasangalala kwambiri. Iye anabatizidwa pa December 14, 2013.

Jemima anati: “Yehova waleza nane mtima kwambiri. Ndikudziwa kuti sadzandisiya. Panopa ndili ndi anzanga  abwino omwe sindikanawapeza m’dzikoli. Ndikaganizira za abale anga padziko lonse ndimaona kuti Yehova amatikonda kwambiri.”

Anasonyeza Ulemu

Ku Russia kuli m’bale wina dzina lake Vasilii amene akutumikira ku Beteli. Pa March 30, 2014, m’baleyu ankalalikira pafupi ndi Beteli pogwiritsa ntchito tebulo lamatayala. Kenako apolisi anamupeza ndipo anamuuza kuti asiye kulalikira chifukwa anthu a m’deralo ankadandaula. Pa nthawiyi wapolisi wina ankajambula zimene zinkachitika. M’bale Vasilli anaganiza zoti asalimbane nawo. Anthu odutsa ankaima kuti aone zimene zinkachitika koma m’baleyu anangochokapo. Patapita masiku awiri, anapempha zoti akakumane ndi mkulu wa apolisi ndipo analoledwa. Pa nthawi yomwe ankakambirana, M’bale Vasillii anathokoza apolisiwo chifukwa cha ntchito yawo yabwino. Anawathokozanso chifukwa chomuletsa mwaulemu kuti asiye kulalikira. Kenako mkulu wa apolisiwo anauza wachiwiri wake kuti: “Pa zaka 32 zimene ndakhala ndikugwira ntchitoyi, palibe munthu aliyense amene anatiyamikirapo.” Kenako, M’bale Vasillii anafotokoza bwino kuti ntchito ya Mboni za Yehova ndi yovomerezeka ndi malamulo a m’dzikolo. Ndiyeno mkulu wa apolisiwo anafunsa kuti: “Ngati mukudziwa kuti malamulo amakulolani kulalikira, n’chifukwa chiyani simunachite makani pamene amakuletsani?” M’bale Vasillii anayankha kuti: “Ndimalemekeza kwambiri apolisi. Ndikudziwa kuti zikanakhala zinthu zopanda ulemu ndikanayamba kukangana nawo pagulu n’kumanena kuti sadziwa malamulo.” Mkulu wa apolisiwo ndiponso wachiwiri wake anasangalala kwambiri. Kenako anatsimikizira m’baleyo kuti sipadzakhalanso vuto lililonse akamalalikira m’deralo.