Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Ku Asia ndi ku Middle East

Ku Asia ndi ku Middle East
  • MAYIKO 48

  • KULI ANTHU 4,315,759,010

  • OFALITSA 703,271

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 732,106

Anafunsa Ngati Angabwere ndi Anthu Ena

Ku Indonesia m’bale wina anapereka kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa munthu wina woyang’anira malo oimika magalimoto. Anachita izi kutangotsala masiku awiri kuti mwambowu uchitike. Munthuyo anali Msilamu ndipo anafunsa ngati angabwere ndi anthu ena. M’baleyo anamuuza kuti  palibe vuto. Munthuyo anapempha kuti amupatse timapepala tina chifukwa choti ali ndi banja lalikulu. M’baleyo anamupatsa timapepala tina 20 ndipo anamuuza kuti mwambowo ndi wokumbukira imfa ya Yesu. Ananena kuti aliyense akhoza kupezekapo kaya Mkhristu kapena Msilamu. Munthuyo ananena kuti adzafika ndi anthu 60 kapena 70.

Nkhani ya Chikumbutso itangoyamba, munthu uja anatulukira limodzi ndi anthu ena 100. Pa nthawiyo n’kuti muhotelo imene ankachitira mwambowu muli kale anthu 248. Munthuyo anabwera ndi amuna, akazi, ana ndiponso mzimayi woyembekezera wotopa. Anthuwo anachita hayala magalimoto popita kumwambowu. Mlonda wa pahoteloyo atangowaona sanafune kuti alowe. Ankaona kuti sizingatheke kuti Asilamu afike pa mwambo wachikhristu. Zitatero anthuwo anasonyeza timapepala towaitanira kumwambowo ndipo mlondayo anawaperekeza. Malo amene anapezeka mkatimo anali a anthu 60 okha.

Patapita masiku ochepa, m’baleyo anakaonana ndi munthu uja n’kumufunsa ngati anzakewo anasangalala ndi mwambowo. Munthuyo ananena kuti: ‘Kunena zoona anthu aja ankachita manyazi koma anasangalala poona kuti alandiridwa bwino ndiponso apatsidwa moni pambuyo pa mwambowo.’ Kenako m’baleyo anaitananso munthuyo kuti adzamvere nkhani yapadera Lamlungu lotsatira. Lamlungulo, anafika ndi anthu 40 ndipo ena anali achibale ake pomwe ena anali anzake. Anthuwa anafika nkhani ili  chakumapeto choncho akulu anakonza zoti ikambidwenso. M’bale amene anali tcheyamani anatchula mutu wa nkhaniyo n’kufotokoza mfundo zina zokhudza pulogalamu ya tsikulo. Anaimbanso nyimbo ndi kupereka pemphero. Pofuna kuthandiza asilamuwo, wokamba nkhani sankanena kuti Baibulo koma ankangoti “Buku Loyera.” M’malo monena kuti Yesu ankati “Mneneri Isa.”

Tsiku lina mkulu wina anapita kunyumba kwa munthu uja ndipo anayamba kuphunzira naye Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mverani Mulungu. Anthu ena 12 anabwera kudzaphunzira nawo ndipo pagululo panali akazi achisilamu ndiponso ana.

Ankaika Mabuku M’basi

Mongolia: Madalaivala analoleza kuti abale aike mabuku m’mabasi

Mabasi ochoka mumzinda wa Ulaanbaatar amazungulira m’madera onse a dziko la Mongolia. Ulendowu umatenga maola 48. Chifukwa cha kutopa ndi ulendo wautaliwu, anthu amakonda kumangoyang’ana pawindo kapena kugona. M’mabasiwa simuikidwa chinthu chilichonse choti anthu aziwerenga ngakhale kuti anthu a m’dzikolo amakonda kuwerenga. Ndiyeno abale ena a mumpingo winawake anaganiza zokacheza ndi madalaivala a mabasiwo ndipo anena kuti: “Tikufuna kukupatsani mphatso ya buku linalake labwino kwambiri. Timaona kuti m’ndege mumaikidwa mabuku oti anthu aziwerenga. Kodi mungakonde kuti tikupatseni mabuku oti anthu okwera mabasi anu aziwerenga?” Madalaivala 8 anavomera ndipo anapereka  magazini 299 ndi timabuku 144. Abalewo anakonzanso kuti nthawi zonse azipereka magazini atsopano kwa madalaivalawo.

Anapita Pashopu Yolakwika

M’dziko lina ku Asia akulu awiri anapemphedwa kuti akayendere mlongo wina amene anasiya kusonkhana kwa zaka 8. Akuluwa anali asanamuonepo ndiye anangomuimbira foni n’kugwirizana kuti akamupeze pashopu yake. Abalewa anadutsa m’misewu yovuta kwambiri mpaka kukafika pashopu ina. Atafika analandiridwa ndi mayi wina amene anali ndi kabaibulo pakauntala. Atamufunsa dzina lake, komwe amakhala, komanso misinkhu ya ana ake anapeza kuti zikugwirizana ndi zimene ankadziwa za mlongoyo. Ndiyeno anamuuza kuti: “Ndife abale anu a Mboni za Yehova.”

Mayiyo anadabwa kwambiri kenako n’kuyankha kuti “Inetu ndi Mkhristu.” Zimene anachitazi zinadabwitsanso abalewo koma anamupatsa mabuku ena ndipo mayiyo anayamikira kwambiri. Pochoka pamalowo abalewa anazindikira kuti anapita pashopu yolakwika. Anauzidwa kuti apite kushopu nambala 2202 koma anapita kushopu nambala 2200. M’bale wina anati: “Titangofika pamene paja mtima wanga unangondiuza kuti pita apo. Ndikuganiza kuti mngelo ankandikokera kwa mayi amene uja. Ndiye zinangochitika kuti afanana ndi mlongoyo mayina, kumene  amachokera komanso misinkhu ya ana awo. Akanasiyana mayina kapena kochokera tikanadziwa kuti si ameneyo.” Ndiyeno atadutsa mashopu awiri, anapeza mlongoyo akuwadikira.

“Ndikuyamikira kwambiri kuti Yehova sanandiiwale ngakhale kuti ndakhala nthawi yaitali kwambiri ndisakumutumikira”

Koma kupita kushopu yolakwika kunathandiza kuti mayi uja ayambe kuphunzira ndiponso kusonkhana. Mlongo amene anafooka uja anayambanso kupezeka pa misonkhano yonse ndiponso kulalikira mwakhama. Mlongoyo anati: “Ndikuyamikira kwambiri kuti Yehova sanandiiwale ngakhale kuti ndakhala nthawi yaitali kwambiri ndisakumutumikira.”

Ankangotumiza Mameseji

Philippines: Greg akutumiza mameseji

Greg ndi Alma anasamukira kuchilumba china m’dziko la Philippines kumene kunkafunika ofalitsa ambiri. Kuchilumbachi kuli mapiri ambiri ndipo kuyenda kumakhala kovuta. Nthawi zambiri Greg ndi Alma amayenda mtunda wa makilomita 19 kuti akafike kudera lomwe akufuna. Masiku ena ankayenda paboti kwa maola awiri. Koma nthawi zambiri amavutika kuyenda ngati kuli mvula. M’malo moti angokhala, iwo amayesetsa kutumiza mameseji kwa anthu chifukwa makampani ambiri a mafoni amapereka mwayi woti anthu azitumizirana mameseji pamtengo wotsika.

Poyamba Greg amalemba dzina lake kenako mawu oti: “Ndikufuna kuti tikambirane uthenga wa m’Baibulo.” Akatero amaika lemba la Yohane 17:3. Kenako amafunsa kuti: Kodi Mulungu woona ndi ndani? Nanga Yesu Khristu ndi ndani? Munthuyo akayankha Greg amamutumizira lemba lina ngati la Salimo 83:18. Ngati munthuyo akuyankhabe, Greg amafunsa ngati n’zotheka kulankhulana pafoni. Greg ndi Alma ananena kuti anthu ambiri amavomera.

 Iwo ananenanso kuti nthawi ina ankatumizirana mameseji ndi mayi wina yemwe ankafunsa mafunso ambirimbiri. Zimenezi zinachititsa kuti ayambe kuphunzira naye Baibulo. Kenako mayiyo anayamba kuuza m’bale wake ndiponso mayi wina wakuntchito zimene ankaphunzira. Pamapeto pake anthu onse atatu anabatizidwa.