Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

North ndi South America

North ndi South America
  • MAYIKO 57

  • KULI ANTHU 980,780,095

  • OFALITSA 4,034,693

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 4,339,285

Ana Amasiye Anafika ku Misonkhano

Angela amakhala ku Suriname ndipo tsiku lina anakalalikira pamalo osungirako ana amasiye omwe ali pafupi ndi kumene amakhala. Mwini wake wa malowo ndi mlongo wofooka ndipo anavomera kuti Angela alalikire anawo. Angela analalikira ana onse 85 ndipo anawaonetsa mavidiyo a pa jw.org. Zimenezi zinachititsa kuti aziphunzira  Baibulo ndi ana ambiri. Kenako alongo awiri omwe ndi apainiya ankaphunziranso ndi anawo ndipo aliyense anali ndi kagulu kake. Mlongo wofookayo ananenanso kuti ankawaphunzitsa nyimbo za Ufumu ndipo usiku ankawawerengera nkhani za m’Baibulo. Iye ankafunitsitsa kupita kumisonkhano koma sankafuna kuwasiya okha anawo. Ndiye anakonza zoti ana onse 85 apite nawo ku Nyumba ya Ufumu. Popeza malo osungira ana amasiyewo sanali patali, abale anapita n’kukathandiza mlongoyu poyenda ndi anawo kuti afike ku Nyumba ya Ufumu. Panopa mlongo amene anafookayo amafika pamisonkhano nthawi zonse limodzi ndi ana 85.

Gabriel Anathandiza Agogo Ake

Paraguay: Gabriel akulankhulana ndi agogo ake

Ku Paraguay kuli mnyamata wa zaka 6 dzina lake Gabriel. Tsiku lina akuchokera kumsonkhano wachigawo ankaganizira kufunika kwa ntchito yolalikira. Kenako iye anakumbukira kuti agogo ake ndi ofunika kwambiri kudzakhala nawo m’Paradaiso. Koma agogo akewo sankafuna kuphunzira Baibulo ndipo ankatsutsa akazi awo ndiponso ana awo chifukwa choti anali a Mboni.

Tsiku lomweli, Gabriel anapempha makolo ake kuti alankhule ndi agogo ake ku Argentina pa sikayipi. Ndiyeno Gabriel anafotokozera agogo akewo kufunika kophunzira Baibulo. Iye anawafunsa kuti: “Kodi agogo n’zotheka kuti ndiziphunzira nanu Baibulo?” Agogowo atavomera, Gabriel anakonza zoti aziphunzira nawo kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. Gabriel anaphunzira ndi agogo akewo  kwa miyezi ingapo. Popeza onse ankavutika kuwerenga, ankakonzekera ndiponso kuyeseza. Nthawi zonse Gabriel ankavala shati ndi tayi pophunzira ndi agogo akewo.

Agogowo anakonza zoti akaone Gabriel ndiponso makolo ake. Iwo atafika, ankapita nawo kumisonkhano. Atabwerera ku Argentina, iwo anapitiriza kuphunzira Baibulo ndi m’bale wina ndipo panopa agogowo ndi wofalitsa wosabatizidwa. Iwo amapemphera pamodzi ndi akazi awo tsiku lililonse. Nayenso Gabriel akulimbikira ndipo panopa ndi wofalitsa wosabatizidwa. Agogowo akufunitsitsa kubatizidwa kuti azitumikira Yehova.

Ndi Mulungu Amene Anakutumizani

Mlongo wina dzina lake Jennifer amakhala ku Brazil. Tsiku lina akugawira kapepala kakuti Kodi N’zoonadi Kuti Akufa Adzauka?, anafika panyumba ina ndipo anapeza mayi amene ankapita kumaliro a mnzake. Jennifer  ananena kuti zangochitika mwamwayi kuti wafika kuti amupatse kapepala kofotokoza zoti akufa adzauka. Mayiyo anadabwa ndi mutu wa kapepalako ndipo analandira. Kenako anapempha timapepala tina kuti akapatseko anamfedwa ndipo mlongoyo anam’patsa timapepala 9.

Patapita masiku angapo, Jennifer anakonza zopitanso kwa mayiyo. Mayiyo anamuuza kuti: “Ndinazindikira kuti nthawi ija sikuti tinangokumana mwamwayi ayi. Koma ndi Mulungu amene anakutumizani kuti mudzanditonthoze.” Mayi uja atafika kumaliro anagawira timapepala 9 timene anapatsidwa tija. Ndipo bambo wina amene ankalalikira anawerenga kapepala konse mokweza. Aliyense pamaliropo anathokoza kwambiri mayi uja chifukwa chobweretsa uthenga wotonthoza. Mayiyu anavomera kuti aziphunzira Baibulo ndi Jennifer.

Ulaliki wa M’minibasi

Abale atatu a pa Beteli ku Haiti anali pa ulendo wa maola awiri ndi hafu. Ankakwera maminibasi otchedwa tap-tap ndipo ankalalikira kwa anthu amene ankakwera nawo. Iwo anagawira magazini 50 ndi timapepala 30. M’bale wina dzina lake Gurvitch anawerengera munthu wina kankhani ka mu Galamukani! Mnyamata wina dzina lake Pépé atamva anayamba kukambirana ndi m’baleyu. Iye anapempha kuti aziphunzira Baibulo ndipo zinangochitika kuti ankakhala m’gawo la mpingo wa Gurvitch. Izi zinachitika mu January 2014 ndipo kuyambira nthawi imeneyo, Pépé wakhala akupezeka pafupifupi pa misonkhano yonse yampingo ndi yadera. Iye amauza anzake zimene akuphunzira ndipo akuganiza kuti posachedwa akhala wofalitsa wosabatizidwa.