Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Africa

Africa
  • MAYIKO 58

  • KULI ANTHU 994,839,242

  • OFALITSA 1,421,375

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 3,516,524

Ana Ankatsatira Aphunzitsi Awo

José amakhala mumzinda wa Luanda ku Angola. Iye ndi mpainiya ndipo amaphunzitsa pasukulu yapafupi ndi Nyumba ya Ufumu. Iye ndi wamakhalidwe abwino ndiponso ndi waluso pa ntchito. Choncho ana ake asukulu okwana 86 amamukonda kwambiri. Iye amachita misonkhano mkati mwa mlungu nthawi ya 4:00 madzulo. Akuluakulu a pasukuluyo  anamuloleza kuti aziweruka mofulumira pa tsiku lamisonkhano. Akaweruka amapita ku Nyumba ya Ufumu osadzera kunyumba kwawo.

Ana ena a pasukuluyo ankadabwa chifukwa chimene José ankawerukira mofulumira ndiponso kumene ankapita. Tsiku lina ana awiri anamutsatira ndipo anakasonkhana nawo. Tsiku linanso José anali ndi nkhani mumsonkhano wa utumiki ndipo ana aja anabwera ndi enanso atatu. Ana ena a m’kalasi yake anamva zimenezi ndipo m’masabata otsatira, chiwerengero cha ana amene ankatsatira José chinafika pa 21. Abale ndi alongo anapempha anawo kuti aziphunzira nawo Baibulo ndipo ambiri anavomera. Anawo ankatenga mabuku athu popita kusukulu ndipo zimenezi zinachititsa kuti anzawo ayambe kumafikanso kumisonkhano. Pofika nthawi yotsekera, ana 54 pa ana 86 omwe José ankawaphunzitsa anafika pamisonkhano. José anafotokoza kuti ana 23 akufikabe pamisonkhano ndipo akutsatira zimene akuphunzirazo.

Gawo Lathu Ndi Lochepa

Nigeria: Joseph ndi Evezi akugwiritsa ntchito DVD puleya mu utumiki

Joseph ndi Evezi ndi apainiya apadera ku Nigeria. Iwo atafika kugawo lawo latsopano, abale a kumeneko anali okhumudwa ndipo anati: “Gawo lathu ndi lochepa kuno ndipo anthu ake timawalalikira mobwerezabwereza.” Patatha chaka, Joseph analemba kalata ku ofesi ya nthambi ndipo anati: “Timalalikira tsiku ndi tsiku m’dera la anthu osafuna kuphunzira koma zikuyenda ndithu. Timatenga ka DVD puleya  n’kumaonetsa anthu osiyanasiyana mavidiyo. Panopa mwezi uliwonse ine ndi mkazi wanga timachititsa maphunziro 18 ndipo nthawi zina timalephera kuyendera onse. Ana ambiri amatipempha kuti tiwaonetse vidiyo ya Kalebe.”

Anthu Apachilumba Anapempha Kuti Aziphunzitsidwa

Congo (Kinshasa): Akulalikira msodzi

Mu April 2014, ofesi ya nthambi ya ku Congo (Kinshasa) inalandira kalata yochokera kwa asodzi a pachilumba  cha Ibinja panyanja ya Kivu. Asodziwa amapitapita m’mizinda ina kukachita malonda. Ndiyeno ulendo wina atapita kumzinda wa Bukavu anakumana ndi a Mboni za Yehova omwe anawalalikira ndiponso kuwapatsa Baibulo ndi mabuku.

Asodziwo anayamikira kwambiri ndipo anakauza anzawo zimene anaphunzira. Enanso anasangalala nazo moti anatuma munthu kuti apite ku Bukavu kukafufuza a Mboni kuti abwere kuchilumbacho koma sanawapeze. Ndiyeno analemba kalata ku ofesi ya nthambi yonena kuti: “Kodi mungatitumizire a Mboni kuti adzatiphunzitse? Tikufuna kuti nafenso tidziwe Baibulo komanso zimene tingachite kuti tipeze moyo wosatha. Tiwasungira nyumba komanso ineyo ndipereka malo oti amangepo tchalitchi. Mabuku anu atithandiza kuzindikira kuti abusa ndi ansembe amangotinamiza. Tapeza chipembedzo chenicheni tsopano. Kuno ku Ibinja kuli anthu ambiri amene akufuna kuphunzira Baibulo n’kukhala a Mboni za Yehova.”

Pachilumbachi pali anthu oposa 18,000 koma kulibe wa Mboni aliyense. Kalata imene analembayo inasonyeza kuti kuli anthu 40 ofuna kuphunzira. Nthawi yomweyo ofesi ya nthambi inatumiza apainiya apadera awiri amene ankadziwa chilankhulo cha pachilumbacho.

Wansembe Wayamba Kuphunzira

Pambuyo pochita nawo chikumbutso, wansembe wa tchalitchi china ku South Africa ananena kuti: “Sindidzalola kuphonya mwambo wachikumbutso uliwonse.” Kodi n’chiyani chinachititsa wansembeyu kukachita nawo chikumbutso mu April 2014? Abale awiri  amitundu yosiyana ankalalikira ndipo anafika panyumba ya wansembeyo. Abalewa ankadziwa kuti iye sankafuna kulankhula ndi a Mboni. Mmodzi wa abalewo anali Adaine ndipo ananena kuti: “Tinadabwa kuona wansembeyo akutiuza kuti tilowe. Tinakambirana naye kwa nthawi yaitali. Iye anadabwa kuona mzungu akulalikira m’dera la anthu akuda ndiponso akumulalikira m’chilankhulo chake. Abalewo anayamba kuphunzira Baibulo ndi wansembeyo.”

Adaine ananenanso kuti: “Wansembeyo anali mmishonale kwa zaka zoposa 40. Koma mayankho amafunso ake wawapeza ali ndi zaka 80. Iye amakonda kwambiri buku lakuti Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo. Tikamaphunzira naye, amaloweza mfundo zina kuti azikalalikira m’tchalitchi chawo. Tsiku lina anaonetsa anthu a kutchalitchi chake buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’kuwauza kuti: ‘A Mboni za Yehova akafika ndi buku ili kunyumba kwanu muziwalandira, chifukwa muli chuma mmenemu.’”

Tsiku lina wansembeyo anafunsa nzeru kwa Adaine. Iye ananena kuti akuluakulu atchalitchi chake anamukalipira n’kumuuza kuti asadzanenenso zokhudza Mboni za Yehova kutchalitchiko. Adaine anakumbukira nkhani ina yake m’Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2013. Nkhaniyo inali yokhudza wansembe wina ku Myanmar. Adaine anamuwerengera nkhaniyo ndipo wansembeyo anati: “Nkhaniyi ikunena za ineyo. Ndifunika ndidziwe zochita pompano.”

 Pa April 14, 2014, wansembeyo anafika pachikumbutso ndipo anati sadzalola kuphonya mwambo wachikumbutso uliwonse. Iye watsimikiza zosiyiratu kuchita zinthu zokhudza chipembedzo chonyenga.

Kufufuza Anthu M’minda ya Koko

Ghana: Baffour ndi Aaron akulalikira m’munda wa koko

Kudera lotchedwa Bokabo m’dziko la Ghana kumalimidwa koko wambiri. Baffour ndi Aaron ndi apainiya apadera kuderali. Kuti munthu afike kuderali amayenda wapansi m’tinjira todutsa m’minda ya koko ndipo m’posavuta kusochera. Nyumba zake ndi zing’onozing’ono za apa ndi apo. Tsiku lina apainiyawo anasochera n’kufika kunyumba zina kumene anakapeza Michael ndi Patience. Anthuwa anavomera kuphunzira Baibulo ndipo Michael anati: “Ifetu tinasiya kupita kutchalitchi zaka ziwiri zapitazo. Tinaona kuti zimene ankatiphunzitsa n’zosiyana ndi zimene Baibulo limanena. Titasiya, tinayamba kuphunzira Baibulo patokha kuti tipeze mayankho a mafunso amene tinali nawo. Tinkapemphera kwa Mulungu kuti atithandize kudziwa zoona.” Anthu awiriwa anayamba kupezeka pamisonkhano ngakhale kuti ankayenera kuyenda mtunda wautali m’minda ya koko. Chaka chisanathe, onsewa anabatizidwa n’kuyamba upainiya wokhazikika. Panopa nawonso amafufuza anthu m’minda ya koko. Iwo akufuna kuti apezenso anthu amene “akhala akupempha Mulungu kuti awathandize kudziwa uthenga wabwino.”

Michael ndi Patience akudutsa m’munda wa koko