Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira

Okondedwa Abale ndi Alongo:

Mawu a pa 1 Atesalonika 1:2, 3 amafotokoza bwino mmene timamvera tikaganizira za inu. Lembali limati: “Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamatchula za inu nonse m’mapemphero athu. Timatero pakuti timakumbukira nthawi zonse ntchito zanu zachikhulupiriro, ndi ntchito zanu zachikondi. Timateronso pokumbukira mmene munapiririra chifukwa cha chiyembekezo chanu mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate.” Kunena zoona timayamikira Yehova chifukwa cha ntchito yabwino imene mukugwira. Pali zifukwa zingapo zimene tikunenera zimenezi.

Chaka chapitachi mwakhala mukugwira ntchito mwakhama ndipo ambirinu mwawonjezera utumiki wanu m’njira zosiyanasiyana. Ena apita kumadera kapena kumayiko kumene kulibe ofalitsa ambiri. Ena ayamba kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri. Enanso anachita upainiya wothandiza pa nyengo ya chikumbutso, pa mlungu wapadera komanso pa nthawi yogawira kapepala mu August 2014. Tikuthokoza kwambiri chifukwa choti mukuyesetsa kutumikira Yehova “ndi moyo wanu wonse” ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto osiyanasiyana.—Akol. 3:23, 24.

 Timayamikiranso chifukwa choti mumathandiza pa ntchito zomangamanga zimene zikuchitika padziko lonse. Panopa anthu akuwonjezekabe m’gulu la Yehova choncho tikufunika kumanga malo ambiri osonkhanira. (Yes. 60:22) Chaka chathachi, chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa chinali 8,201,545, ndipo chiwerengero chapamwamba cha maphunziro a Baibulo chinali 9,499,933. Chifukwa cha zimenezi, tiyenera kuwonjezera nyumba zambiri m’maofesi a nthambi. Nyumba za Ufumu zambiri zikufunikanso. Pakufunikanso maofesi a omasulira mabuku n’cholinga choti ntchitoyi izigwiridwa m’madera amene chilankhulo chawocho chimalankhulidwa.

Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndingathandize bwanji pa ntchito ya zomangamangayi?’ Enafe tikhoza kukwanitsa kugwira nawo ntchitoyi. Kaya tili ndi luso pa ntchitoyi kapena ayi tikhoza kupereka zinthu zina zamtengo wapatali kuti zithandize. (Miy. 3:9, 10) Pamene chihema chinkamangidwa, Aisiraeli anapereka zinthu zambiri mpaka panaperekedwa chilengezo choti asiye kupereka. (Eks. 36:5-7) Zitsanzo ngati zimenezi zimatilimbikitsa kwambiri. Timayamikiranso Yehova chifukwa cha zinthu zamtengo wapatali zimene mumapereka pa ntchitoyi.

Timasangalalanso tikaona abale athu akukhalabe okhulupirika pokumana ndi mavuto. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi abale a ku South Korea. Kuyambira m’ma 1950, abale achinyamata m’dzikoli akhala akumangidwa chifukwa chokana usilikali. Kwa zaka zambiri abale athu akhala akupirira mavutowa ndipo  sasiya kutumikira Yehova. Zimene amachitazi zimatilimbikitsa kwambiri.

Abale atatu a ku Eritrea akhala m’ndende kwa zaka zoposa 20. Ndiye pali abale enanso ndi alongo amene amangidwa kwa nthawi yocheperapo. Takhala tikuyesetsa kuti abalewa amasulidwe koma sizikutheka. Koma chosangalatsa n’chakuti abalewo adakali okhulupirika ngakhale kuti amakumana ndi mavuto oopsa. Timapemphererabe abale athuwa.—Aroma 1:8, 9.

Akhristu ambirinu simunamangidwe chifukwa cha chikhulupiriro chanu. Koma mumakumana ndi mavuto monga ukalamba, matenda aakulu, kutsutsidwa ndi amuna kapena akazi anu komanso ndi achibale. Enanu mukukumana ndi mavuto amene mumawadziwa nokha. Ngakhale zili choncho mumatumikirabe Yehova mokhulupirika. (Yak. 1:12) Timayamikiranso Yehova chifukwa cha kukhulupirika kwanu ngakhale kuti mukukumana ndi mavutowa.

Khama lanu, kukhulupirika kwanu komanso chikondi chanu zimatichititsa ‘kuyamika Yehova chifukwa iye ndi wabwino.’ (Sal. 106:1) Timakukondani nonsenu ndipo timapempha Yehova kuti akupatseni mphamvu, akusamalireni ndiponso akudalitseni n’cholinga choti mumutumikire mpaka kalekale.

Ndife abale anu.

Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova