Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Chigawo 8: Zimene Baibulo Limaneneratu Zimakwaniritsidwa

Chigawo 8: Zimene Baibulo Limaneneratu Zimakwaniritsidwa

Baibulo silimangopereka kokha nkhani yeni-yeni ya zimene zinachitika kale koma’nso limasimba zimene zidzachitika m’tsogolo. Anthu sangathe kuneneratu za m’tsogolo. Ndicho chifukwa chake tikudziwa kuti Baibulo n’lochokera kwa Mulungu. Kodi Baibulo limanenanji ponena za m’tsogolo?

Iro limasimba za nkhondo yaikulu ya Mulungu. M’nkhondo imene’yi Mulungu adzachotsera dziko lapansi kuipa konse ndi anthu oipa, koma iye adzatetezera awo amene amam’tumikira. Mfumu ya Mulungu, Yesu Kristu, idzatsimikizira kuti atumiki a Mulungu akusangalala ndi mtendere ndi chimwemwe, ndi kuti iwo sadzadwala’nso kapena kufa.

Tingathe kukhala achimwemwe kuti Mulungu adzapanga paradaiso watsopano pa dziko lapansi, kodi si choncho? Koma tiyenera kuchita kanthu kena ngati titi tikhale ndi moyo m’paradaiso amene’yu. M’nkhani yotsirizira ya bukhu’li tikuphunziramo zimene tiyenera kuchita kuti tisangalale ndi zinthu zodabwitsa zimene Mulungu wasungira awo amene amam’tumikira. Chotero werengani CHIGAWO 8 ndi kuona zimene Baibulo limaneneratu kaamba ka m’tsogolo.

Mmene paradaiso adzakhalire