O!O! KODI n’chiani chimene chikuchitika pano? Kodi mnyamata wagona kwala’yo wabvulala kwambiri? Taonani! mmodzi wa amuna amene akutuluka m’nyumba’wo ndiye Paulo! Kodi mukuonapo Timoteo? Kodi mnyamata’yo anagwa kutulukira pa zenerapo?

Paulo akupita kukaukitsa Utiko

Inde, n’zimene zinachitika’di. Paulo anali kukamba nkhani kwa ophunzira muno m’Trowa. Iye anadziwa kuti sakawaona’nso kwa nthawi yaitali chifukwa chakuti anayenera kunyamuka ulendo wa pa bwato m’mawa mwake. Chotero anali kumangokamba mpaka pakati pa usiku.

Eya, mnyamata wochedwa Utiko’yu anali atakhala pa zenera, ndipo anagona tulo. Iye anapikuka, nagwa kutulukira pa zenera’lo, kuchokera pa chipinda chosanja chachitatu kukagwera pansi! Chotero mungaone chifukwa chake anthu’wo akuonekera kukhala odera nkhawa kwambiri. Pamene amuna’wo akunyamula mnyamata’yo, kuli monga momwe iwo anaopera. Iye wafa!

Paulo poona kuti wafa, akum’tsamira nam’kupatira. Ndiyeno akuti: ‘Musadere nkhawa. Ali bwino!’ Ndipo iye ali bwino’di! N’chozizwitsa! Paulo wam’khalitsa’nso moyo! Khamu lonse’lo likusangalala.

Iwo onse akubwerera m’chipinda chapamwamba’cho nadya chakudya. Paulo akupitirizabe kukamba mpaka kucha mbee. Koma mosakaikira Utiko sanagone’nso! Ndiyeno Paulo, Timoteo ndi awo oyenda nawo akukwera bwato. Kodi mukudziwa kumene akupita?

Paulo akungomaliza ulendo wake wachitatu womka nalalikira, ndipo ali pa ulendo wobwerera kwao. Pa ulendo’wu Paulo anakhala zaka zitatu mu mzinda wa Efeso wokha. Chotero uno ndi ulendo wotalikirapo koposa wachiwiri uja.

Atachoka ku Trowa, bwato’lo likuima pa Mileto kwa kanthawi. Pakuti Efeso ali pa mtunda wa mamailo owerengeka, Paulo akuitana akulu a mpingo kudza ku Mileto kuti akalankhule nawo kotsiriza. Pambuyo pake, itakwana nthawi yakuti bwato’lo linyamuke, ndi achisoni chotani nanga m’mene iwo aliri kuona Paulo akupita!

Potsirizira pake bwato’lo likufika’nso ku Kaisareya. Paulo ali kuno pa nyumba ya wophunzira Filipo, mneneri Agabu akuchenjeza Paulo. Iye akuti Paulo adzaikidwa m’ndende akadza ku Yerusalemu. Ndipo ndithudi, izi ndizo zinachitika. Ndiyeno, atakhala m’ndende kwa zaka ziwiri mu Kaisareya, Paulo akutumizidwa ku Roma kukaweruzidwa pamaso pa wolamulira Wachiroma Kaisara. Tiyeni tione zimene zikuchitika pa ulendo womka ku Roma.

Machitidwe chaputala 19 mpaka 26.Mafunso

  • Pachithunzipa, kodi mnyamata amene wagona pansiyo ndi ndani, ndipo n’chiyani chinamuchitikira?
  • Kodi Paulo akuchita chiyani ataona kuti mnyamatayo wafa?
  • Kodi Paulo, Timoteo, ndi anthu amene akuyenda nawo akupita kuti, ndipo n’chiyani chikuchitika ataima ku Mileto?
  • Kodi mneneri Agabu akuchenjeza Paulo za chiyani, ndipo kodi zinachitika bwanji ndendende monga mmene ananenera mneneriyo?

Mafunso ena