MWAMUNA wagwada apa’yu ndi Stefano. Iye ndi wophunzira wokhulupirika wa Yesu. Koma taonani zimene zikum’chitikira! Anthu’wa akum’ponyera zimiyala. Kodi iwo akuderanji Stefano kwambiri kuti iwo akuchita chinthu choopsya’chi? Tiyeni tione.

Sitefano akuponyedwa miyala

Mulungu wakhala akuthandiza Stefano kuchita zozizwitsa zodabwitsa. Amuna’wa samakonda izi, ndipo chotero akukangana naye ponena za kuphunzitsa kwake anthu choonadi. Koma Mulungu akum’patsa nzeru yaikulu, ndipo Stefano akusonyeza kuti amuna’wa akhala akuphunzitsa zinthu zonyenga. Izi zikuwapsyetsa mtima kwambiri’di. Chotero akum’gwira, naitana anthu kudzam’nenera zonama.

Mkulu wa ansembe akum’funsa kuti: ‘Kodi izi n’zoona?’ Stefano akuyankha mwa kukamba nkhani yabwino kwambiri yochokera m’Baibulo. Pakutha kwake, iye akusimba m’mene anthu oipa anadera aneneri a Yehova kale. Ndiyeno akuti: ‘Inu muli ngati anthu amene’wo. Munapha mtumiki wa Mulungu Yesu, ndipo simunamvera malamulo a Mulungu.’

Izi zikupsyetsa mtima kwambiri atsogoleri achipembezo’wo! Iwo akum’kukutira mano ao mwaukali. Komano Stefano akutukula mutu wake, nati: ‘Taonani! Ndikuona Yesu ataima ku dzanja lamanja la Mulungu kumwamba.’ Pa izi, amuna’wa akutseka makutu ao ndi manja natukutira Stefano. Akum’gwira nam’kwakwazira kunja kwa mzinda.

Kunoko iwo akubvula malaya ao nawapatsa mnyamata’yo Saulo kuwasungira. Kodi mukuona Saulo? Ndiyeno ena a anthu’wo akuyamba kuponya miyala Stefano. Stefano akugwada, monga momwe mukuonera, napemphera kwa Mulungu kuti: ‘Yehova, musawalange chifukwa cha choipa’chi. Iye akudziwa kuti ena a iwo anyengedwa ndi atsogoleri achipembedzo. Pambuyo pake Stefano akufa.

Pamene munthu wina achita choipa kwa inu, kodi mumayesa kuwabwezera, kapena kupempha Mulungu kuwabvulaza? Sindizo zimene Stefano kapena Yesu anachita. Iwo anali okoma mtima ngakhale kwa awo amene sanali okoma mtima kwa iwo. Tiyeni tiyese kutsanzira chitsanzo chao.

Machitidwe 6:8-15; 7:1-60.Mafunso

  • Kodi Stefano ndi ndani, ndipo Mulungu wakhala akumuthandiza kuchita chiyani?
  • Kodi Stefano akunena chiyani chimene chikukwiyitsa kwambiri atsogoleri a chipembedzo?
  • Amunawo atamukwakwazira Stefano kunja kwa mzinda, kodi akumuchita chiyani?
  • Pachithunzipa, kodi mnyamata amene waima pafupi ndi zovalayo ndi ndani?
  • Asanafe, kodi Stefano akupemphera kuti chiyani kwa Yehova?
  • Potsanzira Stefano, kodi tiyenera kuchita chiyani munthu wina akatichitira chinthu choipa?

Mafunso ena