POPITA masiku, Yesu akudzisonyeza kwa atsatiri ake nthawi zambiri. Pa nthawi ina ophunzira 500 akumuona. Pamene akuonekera kwa iwo, kodi mukudziwa zimene iye akunena nawo? Ufumu wa Mulungu. Yehova anatumiza Yesu pa dziko lapansi kudzaphunzitsa za Ufumu’wo. Ndipo akupitirizabe kutero ngakhale ataukitsidwa kwa akufa.

Yesu akubwerera kumwamba

Kodi mukukumbukira chimene ufumu wa Mulungu uli? Ufumu’wo ndiwo boma leni-leni la Mulungu kumwamba, ndipo Yesu ndiye amene Mulungu anam’sankha kukhala mfumu. Monga momwe taphunzirira, Yesu anasonyeza m’mene iye aliri mfumu yodabwitsa mwa kudyetsa anjala, kuchiritsa odwala, ndipo ngakhale kuukitsa akufa!

Chotero pamene iye alamulira monga mfumu kumwamba kwa zaka chikwi, kodi dziko lapansi lidzakhala lotani? Iro lonse lidzapangidwa kukhala paradaiso wokongola. Sipadzakhala’nso nkhondo, upandu, matenda, kapena ngakhale imfa. Tikudziwa kuti izi n’zoona chifukwa chakuti Mulungu anapanga dziko lapansi kukhala paradaiso woti anthu asangalale naye. Ndicho chifukwa chake anapanga munda wa Edene poyamba. Ndipo Yesu adzatsimikizira kuti chifuniro cha Mulungu potsirizira pake chikukwaniritsidwa.

Nthawi ikukwana tsopano yoti Yesu abwerere kumwamba. Kwa masiku 40 Yesu wakhala akudzisonyeza kwa ophunzira ake. Chotero iwo ali otsimikizira kuti ali ndi moyo. Koma asanasiyane ndi ophunzira ake akuwauza kuti: ‘Khalanibe m’Yerusalemu kufikira mutalandira mzimu woyera.’ Mzimu’wo ndiwo mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, mofanana ndi mphepo yoomba, imene idzathandiza atsatiri ake kuchita chifuniro cha Mulungu. Kenako, akuti: ‘Muyenera kulalikira za ine mpaka ku malekezero a dziko lapansi.’

Atanena izi, chodabwitsa chikuchitika. Iye akuyamba kukwera kumwamba, monga momwe mukuonera pano. Ndiyeno mitambo ikum’phimba osaoneka, ndipo ophunzira’wo sakuona’nso Yesu. Iye akumka kumwamba, ndipo akuyamba kulamulira atsatiri ake pa dziko kuyambira pamenepo.

Ophunzira a Yesu akuyang’ana kumwamba

1 Akorinto 15:3-8; Chivumbulutso 21:3, 4; Machitidwe 1:1-11.Mafunso

  • Panthaŵi ina, kodi ndi ophunzira angati amene akuona Yesu, ndipo akulankhula nawo za chiyani?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndipo kodi moyo udzakhala wotani Yesu akamadzalamulira monga Mfumu kwa zaka 1,000?
  • Kodi Yesu wakhala akudzisonyeza kwa ophunzira ake kwa masiku angati, koma tsopano ndi nthaŵi yoti achite chiyani?
  • Atangotsala pang’ono kuti asiyane ndi ophunzira ake, kodi Yesu akuwauza kuti achite chiyani?
  • Kodi n’chiyani chikuchitika m’chithunzichi, ndipo kodi n’chiyani chikuphimba Yesu kuti asaoneke?

Mafunso ena