Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 102: Yesu Ali Moyo

Nkhani 102: Yesu Ali Moyo

KODI mukudziwa mkazi ndi amuna awiri’wo? Mkazi’yo ndi Mariya wa Magadala, bwenzi la Yesu. Ndipo amuna obvala zoyera’wo ndiwo angelo. Kachipinda kamene Mariya akuyang’anamo ndiko malo amene mtembo wa Yesu unaikidwamo atafa. Amachedwa manda. Koma tsopano mtembo’wo mulibe! Wautenga ndani? Tiyeni tione.

Angelo akulankhula ndi Mariya Mmagadala

Yesu atafa, ansembe anati kwa Pilato: ‘Yesu akali moyo anati akaukitsidwa pambuyo pa masiku atatu. Chotero lamulani kuti manda’wo alonderedwe. Kuti ophunzira ake asabe mtembo wake ndi kunena kuti iye waukitsidwa kwa akufa! Pilato akuuza ansembe kutumiza asilikali ankhondo kukalondera manda’wo.

M’mawa kwambiri pa tsiku lachitatu pambuyo pa imfa ya Yesu mngelo wa Yehova mwadzidzidzi akudza. Akuchotsa mwala pa manda’wo. Asilikali’wo akuopa kwambiri kwakuti sakutha kuyenda. Kenako, poyang’ana m’mandamo, mtembo’wo mulibe! Ena a asilikali’wo akumka ku mzinda’wo nauza ansembe. Kodi mukudziwa zimene ansembe oipa’wo akuchita? Akupatsa ndalama asilikali’wo kuti adzinama. ‘Muziti ophunzira ake anadza usiku, tiri mtulo, naba mtembo’wo,’ akutero ansembe’wo.

Pa nthawi’yi, akazi ena okonda Yesu akufika pa mandapo. Ndi odabwa chotani m’mene aliri kupeza mulibemo! Mwadzidzidzi angelo awiri obvala zoyera akutulukira. Iwo akufunsa kuti, ‘Mukufuniranji Yesu pano?’ ‘Iye waukitsidwa. Thamangani mukauze ophunzira ake.’ Ha, akazi’wo akuthamanga’di mofulumira! Koma ali pa njira mwamuna wina akuwaimika. Mukudziwa kuti iye ndani? Ndiye Yesu! Iye akuti, ‘Kauzeni ophunzira anga.’

Akazi’wo atauza ophunzira’wo kuti Yesu ali moyo ndipo iwo amuona, ophunzira zikuwabvuta kuzikhulupirira. Petro ndi Yohane akuthamangira kumanda’ko kukadzionera okha, koma m’mandamo muli pululu! Pamene akuchoka Mariya wa Magadala akutsalira m’mbuyo. Ndi pa nthawi’yi pamene akusuzumiramo naonamo angelo awiri.

Kodi mukudziwa chimene chinachitikira mtembo wa Yesu? Mulungu anauchititsa kuzimiririka. Iye sanaukitsire Yesu ku moyo wa thupi lanyama limene anafa nalo lija. Iye anam’patsa thupi latsopano lauzimu, longa la angelo akumwamba. Koma kuti asonyeze ophunzira ake kuti ali moyo, iye akubvala thupi loti n’kuonedwa ndi anthu, monga momwe tidzaphunzirira.

Mateyu 27:62-66; 28:1-15; Luka 24:1-12; Yohane 20:1-12.Mafunso

  • Kodi mkazi ali m’chithunziyu ndi ndani, amuna aŵiriwo ndi ndani, ndipo ali kuti?
  • N’chifukwa chiyani Pilato akuuza ansembe kuti atumize asilikali ankhondo kukalondera manda a Yesu?
  • Kodi mngelo akuchita chiyani mmaŵa kwambiri pa tsiku lachitatu Yesu atafa, koma kodi ansembe akuchita chiyani?
  • N’chifukwa chiyani akazi ena ali odabwa atapita ku manda a Yesu?
  • N’chifukwa chiyani Petro ndi Yohane akuthamangira ku manda a Yesu, ndipo akupeza chiyani?
  • N’chiyani chinachitikira thupi la Yesu, koma kodi akuchita chiyani kuti asonyeze ophunzirawo kuti ali moyo?

Mafunso ena

Onaninso

YESU—NDI NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri

Kodi Yesu akanawatsimikizira bwanji ophunzira ake kuti anali ataukitsidwa?

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Yesu Anaukitsidwa ndi Thupi Lotani?

Baibulo limanena kuti Yesu “anaukitsidwa monga mzimu,” ndiye kodi zinatheka bwanji kuti ophunzira ake amuone?

NSANJA YA OLONDA

Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha

Mfundo 6 za m’Baibulo zomwe zimafotokoza mmene imfa ya munthu mmodzi ingathandizire kuti anthu ambiri adzapeze moyo wosatha.