KANTHAWI kochepa atatha kuchiritsa akhungu opempha-pempha’wo, Yesu akufika ku kamudzi ka pafupi ndi Yerusalemu. Iye akuuza ophunzira ake awiri kuti: ‘Pitani m’mudzi ndipo mudzapeza mwana wa bulu. Mmasuleni namudze naye kwa ine.’

Atadza naye bulu’yo, Yesu akukwerapo. Ndiyeno akukwera kumka ku Yerusalemu wokhala chapafupi’yo. Atafika pafupi ndi mzinda’wo, khamu lalikulu la anthu likudza kudzam’chingamira. Ochuluka a iwo akubvula malaya ao nawayalika mu mseu. Ena akudula makhwantha a kanjedza. Akuwaika mu mseu’wo, napfuula kuti: ‘Mulungu adalitse mfumu imene ikudza m’dzina la Yehova!’

Anthu akuchingamira Yesu

Kale-kale mu Israyeli mafumu atsopano ankakwera pa bulu kulowa m’Yerusalemu kudzisonyeza kwa anthu. Izi ndizo zimene Yesu akuchita. Ndipo amene’wa akusonyeza kuti akufuna kuti Yesu akhale mfumu yao. Koma si anthu onse akum’funa. Tingaone izi mwa zimene zikuchitikira Yesu pamene akumka ku kachisi.

Pa kachisi’po Yesu akuchiritsa anthu amene ali akhungu ndi opunduka. Ana ang’ono poona izi, iwo akutamanda Yesu. Koma izi zikukwiyitsa ansembe, ndipo akuuza Yesu kuti: ‘Ukumva zimene ana’wo akunena?’

‘Inde, ndikumva,’ akuyankha motero Yesu. ‘Kodi simunawerenge m’Baibulo pamene pamati: “Mulungu adzachititsa mkamwa mwa tiana kutulutsa chitamando?”’ Chotero ana’wo akupitirizabe kutamanda mfumu ya Mulungu.

Ife timafuna kukhala ngati ana’wo, kodi si choncho? Anthu ena angayese kutiletsa kulankhula za ufumu wa Mulungu. Koma tidzapitirizabe kuuza ena za zinthu zodabwitsa zimene Yesu adzachitira anthu.

Sinali nthawi yakuti Yesu ayambe kulamulira monga mfumu pamene anali pa dziko lapansi. Kodi nthawi imene’yi idzakwana liti? Ophunzira a Yesu akufuna kudziwa. Tidzawerenga za izi pambuyo pake.

Mateyu 21:1-17; Yohane 12:12-16.Mafunso

  • Yesu atafika ku kamudzi kapafupi ndi Yerusalemu, kodi akuuza ophunzira ake kuchita chiyani?
  • Pachithunzipa, kodi chikuchitika n’chiyani Yesu atayandikira mzinda wa Yerusalemu?
  • Kodi ana aang’ono akuchita chiyani ataona Yesu akuchiza anthu akhungu ndi opunduka?
  • Kodi Yesu akuuza ansembe okwiyawo chiyani?
  • Kodi tingakhale bwanji ngati ana amene akutamanda Yesu?
  • Kodi ophunzira akufuna kudziŵa chiyani?

Mafunso ena