Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 95: Kaphunzitsidwe ka Yesu

Nkhani 95: Kaphunzitsidwe ka Yesu

TSIKU lina Yesu akuuza munthu wina kuti ayenera kukonda mnansi wake. Munthu’yo akufunsa Yesu kuti: ‘Ndani amene ali mnansi wanga?’ Eya, Yesu akudziwa zimene iye akuganiza. Munthu’yo akuganiza kuti anthu a pfuko lake okha ndi chipembedzo ndiwo anansi ake. Chotero tiyeni tione zimene Yesu akunena naye.

Nthawi zina Yesu amaphunzitsa mwa kunena nthano. Ndizo zimene iye akuchita tsopano. Akusimba za nkhani yonena za Myuda ndi Msamariya. Taphunzira kale kuti Ayuda ochuluka samakonda Asamariya. Chabwinotu, nayi nthano ya Yesu:

Tsiku lina Myuda wina anali kuyenda mu mseu wa m’mapiri kumka ku Yeriko. Koma achifwamba anam’lumphira. Iwo anatenga ndalama zake nam’menya mpaka kukomoka.

Pambuyo pake wansembe Wachiyuda anadza mu mseu’wo. Iye anaona munthu womenyedwa’yo. Kodi muganiza anachitanji? Eya, iye anangopambukira ku njira ina napita. Ndiyeno munthu wina wokonda chipembedzo kwambiri anadza. Iye anali Mlevi. Kodi iye anaima? Ai, iye sanaime kuti athandize munthu womenyedwa’yo. Mungaone wansembe ndi Mlevi awo akumka chauko’wo.

Koma onani uyu ali pano ndi munthu womenyedwa’yu. Iye ndi Msamariya. Ndipo iye akuthandiza Myuda. Iye akuika mankhwala pa mabala ake. Kenako, iye akutengera Myuda’yo ku malo amene iye angapume ndi kupeza bwino.

Msamariya wachifundo

Atatha kukamba nthano yake’yo, Yesu akuti kwa munthu’yo: ‘Kodi ndi uti wa atatu’wa uganiza kuti anachita monga mnansi kwa munthu womenyedwa’yo? Kodi anali wansembe’yo, Mlevi kapena Msamariya’yo?’

Munthu’yo akuyankha kuti: ‘Msamariya’yo. Anakomera mtima womenyedwa’yo.’

Yesu akuti: ‘Walondola. Chotero pita ukachitire anthu monga momwe iye anachitira.’

Kodi simukukonda m’mene Yesu akuphunzitsira? Tingaphunzire zinthu zochuluka ngati timvetsera zimene Yesu akunena m’Baibulo, kodi si choncho?

Luka 10:25-37.Mafunso

  • Kodi munthu wina akufunsa Yesu funso lotani, ndipo n’chifukwa chiyani akufunsa zimenezi?
  • Kodi Yesu nthaŵi zina amagwiritsa ntchito chiyani pophunzitsa, ndipo kodi taphunzira kale chiyani za Ayuda ndi Asamariya?
  • Mu nthano imene Yesu akukamba, kodi n’chiyani chikuchitikira Myuda pamene anali kuyenda mu msewu wopita ku Yeriko?
  • Kodi chikuchitika n’chiyani pamene wansembe wachiyuda ndi Mlevi akudutsa mumsewuwo?
  • Pachithunzipa, kodi ndani akuthandiza Myuda amene wavulalayo?
  • Yesu atatha kukamba nthanoyo, kodi akufunsa funso lotani, ndipo munthuyo akuyankha bwanji?

Mafunso ena

Onaninso

YESU—NDI NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni

Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo liti pophunzitsa mfundo yofunika kwambiri?

YESU—NDI NJIRA, CHOONADI NDI MOYO

Mwana Wotayika Anabwerera

Kodi tikuphunzira chiyani m’fanizo la Yesu la mwana wotayika?