TAONANI Yesu pano atakupatira kamnyamata’ko. Mungathe kuona kuti Yesu amasamalira’di tiana. Amuna amene akuonerera’wo ndiwo atumwi ake. Kodi Yesu akunenanji nawo? Tiyeni tione.

Yesu ndi atumwi ake angobwera kumene kuchokera ku ulendo wautali. Ali m’njira atumwi’wo akukangana. Chotero atatha ulendo’wo Yesu akuwafunsa kuti: ‘Kodi munali kukanganira chiani m’njira muja?’ Kweni-kweni, Yesu akudziwa zimene zinali kukanganiridwa. Koma akuwafunsa kuti aone ngati iwo adzamuuza.

Yesu ndi kamnyamata

Atumwi’wo sakuyankha, chifukwa chakuti m’njiramo iwo anali kukanganira kuti wamkulu ndani. Atumwi ena akufuna kukhala ofunika kwambiri koposa ena. Kodi ndi motani m’mene Yesu akuwauzira kuti si koyenera kufuna kukhala wamkulu kopambana onse?

Iye akuitana kamnyamata, nakaimika patsogolo pao. Ndiyeno iye akuuza ophunzira ake kuti: ‘Ndikufuna kuti mudziwe izi motsimikizirika, Ngati simusintha nimukhala ngati ana ang’ono, simudzalowa mu ufumu wa Mulungu. Wamkulu kopambana mu ufumu’wo ndiye munthu amene akhala ngati kamwana’ka.’ Kodi mukudziwa chifukwa chake iye ananena izi?

Eya, tiana sitimadera nkhawa ndi kukhala wamkulu kwambiri kapena kufunika kwambiri koposa ena. Chotero atumwi’wo ayenera kuphunzira kukhala ngati ana m’njira imene’yi ndi kusakanganira kukhala wamkulu kapena wofunika.

Pali nthawi zina’nso, pamene Yesu akusonyeza m’mene iye amasamalirira ana. Miyezi yowerengeka pambuyo pake anthu akudza ndi ana oa kudzaona Yesu. Atumwi akuyesa kuwaletsa. Koma Yesu akuuza atumwi ake kuti: ‘Tiloleni tiana tidze kwa ine, ndipo musatiletse, chifukwa ufumu wa Mulungu uli wa anthu onga iwo.’ Ndiyeno Yesu akuyangata ana’wo nawadalitsa. Kodi si kwabwino kudziwa kuti Yesu amakonda tiana?

Mateyu 18:1-4; 19:13-15; Maliko 9:33-37; 10:13-16.Mafunso

  • Kodi atumwi akukanganirana chiyani pobwerera ku ulendo wawo wautali?
  • N’chifukwa chiyani Yesu akuitana kamnyamata n’kukaimika pakati pa ophunzirawo?
  • Kodi atumwiwo ayenera kuphunzira kukhala ngati ana m’njira yotani?
  • Miyezi ingapo izi zitachitika, kodi Yesu akusonyeza bwanji kuti amakonda ana?

Mafunso ena