Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 92: Yesu Aukitsa Akufa

Nkhani 92: Yesu Aukitsa Akufa

MTSIKANA mukumuona apa’yu ali ndi zaka 12. Yesu wagwira dzanja lake, ndipo mai ndi atate wake aima pafupi naye. Kodi mukudziwa chifukwa chake akuoneka kukhala wachimwemwe? Tiyeni tione.

Yesu akuukitsa mwana wamkazi wa Yairo

Atate wa mtsikana’yo ndi munthu wochuka wochedwa Yairo. Tsiku lina mwana wake wamkazi’yu akudwala, ndipo akugonekedwa pa kama. Koma sakupeza bwino konse. Iye akungodwala moonjezereka-onjezereka. Yairo ndi mkazi wake akudera nkhawa kwambiri, chifukwa kukuonekera kuti buthu lao’lo lidzafa. Iye ndiye mtsikana wao mmodzi yekha. Chotero Yairo akumka kukafuna-funa Yesu. Iye wamva za zozizwitsa zimene Yesu akuchita.

Pamene Yairo akupeza Yesu, pali khamu lalikulu lom’zinga. Koma Yairo akulowa m’khamulo nagwa pa mapazi a Yesu. ‘Mwana wanga wamkazi akudwala kwambiri ndithu,’ akutero. ‘Chonde, bwerani mudzam’chiritse,’ akupempha motero. Yesu akuti ndidzafika.

Pamene iwo akuyenda, khamulo likupitirizabe kukankhana kuti adze pafupi. Yesu akuima mwadzidzidzi. Iye akufunsa kuti, ‘Wandikhudza ndani?’ Yesu anamva mphamvu ikutuluka mwa iye chotero iye akudziwa kuti wina wake wam’khudza. Koma ndani? Ndiye mkazi amene wakhala akudwala kwambiri kwa zaka 12. Iye anadza nakhudza zobvala za Yesu nachiritsidwa!

Izi zikupangitsa Yairo kumva bwino kwambiri, chifukwa angathe kuona m’mene kuliri kosabvuta kwa Yesu kuchiritsa munthu. Komano mthenga ukufika. Ukuuza Yairo kuti, ‘Musabvute’nso Yesu. Buthu lanu’lo langofa kumene.’ Yesu akumvera izi patali nati kwa Yairo: ‘Usadere nkhawa adzapeza bwino.’

Pamene iwo kenako akufika ku nyumba ya Yairo, anthu akulira mwa chisoni chachikulu. Koma Yesu akuti: ‘Tontholani. Mwan’yo sanafe. Ali mtulo chabe.’ Koma iwo akuseka Yesu monyodola, chifukwa chakuti akudziwa kuti iye wafa.

Pamenepo Yesu akutenga atate wa buthu’lo ndi amai ndi atumwi ake atatu kulowa m’chipinda m’mene mwagona mwana’yo. Iye akum’gwira dzanja nati: ‘Tauka!’ Ndipo anakhala ndi moyo, monga momwe’di mukuonera pano. Ndipo iye akunyamuka ndi kuyenda-yenda! N’cho chifukwa chake amai ndi atate wake ali achimwemwe kopambana.

Uyu sindiye munthu woyamba kuukitsidwa kwa akufa ndi Yesu. Woyamba amene Baibulo limam’simba ndiye mwana wamwamuna wa mkazi wamasiye amene amakhala mu mzinda wa Nayini. Pambuyo pake, Yesu akuukitsa’nso Lazaro, mbale wa Mariya ndi Marita, kwa akufa. Pamene Yesu alamulira monga mfumu ya Mulungu, adzaukitsa anthu ochuluka kwambiri. Kodi sitingakhale okondwa ndi zimene’zo?

Luka 8:40-56; 7:11-17; Yohane 11:17-44.Mafunso

  • Kodi atate wa mtsikana ali pachithunziyu ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani iye ndi mkazi wake akuda nkhaŵa kwambiri?
  • Kodi Yairo akuchita chiyani atapeza Yesu?
  • Kodi n’chiyani chikuchitika pamene Yesu akupita ku nyumba ya Yairo, ndipo kodi Yairo akulandira uthenga wotani ali panjira?
  • N’chifukwa chiyani anthu amene ali m’nyumba ya Yairo akumuseka Yesu?
  • Atatenga atumwi atatu ndi atate ndi amayi a buthulo kuloŵa nawo m’chipinda mwa buthulo, kodi Yesu akuchita chiyani?
  • Kodi ndani winanso amene Yesu wamuukitsa kwa akufa, ndipo kodi zimenezi zikusonyeza chiyani?

Mafunso ena