Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 91: Yesu Aphunzitsa pa Phiri

Nkhani 91: Yesu Aphunzitsa pa Phiri

MUKUMUONA Yesu wakhala apa’yu. Iye akuphunzitsa anthu onse’wa pa phiri m’Galileya. Awo okhala chifupi naye kwambiri ndiwo ophunzira ake. Iye wasankha 12 a iwo kukhala atumwi. Atumwi ndiwo ophunzira apadera a Yesu. Kodi mukudziwa maina ao?

Yesu akuphunzitsa

Pali Simoni Petro ndi mbale wake Andreya. Pali Yakobo ndi Yohane, amene’nso ali abale. Mtumwi wina akuchedwa’nso Yakobo, ndipo wina’nso akuchedwa Simoni. Atumwi awiri akuchedwa Yudasi. Mmodzi ndiye Yudasi Isikariote, ndipo Yudasi wina’yo akuchedwa’nso Tadeyo. Ndiyeno pali Filipo ndi Natanayeli (wochedwa’nso Bartolomeyo), ndi Mateyu ndi Tomasi.

Atabwerera’nso ku Samariya, Yesu anayamba kulalikira kwa nthawi yoyamba kuti: ‘Ufumu wa kumwamba wayandikira.’ Kodi mukudziwa chimene ufumu umene’wo uli? Ndiwo boma leni-leni la Mulungu. Yesu ndiye mfumu yake. Iye adzalamulira ali kumwamba ndi kudzetsa mtendere pa dziko lapansi. Dziko lonse lapansi lidzapangidwa kukhala paradaiso wokongola ndi ufumu wa Mulungu.

Yesu akuphunzitsa anthu pano za ufumu’wo. ‘Pempherani motere,’ akulongosola motero. “Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwe’cho pansi pano.” Anthu analicha ‘Pemphero la Ambuye.’ Ena amalicha ‘Atate Wathu.’ Kodi mungalinene pemphero lonse’lo?

Yesu akuphunzitsa’nso anthu m’mene ayenera kuchitirana. ‘Chitirani ena zimene mukafuna kuti iwo akuchitireni,’ akutero. Kodi simumakondwera pamene ena akuchitirani mokoma mtima? Yesu akuti, chotero tiyenera kuchitira ena mokoma mtima. Kodi sikudzakhala kwabwino kwambiri m’paradaiso wa pa dziko pano pamene ali yense adzakhala wokhoza kuchita izi?

Mateyu chaputala 5 mpaka 7; 10:1-4.Mafunso

  • M’chithunzichi, kodi n’kuti kumene Yesu ali pophunzitsa, ndipo amene akhala pafupi kwambiri nayewo ndi ndani?
  • Kodi mayina a atumwi 12 ndi ndani?
  • Kodi Ufumu umene Yesu akulalikira n’chiyani?
  • Kodi Yesu akuphunzitsa anthuwo kupempherera chiyani?
  • Kodi Yesu akunena kuti anthu ayenera kuchitirana zinthu motani?

Mafunso ena