TAONANI kamnyamata’ko kakulankhula ndi anthu achikulire’wa. Iwo ndi aphunzitsi m’kachisi wa Mulungu pa Yerusalemu. Kamnyamata’ko ndiko Yesu. Iye wasinkhukirapo. Tsopano ali ndi zaka 12. TAONANI kamnyamata’ko kakulankhula ndi anthu achikulire’wa. Iwo ndi aphunzitsi m’kachisi wa Mulungu pa Yerusalemu. Kamnyamata’ko ndiko Yesu. Iye wasinkhukirapo. Tsopano ali ndi zaka 12.

Aphunzitsi’wo akudabwa kwambiri kuti iye akudziwa zambiri zonena za Mulungu ndi zolembedwa m’Baibulo. Koma n’chifukwa ninji Yosefe ndi Mariya nawo’nso salipo? Kodi ali kuti? Tiyeni tione.

Yesu ali kamnyamata akulankhula ndi aphunzitsi

Chaka chiri chonse Yosefe anali kumka ndi banja lake ku Yerusalemu kaamba ka phwando lapadera la Paskha. Ndi ulendo wautali kuchokera ku Nazarete kukafika ku Yerusalemu Palibe anali ndi galimoto, ndipo palibe matreni. Analibe pa nthawi’yo. Ochuluka anayenda pansi, ndipo kumawatengera masiku atatu kukafika ku Yerusalemu.

Pa nthawi ino Yosefe anali ndi banja lalikulu. Chotero pali ang’ono ndi alongo a Yesu owayang’anira. Eya, chaka chino Yosefe ndi Mariya anali atanyamuka ndi ana ao pa ulendo wao wautali’wo wobwerera ku Nazarete. Iwo akuganiza kuti Yesu akuyendera limodzi ndi oyenda ena’wo. Koma pamene akuima pa mapeto a tsiku, Yesu palibe. Iwo akum’funa-funa pakati pa achibale ao ndi mabwenzi, koma sali nawo! Chotero akubwerera ku Yerusalemu kukam’funa-funa.

Potsiriza iwo akum’peza pano ndi aphunzitsi. Iye akuwamvetsera nawafunsa mafunso. Ndipo anthu onse akudabwa ndi nzeru za Yesu. Koma Mariya akuti: ‘Mwanawe, watichitiranji izi? Atate wako ndi ine takhala odera nkhawa kwambiri kuyesa-yesa kukupeza.’

‘Mumandifuniranji?’ akutero Yesu. ‘Kodi simunadziwe kuti ndiyenera kukhala m’nyumba ya Atate wanga?’

Inde, Yesu amakonda kukhala kumene iye angaphunzire za Mulungu. Kodi m’menemo sindimo m’mene ife’nso tiyenera kumvera? Kwaoko ku Nazarete, Yesu ankapita ku misonkhano ya kulambira mlungu ndi mlungu. Chifukwa nthawi zonse anamvetsera, anaphunzira zinthu zambiri za m’Babulo. Tiyeni tikhale ngati Yesu ndi kutsatira chitsanzo chake.

Luka 2:41-52; Mateyu 13:53-56.Mafunso

  • Kodi Yesu ali ndi zaka zingati pachithunzipa, ndipo ali kuti?
  • Kodi Yosefe ndi banja lake amachita chiyani chaka chilichonse?
  • Atayenda tsiku limodzi pa ulendo wobwerera kwawo, n’chifukwa chiyani Yosefe ndi Mariya akubwerera ku Yerusalemu?
  • Kodi Yosefe ndi Mariya akumupeza kuti Yesu, ndipo n’chifukwa chiyani anthu kumeneko akudabwa?
  • Kodi Yesu akunena chiyani kwa amayi ake, Mariya?
  • Kodi tingakhale bwanji ngati Yesu pophunzira za Mulungu?

Mafunso ena