Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 86: Amuna Atsogozedwa ndi Nyenyezi

Nkhani 86: Amuna Atsogozedwa ndi Nyenyezi
Okhulupirira nyenyezi

KODI mukuona nyenyezi yowala’yo imene amuna’wa akuiloza? Pamene ananyamuka m’Yerusalemu, nyenyezi’yo inaoneka. Amuna’wa ngochokera Kum’mawa, ndipo iwo amaphunzira nyenyezi. Iwo amakhulupirira kuti nyenyezi yatsopano’yi ikuwatsogolera kwa wina wake wofunika.

Pamene amuna’wo akufika ku Yerusalemu, iwo anafunsa kuti: ‘Kodi ali kuti mwana amene adzakhala mfumu ya Ayuda?’ “Ayuda” ndi dzina lina la Aisrayeli. ‘Tinayamba kuona nyenyezi ya mwana’yo tikali Kum’mawa,’ anatero amuna’wo, ndipo tadza kudzam’lambira.’

Herode, amene ali mfumu pa Yerusalemu, pomva izi, anabvutika maganizo. Iye sanafune kuti mfumu ina itenge malo ake. Chotero iye anaitana akulu ansembe nawafunse kuti: ‘Kodi mfumu yolonjezedwa’yo idzabadwira kuti’ Iwo akuyankha kuti: ‘Baibulo limati m’Betelehemu.’

Chotero Herode anaitana amuna Akum’mawa’wo, nati nawo: ‘Mukani mukafune-fune kamwana’ko. Mutakapeza, zandidziwitseni. Nane’nso ndikufuna kumka kukakalambira.’ Koma, kweni-kweni, Herode anafuna kupeza mwana’yo ndi kum’pha!

Ndiyeno nyenyezi’yo ikuyenda patsogolo pa amuna’wo kumka ku Betelehemu, ndipo ikuima pa malo pamene pali mwana’yo. Atalowa m’nyumbamo amuna’wo, akupezamo Mariya ndi mwana’yo Yesu. Iwo akutulutsa mphatso nazipereka kwa Yesu. Koma kenako Yehova akuwachenjeza m’kulota kusabwerera kwa Herode. Chotero akubwerera kwao pa njira ina.

Herode atamva kuti amuna a Kum’mawa aja abwerera kwao, akupsya mtima kwambiri. Chotero akulamula kuti ana amuna onse m’Betelehemu a zaka ziwiri ndi zocheperapo aphedwe. Koma Yehova akuchenjeza Yosefe pasadakhale m’kulota, ndipo Yosefe ndi banja lake akuchoka kumka ku Betelehemu. Kenako, Yosefe atamva kuti Herode wafa, akutenga Mariya ndi Yesu nabwerera ku Nazarete kwao. Kuno ndiko kumene Yesu anakulira.

Kodi muganiza kuti ndani amene anapangitsa nyenyezi yatsopano’yo kuwala? Pajatu, choyamba amuna’wo anamka ku Yerusalemu ataona nyenyezi’yo. Satana Mdierekezi anafuna kupha Mwana wa Mulungu, ndipo anadziwa kuti Mfumu Herode ya Yerusalemu ikayesa kum’pha. Chotero Satana ndiye amene ayenera kukhala atapangitsa nyenyezi’yo kuwala.

Mateyu 2:1-23; Mika 5:2.Mafunso

  • Kodi amuna ali m’chithunziŵa ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani mmodzi wa iwo akuloza nyenyezi yowala kwambiri?
  • N’chifukwa chiyani Mfumu Herode akukwiya, ndipo akuchita chiyani?
  • Kodi nyenyezi yowala ija inawalondolera kuti amunawo, koma n’chifukwa chiyani anabwerera kwawo podzera njira ina?
  • Kodi Herode akupereka lamulo lotani, ndipo n’chifukwa chiyani akupereka lamulo limeneli?
  • Kodi Yehova akuuza Yosefe kuchita chiyani?
  • Kodi ndani anachititsa nyenyezi yatsopanoyo kuwala, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

Funso lina

  • Ŵerengani Mateyu 2:1-23.

    Kodi Yesu anali ndi zaka zingati pamene okhulupirira nyenyezi anadzamuzonda, ndipo anali kukhala kuti? (Mat. 2:1, 1116)