Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Chigawo 6: Kubadwa kwa Yesu Mpaka pa Imfa Yake

Chigawo 6: Kubadwa kwa Yesu Mpaka pa Imfa Yake

Mngelo Gabrieli anatumizidwa kwa mtsikana wabwino kwambiri wochedwa Mariya. Iye anamuuza kuti akabala mwana amene adzalamulira monga mfumu kwamuyaya. Mwana’yo Yesu, anabadwira modyera ng’ombe, m’mene abusa anadzam’zondamo. Pambuyo pake, nyenyezi inatsogolera amuna ochokera Kum’mawa kumka kwa kwamwana’ko. Timaphunzira za amene anachititsa awa kuona nyenyezi’yi, ndi m’mene Yesu anapulumutsidwira ku zoyesa-yesa za kum’pha.

Kenako, tikupeza Yesu, pamene anali ndi zaka 12, akulankhula ndi aphunzitsi m’kachisi. Zaka khumi ndi zisanu ndi zitatu pambuyo pake iye anabatizidwa, ndiyeno anayamba kulalikira Ufumu ndi ntchito ya kuphunzitsa imene Mulungu anam’tumizira pa dziko lapansi kudzaichita. Kuti am’thandiza m’ntchito’yi, Yesu anasankha amuna 12 nawapanga kukhala atumwi ake.

Yesu anachita’nso zozizwitsa zambiri. Iye anadyetsa anthu zikwi zochuluka ndi nsomba zazing’ono zowerengeka ndi mikate yowerengeka. Iye anachiritsa odwala ndipo ngakhale kuukutsa akufa. Potsirizira pake, timaphunzira za zinthu zambiri zimene zinachitikira Yesu m’kati mwa masiku otsiriza a moyo wake, ndi m’mene iye anaphedwera. Yesu analalikira kwa pafupi-fupi zaka zitatu ndi theka, chotero CHIGAWO 6 chikulowetsamo nyengo ya zaka zoposa pang’ono 34.

Yesu akuphunzitsa anthu

Onaninso

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Nkhani Zokhudza Moyo wa Yesu Zinalembedwa Liti?

Kodi panapita nthawi yaitali bwanji kuchokera pamene Yesu anafa kufika pamene mabuku a Uthenga Wabwino analembedwa?

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Yesu Khristu Ndani?

Dziwani chifukwa chake Yesu anafa, tanthauzo la mawu akuti dipo, komanso zimene Yesu akuchita panopa.