Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 81: Kudalira Thandizo la Mulungu

Nkhani 81: Kudalira Thandizo la Mulungu

PAFUPI-FUPI anthu 50,000 akuyenda ulendo wautali’wo wochokera ku Babulo kumka ku Yerusalemu. Koma pofika, Yerusalemu wangokhala bwinja lalikulu. Mulibe wokhalamo. Iwo ayenera kumanga chiri chonse kachiwiri’nso.

Chinthu choyambirira chimene iwo akumanga ndicho guwa la nsembe. Awa ndi malo amene iwo angaperekerepo nsembe zopsyereza, kapena mphatso kwa Yehova. Miyezi yowerengeka pambuyo pake iwo akuyamba kumanga kachisi. Koma adani okhala m’maiko apafupipi sakufuna kuti Aisrayeli am’mange. Chotero Akuyesa kuwaopsyeza kuti aleke. Potsirizira pake, adani’wa akuchititsa mfumu yatsopano ya Perisiya kupanga lamulo loletsa ntchito yomanga’yo.

Zaka zambiri zikupitapo. Tsopano papita zaka 17 chibwerere Aisrayeli kuchokera ku Babulo. Yehova akutumiza mneneri wake Hagai ndi Zekariya kukauza anthu’wo kuyamba’nso kumanga. Anthu’wo akudalira m’thandizo la Mulungu, ndipo akumvera aneneri’wo. Iwo akuyamba kumanga’nso, ngakhale kuli kwakuti lamulo likunena kuti sayenera kukuchita.

Chotero mkulu wa Perisiya wochedwa Tatenayi akudza nafunsa Aisrayeli kuyenera kumene ali nako kwa kumanga kachisi. Iwo akumuuza kuti pamene iwo anali m’Babulo, Mfumu Koresi anawauza kuti: ‘Pitani, tsopano, ku Yerusalemu ndi kukamanga kachisi wa Yehova, Mulungu wanu.’

Tatenayi akutumiza kalata ku Babulo nafunsa ngati Koresi, amene tsopano ali wakufa, ananena’di zimene’zo. Posakhalitsa kalata ikudza kuchokera kwa mfumu yatsopano’yo. Ikunena kuti ananena’di. Ndipo chotero mfumu’yo ikulemba kuti: ‘Lolani Aisrayeli amange kachisi wa Mulungu wao. Ndipo ndikukulamulani kuwathandiza.’ M’kati mwa pafupi-fupi zaka zinai kachisi’yo watha, ndipo Aisrayeli ali achimwemwe kwambiri.

Zaka zina zambiri zukupitapo. Tsopano papita pafupi-fupi zaka 48 chiyambire pamene kachisi anamalizidwa. Anthu a m’Yerusalemu ali osauka, ndipo mzinda’wo ndi kachisi wa Mulungu sizikuoneka kukhala zokongola. Ku Babulo’ko Muisrayeli Ezara akumva za kufunikira kwa kukonza kachisi wa Mulungu. Chotero kodi mukudziwa chimene akuchita?

Ezara akumka kukaonana ndi Aritasasta, mfumu ya Perisiya, ndipo mfumu yabwino’yi ikupatsa Ezara mphatso zambiri zomka nazo ku Yerusalemu. Ezara akufunsa Aisrayeli okhala m’Babulo kum’thandiza kunyamula mphatso’zi kumka ku Yerusalemu. Anthu okwanira 6,000 akunena kuti adzamuka. Iwo ali ndi siliva wochuluka ndi golidi ndi zinthu zina za mtengo wapatali zomka nazo.

Ezara akubvutika maganizo, chifukwa chakuti muli anthu oipa m’njiramo. Anthu’wa angalande siliva ndi golidi wao, ndi kuwapha. Chotero Ezara akuitana anthu’wo, monga momwe mukuonera m’chinthunzi’chi. Ndiyeno akupemphera kwa Yehova kaamba ka chitetezo chake pa ulendo wao wobwerera ku Yerusalemu.

Ezara ndi Aisiraeli akupemphera

Yehova akuwatetezera. Ndipo pambuyo pa miyezi inai ya kuyenda, iwo akufika bwino lomwe ku Yerusalemu. Kodi zimene’zi sizikusonyeza kuti Yehova angatetezere awo amene amam’dalira kaamba ka chithandizo?

Ezara chaputala 2 mpaka 8.Mafunso

  • Kodi ndi anthu angati amene akuyenda ulendo wautali wochokera ku Babulo kupita ku Yerusalemu, koma kodi akupeza chiyani pofika?
  • Kodi n’chiyani chimene Aisrayeli akuyamba kumanga atafika, koma kodi adani awo akuchita chiyani?
  • Kodi Hagai ndi Zekariya ndi ndani, ndipo kodi akuuza anthuwo chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Tatenayi akutumiza kalata ku Babulo, ndipo kodi akulandira yankho lotani?
  • Kodi Ezara akuchita chiyani atamva kuti pakufunika kukonza kachisi wa Mulungu?
  • Kodi Ezara akupempherera chiyani m’chithunzichi, kodi pemphero lake likuyankhidwa motani, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani ifeyo?

Mafunso ena