Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 78: Zolembedwa ndi Manja pa Khoma

Nkhani 78: Zolembedwa ndi Manja pa Khoma
Dzanja likulemba pakhoma

KODI chikuchitika pano n’chiani? Anthu’wa ali pa madyerero. Mfumu ya Babulo yaitana anthu ochuka zikwi-zikwi. Akugwiritsira ntchito zikho zagolidi ndi zasiliva ndi mbale zotengedwa m’kachisi wa Yehova. Komano. modzidzimutsa, zala za dzanja la munthu zikuoneka m’malere naziyamba kulemba pa khoma. Ali yense akuopsyedwa.

Belisazara ndi alendo ake

Belisazara, mdzukulu wa Nebukadinezara, pa nthawi ino ndiye mfumu. Akuitana anzeru onse mopfuula. ‘Ali yense amene angadiwerengere zolembedwa’zi n’kundiuza kutanthauza kwake,’ ikutero mfumu’yo, ‘adzapatsidwa mphatso zambiri ndi kupangidwa kukhala wolamulira wachitatu mu ufumu.’ Koma palibe wanzeru wokhoza kuwerenga zolembedwa’zo, kapena kuzitanthauzira.

Mai wa mfumu pomva phokoso akudza modyeramo. ‘Chonde musaopsyedwe kwambiri,’ akutero mai’yo. ‘Muli munthu mu ufumu wanu wodziwa milungu yoyera. Muja gogo wanu Nebukadinezara anali mfumu anam’panga kukhala mkulu wa anzeru onse. Munthu’yo ndiye Danieli. Kamuitaneni, adzakuuzani tanthauzo lake.’

Pomwepo Danieli akulowetsedwa. Atakana kulandira mphatso iri yonse, Danieli akuyamba kufotokoza chifukwa chake Yehova pa nthawi ina anachotsa gogo wa Belisazara, Nebukadinezara pa ufumu. ‘Iye anali wodzitukumula kwambiri,’ Danieli akutero. ‘Yehova anam’langa.’

‘Koma inu,’ Danueli akuuza Belisazara, ‘munadziwa zonse zimene zinam’chitikira, ndipo komabe muli wonyada monga momwe analiri iye. Mwadza ndi zikho ndi mbale za m’kachisi wa Yehova ndi kumweramo. Mwatamanda milungu yopangidwa ndi mtengo, ndi mwala, ndipo simunalemekeza Mlengi wathu Wamkulu. Ndicho chifukwa chake Mulungu watumiza dzanja kudzalemba mau’wa.

‘Zolembedwa ndi izi,’ akutero Danieli: ‘ME′NE, ME′NE, TE′KEL ndi PAR′SIN.’

‘ME′NE amatanthauza kuti Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu n’kuwatha. TE′KEL amatanthauza kuti waikidwa pa muyeso nupezeka woperewera. PAR′SIN amatanthauza kuti ufumu wanu waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisi.’

Danieli akali chilankhulire, Amedi ndi Aperisi aukira kale Babulo. Akulanda mzinda’wo napha Belisazara. Mau olembedwa ndi manja pa khoma’wo akukwaniritsidwa usiku womwewo! Kodi n’chiani chimene chidzachitikira Aisrayeli tsopano? Tidzaona posachedwa, koma tiyeni tiyambe taona chimene chukuchitikira Danieli.

Danieli 5:1-31.Mafunso

  • Kodi chikuchitika n’chiyani pamene mfumu ya ku Babulo yakonza madyerero n’kugwiritsa ntchito zikho ndi mbale zotengedwa m’kachisi wa Yehova ku Yerusalemu?
  • Kodi Belisazara akuuza anzeru ake chiyani, koma kodi anzeruwo akulephera kuchita chiyani?
  • Kodi mayi ake a mfumuyo akumuuza kuti achite chiyani?
  • Malinga ndi zimene Danieli akuuza mfumuyo, n’chifukwa chiyani Mulungu watumiza dzanjalo kudzalemba pa khoma?
  • Kodi Danieli akufotokoza bwanji tanthauzo la mawu amene ali pakhomawo?
  • Kodi chikuchitika n’chiyani Danieli akali chilankhulire?

Mafunso ena