Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 77: Sakanagwada

Nkhani 77: Sakanagwada

KODI mukukumbukira kukhala mutamva za anyamata atatu’wa? Inde, iwo ndiwo mabwenzi a Danieli amene anakana kudya chimene sichinali chabwino kwa iwo. Ababulo anawacha Sadrake, Mesake ndi Abedinego. Koma tawayang’anani tsopano. Kodi n’chifukwa ninji sakugwadira chifano’chi mofanana ndi wina ali yense? Tiyeni tione.

Kodi mukukumbukira malamulo amene Yehova mwini anawalemba ochedwa Malamulo Khumi? Loyamba la amene’wa limati: ‘Usakhale nayo milungu ina koma ine ndekha.’ Anyamata’wa pano akumvera lamulo’li, ngakhale kuli kwakuti si chinthu chokhweka kuchichita.

Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, waitana anthu ambiri ochuka kudzalemekeza fano’li limene iye waliimika. Iye wangotha kumene kuuza anthu kuti: ‘Pakumva inu mau a mphalasa, azeze ndi zoyimbira zina, muyunera kugwadira fano lagolidi’li. Ali yense wosagwada ndi kulambira adzaponyedwa pompo m’ng’anjo ya moto.’

Pamene Nebukadinezara akumva kuti Sadrake, Mesake ndi Abedinego sanagwade, wapsya mtima kwambiri. Iye akuwachititsa kudza pamaso pake. Iye akuwapatsa mwai wina wakuti agwade. Koma anyamata’wo akudalira pa Yehova. ‘Mulungu wathu amene tim’tumikira akhoza kutipulumutsa,’ iwo akuuza motero Nebukadinezara. ‘Koma ngakhale ngati satipulumutsa, sitidzagwadira fano lanu lagolidi’li.’

Sadirake, Mesake ndi Abedinego

Pomva izi, Nebukadinezara akupsya mtima moonjezereka. Pali ng’anjo pafupipo ndipo akulamula kuti: ‘Sonkhezani ng’anjo’yo kasanu ndi kawiri kutentha kwake koposa poyamba!’ Ndiyeno akuchita kuti amuna amphamvu kopambana a ankhondo ake amange Sadrake, Mesake ndi Abedinego ndi kuwaponya m’ng’anjomo. Ng’anjo’yo njotentha kwambiri kwakuti amuna amphamvu’wo akuphedwa ndi malawi ake. Koma bwanji anyamata amene iwo anawaponyamo’wo?

Mfumu ikuyang’ana m’ng’anjomo, ndipo ikuopa kwambiri. ‘Kodi sitinamanga amuna atatu n’kuwaponya m’ng’anjo yotentha’yo?’ akufunsa.

‘Inde tinaponyamo,’ akuyankha motero atumiki ake.

‘Koma ndikuona amuna anai akuyenda-yenda m’motomo,’ akutero. ‘Ali osamangidwa, ndipo moto sukuwabvulaza. Ndipo wachinai’yo akuoneka ngati mulungu.’ Mfumu’yo ikumka pafupi ndi khomo la ng’anjo’yo niitana kuti: ‘Sadrake! Mesake! Abedinego! Tulukani, inu atumiki a Mulungu Wam’mwamba-mwamba!’

Pamene iwo akutuluka, ali yense akuona kuti sanabvulazike. Ndiyeno mfumu’yo ikuti: ‘Atamandidwe Mulungu wa Sadrake, Mesake ndi Abedinego! Watumiza mngelo wake nawapulumutsa chifukwa chakuti iwo sakanagwadira ndi kulambira mulungu ali yense kusiyapo wao.’

Kodi ichi si chitsanzo chabwino cha kukhulupirika choti ife tichitsatire?

Ekisodo 20:3; Danieli 3:1-30.Mafunso

  • Kodi Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, wapereka lamulo lotani kwa anthu?
  • N’chifukwa chiyani anzake atatu a Danieli sakugwadira fano la golidi?
  • Nebukadinezara atawapatsa Ahebri atatu aja mwayi wina woti agwade, kodi akusonyeza bwanji kuti akudalira Yehova?
  • Kodi Nebukadinezara akuuza amuna ake kuchita chiyani ndi Sadrake, Mesake, ndi Abedinego?
  • Kodi Nebukadinezara akuona chiyani atasuzumira m’ng’anjomo?
  • N’chifukwa chiyani mfumuyo ikulemekeza Mulungu wa Sadrake, Mesake, ndi Abedinego, ndipo kodi anyamata atatuŵa akutipatsa chitsanzo chotani?

Mafunso ena