PAPITA zaka zoposa 10 chiyambire pamene Nebukadinezara anatenga Aisrayeli ophunzira kopambana kumka nawo ku Babulo. Tsopano onani zimene zikuchitika! Yerusalemu akutenthedwa, Ndipo Aisrayeli osaphedwa akutengedwa kukhala akapolo kumka nawo ku Babulo.

Pajatu, izi ndizo zimene mneneri wa Yehova anachenjeza kuti zikachitika anthu’wo akapanda kusintha njira zao zoipa. Koma Aisrayeli sanamvere aneneri. Anapitirizabe kulambira milungu yonyenga m’malo mwa Yehova. Chotero iwo anali oyenerera kulangidwa. Tikudziwa izi chifukwa chakuti mneneri wa Mulungu Ezekieli akutiuza za zinthu zoipa zimene Aisrayeli analinkuchita.

Kodi Ezekieli mukum’dziwa? Ndiye mmodzi wa anyamata amene Nebukadinezara anawatengera ku Babulo zaka 10 zapita’zo kuonongedwa kwakukulu’ku kwa Yerusalemu kusanachitike. Danieli ndi anzake atatu aja, nawo’nso anatengeredwa ku Babulo pa nthawi yomwe’yi.

Ezekieli akali m’Babulo, Yehova akum’sonyeza zoipa zimene zikuchitika m’Yerusalemu pa kachisi. Yehova akuchita izi mwa chozizwitsa. Ezekieli ali’di chikhalire m’Babulo, koma Yehova akum’chititsa kuona chiri chonse chimene chikuchitika pa kachisi. Ndipo zimene iye akuona n’zobvutitsa maganizo!

‘Taona zonyansa zimene anthu akuchita m’kachisi muno,’ Yehova akuuza motere Ezekieli. ‘Taona makoma okutidwa ndi zithunzi za njoka ndi zinyama zina’wo. Ndipo taona Aisrayeli akuzilambira!’ Iye akuona zinthu’zi, ndipo akulemba zimene akuona zikuchitika.

Akapolo akuchoka ku Yerusalemu

‘Kodi ukuona zimene atsongoleri a Israyeli akuchita mu mdimamo?’ Yehova akufunsa Ezekieli. Inde, naye’nso akuziona. Muli amuna 70, ndipo akulambira milungu yonyenga. Iwo akuti: ‘Yehova sationa. Iye wasiya dziko.’

Ndiyeno Yehova akusonyeza Ezekieli akazi ena ku chipata cha kumpoto cha kachisi. Akhala pamenepo akulambira mulungu wonyenga Tamuzi. Ndipo taona amuna’wo pa khomo la kachisi! Alipo 25. Ezekieli akuwaona. Iwo akuweramira kum’mawa ndi kulambira dzuwa!

‘Anthu’wa sakundilemekeza,’ akutero Yehova. ‘Iwo sakungochita kokha zoipa koma kudza ku kachisi wanga kweni-kweni kudzazichita! Chotero Yehova akulonjeza kuti: ‘Iwo adzaona mphamvu ya mkwiyo wanga. Ndipo sindidzawamvera chisoni pakuonongedwa iwo.’

Pangopita zaka pafupi-fupi zitatu zokha Yehova ataonetsa Ezekieli zinthu’zi pamene Aisrayeli akupandukira Mfumu Nebukadinezara. Chotero iye akumka kukamenyana nawo. Patapita chaka ndi theka Ababulo akuboola malinga a Yerusalemu ndi kutentha m’zinda’wo psyiti. Anthu ochuluka akuphedwa kapena kutengedwa ukapolo kumka ku Babulo.

Kodi Yehova walolelanji chionongeko choopsya’chi kuchitikira Aisrayeli? Inde. chifukwa cha kusamvetsera Yehova ndipo akhala asakumvera malamulo ake. Izi zikutisonyeza kufunika kwa kuchita nthawi zonse zimene Mulungu amanena.

Poyamba anthu pang’ono akuloledwa kukhala m’dziko la Israyeli. Nebukadinezara akuika Myuda wochedwa Gedaliya kuyang’anira anthu’wa. Komano Aisrayeli ena akupha Gedaliya. Tsopano iwo akuopa kuti Ababulo akadza kudzawaononga onse chifukwa cha kuchitika kwa choipa’chi. Chotero iwo akuumiriza Yeremiya kutsagana nawo, ndipo akuthawira ku Igupto.

Izi zikuchititsa dziko la Israyeli kukhala lopanda anthu. Kwa zaka 70 palibe akukhala m’dziko’lo. Liri labwinja kotheratu. Koma Yehova akulonjeza kuti adzabwezera anthu ake ku dziko’lo pambuyo pa zaka 70. Pa nthawi’yi, kodi n’chiani chimene chikuchitikira anthu a Mulungu m’dziko la Babulo kumene iwo anatengeredwa’ko? Tiyeni tione.

2 Mafumu 25:1-26; Yeremiya 29:10; Ezekieli 1:1-3; 8:1-18.Mafunso

  • Kodi n’chiyani chikuchitikira Yerusalemu ndi Aisrayeli amene awasonyeza m’chithunzichi?
  • Kodi Ezekieli ndi ndani, ndipo kodi Yehova akumusonyeza zoipa zotani?
  • Kodi n’chiyani chimene Yehova akulonjeza chifukwa choti Aisrayeli sakum’lemekeza?
  • Kodi n’chiyani chimene Mfumu Nebukadinezara akuchita Aisrayeli atamupandukira?
  • N’chifukwa chiyani Yehova akulola kuti Aisrayeli awonongedwe moipa chonchi?
  • Kodi n’chiyani chikuchititsa kuti dziko la Israyeli likhale lopanda anthu, ndipo linakhala choncho kwa nthaŵi yaitali bwanji?

Mafunso ena