Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 75: Anyamata Anai M’Babulo

Nkhani 75: Anyamata Anai M’Babulo

MFUMU Nebukadinezara akutenga Aisrayeli onse ophunzira bwino kwambiri kumka nawo ku Babulo. Kenako mfumu ikusankha pakati pao anyamata okongola ndi ochenjera kopambana. Anai a amene’wa ndiwo anyamata mukuwaona apa’wa. Mmodzi’yo ndi Danieli, ndipo atatu ena’wo Ababulo akuwacha Sadrake, Mesake ndi Abedinego.

Nebukadinezara akulinganiza kuphunzitsa anyamata’wo kuti atumikire m’mphala yake. Pambuyo pa zaka zitatu za kuphunzitsidwa iye adzangosankhapo ochenjera kopambana onse kum’thandiza kuthetsa zobvuta. Mfumu ikufuna kuti anyamata’wo akhale amphamvu ndi athanzi m’kati mwa kuphunzitsidwa kwao. Chotero ikulamula kuti awapatse zakudya zabwino zofanana’zo zimene iye amadya ndi banja lake.

Danieli, Sadrake, Mesake ndi Abedinego akufotokoza zimene amakhulupirira

Taonani Danieli’yo. Kodi mukudziwa zimene akunena ndi mtumiki wamkulu wa mfumu’yo Asipenazi? Akumuuza kuti sakufuna kudya zakudya zabwino za pa gome la mfumu. Koma Asipenazi akudera nkhawa. ‘Mfumu ndiyo imene yanena zimene muzidya ndi kumwa,’ akutero. ‘Ndipo ngati simuoneka muli athanzi monga anyamata ena’wo, angandiphe.’

Chotero Danieli akumka kwa wom’yang’anira woikidwa ndi Asipenazi limodzi ndi mabwenzi ake atatu’wo. ‘Chonde tiyeseni kwa masiku 10,’ akutero. ‘Tipatseni zomera tidye ndi madzi timwe. Ndiyeno mutiyerekezere ndi anyamata ena odya chakudya cha mfumu, ndi kuona amene akuoneka bwino.’

Woyang’anira’yo akubvomereza kuchita izi. Pakutha kwa masiku 10, Danieli ndi anzake atatu’wo akuoneka kukhala athanzi kwambiri koposa anyamata ena onse’wo. Chotero woyang’anira’yo akuwalola kumangodya zomera m’malo mwa zimene mfumu imapereka.

Zitatha zaka zitatu anyamata’wo akutengeredwa kwa Nebukadinezara. Pambuyo pa kulankhula nawo onse, mfumu ikuona Danieli ndi mabwenzi ake atatu kukhala koposa onse. Chotero akuwatenga kum’thandiza m’mphala yake. Ndipo pali ponse pamene iyo ifunsa Danieli, Sadrake, Mesake ndi Abedinego mafunso kapena kuwapatsa chothetsa nzeru, iwo akudziwa nthawi 10 koposa ali yense wa ansembe ake kapena anzeru.

Danieli 1:1-21.Mafunso

  • Kodi anyamata anayi amene ali pachithunzipa ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali m’Babulo?
  • Kodi n’chiyani chimene Nebukadinezara akulinganiza kuchitira anyamatawo, ndipo akulamula atumiki ake kuchita chiyani?
  • Kodi n’chiyani chimene Danieli akupempha chokhudza zakudya ndi zakumwa zake ndi za anzake atatu?
  • Atadya zomera kwa masiku 10, kodi Danieli ndi anzake atatu aja akuoneka bwanji powayerekezera ndi anyamata ena onse?
  • Kodi chinachitika n’chiyani kuti Danieli ndi anzake atatu aja akhale m’mphala mwa mfumu, ndipo kodi iwowo akudziŵa zinthu zambiri motani poyerekezera ndi ansembe ndi anzeru?

Mafunso ena