Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 74: Munthu Wosaopa

Nkhani 74: Munthu Wosaopa

ONANI anthu’wo akuseka mnyamata’yu. Kodi mukum’dziwa? Uyu ndi Yeremiya. Iye ndi mneneri wofunika kwambiri wa Mulungu.

Anthu akumuseka Yeremiya

Chotero pamene Yosiya wangoyamba kumene kuononga mafano m’dziko’lo, Yehova akuuza Yeremiya kukhala mneneri Wake. Komabe, iye akuganiza kuti akali mwana wosati n’kukhala mneneri. Koma Yehova akuti Iye adzam’thandiza.

Iye akuuza Aisrayeli kuleka kuchita zoipa. ‘Milungu imene anthu a dziko amailambira ndi yonyenga,’ akutero. Koma Aisrayeli ambiri akakonda kulambira mafano koposa kulambira Mulungu woona Yehova. Pamene Yeremiya akuuza anthu’wo kuti Mulungu adzawalanga chifukwa cha kuipa kwao, akungom’seka.

Zaka zambiri zikupitapo. Yosiya akufa, ndipo patapita miyezi itatu mwanake Yehoyakimu akukhala mfumu. Yeremiya akuuzabe anthu kuti: ‘Yerusalemu adzaonongedwa ngati simusintha njira zanu zoipa’zi.’ Ansembe akugwira Yeremiya napfuula kuti: ‘Uyenera kuphedwa chifukwa cha kunena izi.’ Ndiyeno akuuza akalonga a Israyeli kuti: ‘Yeremiya ayenera kuphedwa, chifukwa walankhula motsutsa mzinda wathu.’

Kodi iye adzachitanji tsopano? Sakuopa! Iye akuuza onse’wo kuti: ‘Yehova ananditumiza kudzakuuzani zinthu’zi. Ngati simusintha njira zanu za kakhalidwe, Yehova adzaononga Yerusalemu. Koma dziwani izi: Mukandipha, mudzakhala mukupha munthu wosalakwa.’

Akalonga akulola Yeremiya kukhalabe ndi moyo, koma Aisrayeli sakusintha njira zao zoipa. Kenako Nebukadinezara, mfumu ya Babulo, akudza kudzamenyana ndi Yerusalemu. Potsiriza iye akupanga Aisrayeli kukhala akapolo ake. Iye akutenga zikwi zochuluka kumka nazo ku Babulo. Taganizirani m’mene zikakhalira kutengedwa ndi anthu osawadziwa kumka ku dziko lachilendo!

Yeremiya 1:1-8; 10:1-5; 26:1-16; 2 Mafumu 24:1-17.Mafunso

  • Kodi mnyamata ali m’chithunziyu ndi ndani?
  • Kodi Yeremiya akuganiza chiyani pankhani yoti akhale mneneri, koma kodi Yehova akumuuza chiyani?
  • Kodi Yeremiya akuuzabe anthu uthenga wotani?
  • Kodi ansembe akuyesera bwanji kuletsa Yeremiya, koma kodi iye akusonyeza bwanji kuti sakuopa?
  • Kodi n’chiyani chikuchitika pamene Aisrayeli sakusintha njira zawo zoipa?

Mafunso ena