Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 72: Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya

Nkhani 72: Mulungu Athandiza Mfumu Hezekiya

KODI mukudziwa chifukwa chake munthu’yu akupemphera kwa Yehova? Kodi waikiranji makalata’wa patsogolo pa guwa lansembe la Yehova? Mwamuna’yo ndiye Hezekiya. Iye ndi mfumu ya ufumu wakumwela wa mafuko awiri wa Israyeli. Ndipo ali m’mabvuto ambiri. Chifukwa ninji?

Mfumu Hezekiya ikupemphera

Chifukwa chakuti ankhondo a Asuri aononga kale mafuko 10 akumpoto. Yehova akulola izi kuchitika chifukwa chakuti athu’wa anali oipa kwambiri. Tsopano ankhondo a Asuri adza kudzamenyana ndi ufumu wa mafuko awiri.

Mfumu ya Asuri yangotumiza kumene makalata kwa Hezekiya. Hezekiya wawaika pano pamaso pa Mulungu. Iwo akunyoza Yehova, ndi kuuza Hezekiya kuleka. N’cho chifukwa chake Hezekiya akupemphera kuti: ‘O Yehova, tipulumutseni kwa mfumu ya Asuri. Pamenepo mitundu yonse idzadziwa kuti inu nokha ndinu Mulungu.’ Kodi Yehova adzamvetsera Hezekiya?

Iye ndi mfumu yabwino. Iye sali ngati mafumu oipa a mafuko 10 a ufumu wa Israyeli, kapena ngati atate wake woipa Ahazi. Hezekiya wakhala wosamalitsa kumvera malamulo onse a Yehova. Chotero, atatha kupemphera, mneneri Yesaya akum’tumizira uthenga uwu wochokera kwa Yehova: ‘Mfumu ya Asuri sidzalowa m’Yerusalemu. Palibe ali yense wa ankhondo ake adzauyandikira. Iwo sadzaponyamo mubvi ndi umodzi womwe.’

Taonani pa chithunzi cha pa tsamba lino. Kodi mukudziwa amene ankhondo akufa’wa ali? Iwo ndi a Asuri. Yehova anatumiza mngelo wake, ndipo mu usiku umodzi wokha anapha ankhondo a Asuri 185,000. Chotero mfumu ya Asuri ikuchoka nibwerera kwao.

Asilikali a Asuri ataphedwa

Ufumu wa mafuko awiri wapulumutsidwa, anthu’wo nakhala ndi mtendere kwa kanthawi. Koma atafa Hezekiya mwanake Manase akukhala mfumu. Manase ndi mwanake Amoni wom’tsatira onse ndi mafumu oipa kwambiri. Chotero kachiwiri’nso dziko’lo ladzazidwa ndi upandu ndi chiwawa. Pamene Mfumu Amoni akuphedwa ndi atumiki ake, mwanake Yoasi akukhala mfumu ya ufumu wa mafuko awiri’wo.

2 Mafumu 18:1-36; 19:1-37; 21:1-25.Mafunso

  • Kodi mwamuna ali m’chithunziyu ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ali m’mavuto ambiri?
  • Kodi makalata amene Hezekiya waika pamaso pa Mulungu ndi otani, ndipo Hezekiya akupempherera chiyani?
  • Kodi Hezekiya ndi mfumu yotani, ndipo Yehova akumutumizira uthenga wotani kudzera mwa mneneri Yesaya?
  • Kodi mngelo wa Yehova anachita chiyani kwa Asuri, monga momwe chikusonyezera chithunzichi?
  • Ngakhale kuti ufumu wa mafuko aŵiri uli ndi mtendere kwa kanthaŵi, n’chiyani chikuchitika Hezekiya atamwalira?

Mafunso ena