Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 70: Yona ndi Chinsomba

Nkhani 70: Yona ndi Chinsomba

TAONANI munthu ali m’madzi’yo. Ali m’bvuto, kodi si choncho? Chinsomba’cho chatsala pang’ono kum’meza! Kodi mukudziwa munthu’yu? Dzina lake ndi Yona. Tiyeni tione m’mene analowera m’bvuto lalikulu kwambiri’lo.

Yona ndi mneneri wa Yehova. Sipanapite nthawi yaitali chifere mneneri Elisa pamene Yehova akuuza Yona kuti: ‘Muka ku mzinda waukulu wa Nineve. Kuipa kwa anthu kumene’ko n’kwakukulu kwambiri, ndipo ndikufuna kuti ukalankhule nawo za izi.’

Yona ndi chinsomba chachikulu

Koma Yona sakufuna kupita. Chotero akukwera m’bwato limene likumka kwina kosakhala ku Nineve. Yehova sakukondwera naye chifukwa cha kuthawa’ko. Chotero Iye akuchititsa pfunde lalikulu. N’loipa kwambiri kwakuti bwato’lo lingamire. Amalinyero akuopa kwambiri, ndipo akuitanira kwa milungu yao kaamba ka chithandizo.

Potsirizira Yona akuwauza kuti: ‘Ine ndimalambira Yehova, Mulungu amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo ndikuthawa kuchita zimene Yehova wandiuza kuchita.’ Chotero amalinyero’wo akufunsa kuti: ‘Tichitenji kwa iwe kuti tiletse pfunde’li?

‘Ndiponyeni m’nyanjamo, ndipo nyanja idzakhala’nso bata,’ akutero Yona. Amalinyero’wo sakufuna kukuchita, koma pamene pfunde’lo likuipira-ipira potsirizira pake akuponyera Yona m’madzimo. Pompo pfunde’lo likuleka, ndipo nyanja’yo yakhala bata kachiwiri’nso.

Pamene Yona akumira m’madzimo, chinsomba chikum’meza. Koma sakufa. Kwa mausana ndi mausiku atatu ali m’mimba mwa nsomba’yo. Iye ali wachisoni kwambiri kuti sanamvere Yehova ndi kupita ku Nineve. Chotero kodi mukudziwa chimene iye akuchita?

Yona akupemphera kwa Yehova kaamba ka chithandizo. Ndiyeno Yehova akuchititsa nsomba’yo kum’sanzira pa mtunda pouma. Pambuyo pake Yona akumka ku Nineve. Kodi zimene’zi sizikutiphunzitsa m’mene kuliri kofunika kuti tiyenera kuchita zimene Yehova akunena?

Bukhu la Baibulo la Yona.Mafunso

  • Kodi Yona ndi ndani, ndipo Yehova akumuuza kuti achite chiyani?
  • Chifukwa chakuti sakufuna kupita kumene Yehova wamuuza, kodi Yona akuchita chiyani?
  • Kodi Yona akuuza amalinyero kuchita chiyani kuti aletse mafunde?
  • Monga mukuonera pachithunzipa, kodi n’chiyani chikuchitika pamene Yona akumira?
  • Kodi Yona akukhala m’mimba mwa chinsomba kwa nthaŵi yaitali bwanji, ndipo ali m’menemo akuchita chiyani?
  • Kodi Yona akupita kuti atatuluka m’mimba mwa chinsombacho, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

Mafunso ena

Onaninso

MAKADI A ANTHU OTCHULIDWA M’BAIBULO

Khadi la M’Baibulo Lonena za Yona

Kodi nkhani ya m’Baibulo yonena za Yona imatiphunzitsa makhalidwe a Yehova ati?