Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 66: Yezebeli—Mkazi Woipa wa Mfumu

Nkhani 66: Yezebeli—Mkazi Woipa wa Mfumu

ATAFA Mfumu Yerobiamu, mfumu iri yonse imene ikulamulira ufumu wakumpoto wa mafuko 10 a Israyeli njoipa. Mfumu Ahabu ndiye anali woipitsitsa. Kodi mukudziwa chifukwa chake? Chifukwa chimodzi chachikulu ndicho mkazi wake, Mkazi woipa wa Mfumu Yezebeli.

Yezebeli si mkazi Wachiisrayeli. Iye ndi mwana wamkazi wa mfumu ya Sidoni. Iye amalambira mulungu wonyenga Baala, ndipo akuchititsa Ahabu ndi Aisrayeli ambiri kulambira’nso Baala. Yezebeli amada Yehova ndipo akupha aneneri ake ambiri. Ena anafunikira kubisala m’mapanga kuti asaphedwe. Yezebeli akafuna kanthu kena, iye angangopha munthu kuti achipeze.

Tsiku lina Mfumu Ahabu wakwiya kwambiri. Chotero Yezebeli akum’funsa kuti: ‘Kodi wakwiyiranji lero?’

‘Chifukwa cha zimene Naboti wandiuza,’ akutero Ahabu. ‘Ndinafuna kugula munda wake wamphesa. Koma iye anati sindingaugule.’

Yezebeli akuti, ‘Usabvutike, ndidzakupezera ndine.’

Chotero Yezebeli akulembera makalata kwa akalonga ena a mu mzinda umene Naboti’yu amakhala. ‘Pezani anthu ena oipa oti anamizire Naboti kuti anatukwana Mulungu ndi mfumu,’ iye akuwauza motero. ‘Ndiyeno m’tulutsireni kunja kwa mzinda ndi kum’ponya miyala mpaka atafa.’

Pamene angomva kuti Naboti wafa, iye akuti kwa Ahabu: ‘Tsopano pita katenge munda wake wamphesa.’ Kodi simubvomereza kuti Yezebeli ayenera kulangidwa chifukwa cha kuchita chinthu choopsya’chi?

Mfumukazi Yezebeli

Chotero, m’nthawi yake, Yehova akutumiza Yehu kukam’langa. Pakumva Yezebeli kuti Yehu akudza, akulocha maso ake ndi kuyesa kudzikonza kuti aoneke kukhala wokongola. Koma pakudza Yehu ndi kuona Yezebeli pa zenera, iye akuitana amuna okhala m’mphala’yo nati: ‘Mponyereni pansi!’ Amuna’wo akumvera, monga momwe mukuonera m’chithunzi’cho. Akum’ponyera pansi, nafa. Ndiwo mapeto a Yezebeli woipa’yo.

1 Mafumu 16:29-33; 18:1-4; 21:1-16; 2 Mafumu 9:30-37.Mafunso

 • Kodi Yezebeli ndi ndani?
 • N’chifukwa chiyani Mfumu Ahabu anakwiya tsiku lina?
 • Kodi Yezebeli akuchita chiyani kuti atenge munda wamphesa wa Naboti n’kuupereka kwa mwamuna wake, Ahabu?
 • Kodi Yehova akutumiza ndani kukalanga Yezebeli?
 • Monga momwe mukuonera pachithunzipa, kodi chikuchitika n’chiyani Yehu atafika kunyumba yachifumu ya Yezebeli?

Mafunso ena

 • Ŵerengani 1 Mafumu 16:29-33 ndi 18:3, 4.

  Kodi zinthu zinaipa motani ku Israyeli mu nthaŵi ya Mfumu Ahabu? (1 Maf. 14:9)

 • Ŵerengani 1 Mafumu 21:1-16.

  Kodi Naboti anasonyeza bwanji kulimba mtima ndi kukhulupirika kwa Yehova? (1 Maf. 21:1-3; Lev. 25:23-28)

  Kuchokera ku chitsanzo cha Ahabu, kodi tingaphunzirenji za zimene tingachite tikakhumudwitsidwa? (1 Maf. 21:4; Aroma 5:3-5)

 • Ŵerengani 2 Mafumu 9:30-37.

  Kodi tingaphunzirenji kuchokera ku changu cha Yehu pochita chifuniro cha Yehova? (2 Maf. 9:4-10; 2 Akor. 9:1, 2; 2 Tim. 4:2)

Onaninso

ZOTI MUCHITE POPHUNZIRA BAIBULO

Mulungu Amadana ndi Zinthu Zopanda Chilungamo

Koperani nkhaniyi ndipo muone zimene mungaphunzire pa nkhani yokhudza Ahabu, Yezebeli, Naboti ndi Eliya.