Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 64: Solomo Amanga Kachisi

Nkhani 64: Solomo Amanga Kachisi

DAVIDE asanafe, anapatsa Solomo malinganizidwe a kamangidwe ochokera kwa Mulungu a kachisi wa Yehova. M’chaka chachinai cha ulamuliro wake, iye akuyamba kumanga kachisi’yo, ndipo kukutenga zaka zisanu ndi ziwiri kum’maliza. Amuna zikwi makumi ochuluka akugwira ntchito pa kachisi, ndipo nyumba’yo ikudya ndalama zochuluka kwambiri. Izi ziri choncho chifukwa chakuti golidi ndi siliva zochuluka zikugwiritsiridwapo ntchito.

Kachisi’yo ali ndi zipinda zazikulu ziwiri, monga momwe chinaliri chihema. Koma zipinda’zi ziri zowirikiza ukulu wa za chihema. Solomo akuchititsa likasa la chipangano kuikidwa m’chipinda cha m’kati-kati, ndipo zinthu zina zimene zinalikusungidwa m’chihema zikuikidwa m’china’cho.

Pamene kachisi’yo atha, pali madyerero akulu. Solomo akugwada patsogolo pa kachisi’yo napemphera, monga momwe mukuonera m’chithunzi’chi. ‘Ngakhale kumwamba kweni-kweni’ko simungakwane’ko,’ akutero Solomo kwa Yehova, ‘koposa kotani nanga, kachisi uyu. Koma, O Mulungu wanga, chonde mverani anthu anu popemphera ataloza ku malo kuno.’

Mfumu Solomo ikupemphera

Pamene atsiriza pemphero lake, ukutsika moto kuchokera kumwamba. Ukuocha nyama za nsembe’zo. Ndipo kuunika kowala kochokera kwa Yehova kukudzaza kachisi’yo. Izi zikusonyeza kuti Yehova akumvetsera, n’kuti akukondwera naye kachisi’yo ndi pemphero la Solomo. Kachisi’yo, m’malo mwa chihema, tsopano akukhala malo kumene anthu’wo akudza kudzalambira.

Kwa nthawi yaitali Solomo akulamulira mwanzeru, ndipo anthu nakhala achimwemwe. Koma Solomo akukwatira akazi ambiri a ku maiko ena osalambira Yehova. Kodi mukuona mmodzi wa iwo akulambira fano? Potsiriza akazi ake akupangitsa Solomo naye’nso kulambira milungu ina. Kodi mukudziwa chimene chikuchitika pamene Solomo achita izi? Iye sakuchitira’nso anthu’wo mokomo mtima. Iye akukhala wankhanza, ndipo anthu’wo sali’nso achimwemwe.

Mfumu Solomo ikulambira fano

Izi zikukwiyitsa Yehova, ndipo akumuuza kuti: ‘Ndidzakuchotsera ufumu ndi kuupatsa kwa munthu wina. Sindidzachita izi m’nthawi ya moyo wako, koma m’kulamulira kwa mwanako. Koma sindidzachotsa anthu onse a ufumu’wo kwa mwanako. Tiyeni tione m’mene zikuchitikira.

1 Mbiri 28:9-21; 29:1-9; 1 Mafumu 5:1-18; 2 Mbiri 6:12-42; 7:1-5; 1 Mafumu 11:9-13.Mafunso

 • Kodi zikutenga nthaŵi yaitali motani kuti Solomo amalize kumanga kachisi wa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani kachisiyo akudya ndalama zochuluka kwambiri?
 • Kodi m’kachisimo muli zipinda zazikulu zingati, ndipo m’chipinda cham’katikati akuikamo chiyani?
 • Kodi Solomo akunena chiyani m’pemphero lake pamene kachisiyo watha kumangidwa?
 • Kodi Yehova akusonyeza bwanji kuti wakondwera ndi pemphero la Solomo?
 • Kodi akazi a Solomo akumupangitsa kuchita chiyani, ndipo n’chiyani chikuchitikira Solomo?
 • N’chifukwa chiyani Yehova wakwiyira Solomo, ndipo kodi Yehova akunena chiyani kwa iye?

Mafunso ena

 • Ŵerengani 1 Mbiri 28:9, 10.

  Mogwirizana ndi mawu a Davide olembedwa pa 1 Mbiri 28:9, 10, kodi tiyenera kuyesetsa kuchita chiyani tsiku lililonse pamoyo wathu? (Sal. 19:14; Afil. 4:8, 9)

 • Ŵerengani 2 Mbiri 6:12-21, 32-42.

  Kodi Solomo anasonyeza bwanji kuti palibe nyumba yomangidwa ndi anthu imene Mulungu Wam’mwambamwamba angakhalemo? (2 Mbiri 6:18; Mac. 17:24, 25)

  Kodi mawu a Solomo opezeka pa 2 Mbiri 6:32, 33 amasonyeza chiyani za Yehova? (Mac. 10:34, 35; Agal. 2:6)

 • Ŵerengani 2 Mbiri 7:1-5.

  Mofanana ndi mmene ana a Israyeli anakhudzidwira mumtima n’kunena mawu olemekeza Yehova ataona ulemerero wake, kodi nafenso masiku ano tiyenera kukhudzidwa motani tikaganizira mmene Yehova wadalitsira anthu ake? (2 Mbiri 7:3; Sal. 22:22; 34:1; 96:2)

 • Ŵerengani 1 Mafumu 11:9-13.

  Kodi moyo wa Solomo umasonyeza bwanji kufunika kokhala wokhulupirika mpaka mapeto? (1 Maf. 11:49; Mat. 10:22; Chiv. 2:10)