Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 61: Davide Akulongedwa Ufumu

Nkhani 61: Davide Akulongedwa Ufumu

SAULI akuyesa’nso kugwira Davide. Akutenga ankhondo ake amphamvu 3,000 namka kukasa-saka Davide. Iye atamva za izi, iye akutumiza azondi kukaona kumene Sauli ndi ankhondo ake agona usiku’wo. Ndiyeno iye akufunsa awiri a amuna ake’wo kuti: ‘Ndani adzafuna kumka nane ku msasa wa Sauli?’

Davide akuitana Mfumu Sauli

‘Ine,’ Akutero Abisai. Abisai ndi mwana wa mlongo wa Davide Zeruya. Sauli ndi anthu ake ali mtulo, Davide ndi Abisai akulowa mu msasa’wo mwakachetechete. Akutenga mkondo wa Sauli ndi mtsuko wa madzi, umene uli kumutu kwa Sauli. Palibe woona kapena kumva chifukwa iwo onse ali mtulo tatikulu.

Onani Davide ndi Abisai tsopano. Achokapo, afika bwino lomwe pa phiri. Davide akuitana mkulu wankhondo wa Israyeli mopfuula: ‘Abineri, n’chifukwa ninji sukutetezera mbuyako, mfumu? Tayang’ana! Ziri kuti mkondo ndi mtsuko wa madzi za mfumu?’

Sauli akudzambatuka. Akuzindikira mau a Davide, nafunsa kuti: ‘Kodi ndiwe Davide?’ Kodi mukuona Sauli ndi Abineri apo?

‘Inde, mbuyanga mfumu,’ Davide akuyankha Sauli. Nafunsa kuti: ‘Kodi n’cifukwa ninji mukuyesa kundigwira? Kodi ndachita choipa chotani? Nawu mkondo wanu, O mfumu. Tumani mmodzi wa amuna anu adzautenge.’

Mfumu Sauli ndi Abineri

Sauli akubvomereza kuti, ‘Ndalakwa. Ndachita mopusa.’ Zitatero Davide akuchoka, Sauli nabwerera kwao. Koma Davide akuti mu mtima mwake: ‘Tsiku lina Sauli’yu adzandipha. Ndiyenera kuthawira ku dziko la Afilisti.’ Ndipo anatero’di. Iye akuputsitsa Afilisti n’kuwachititsa kukhulupirira kuti ali ku mbali yao tsopano.

Nthawi ina pambuyo pake Afilisti akumka kukamenyana ndi Israyeli. M’nkhondo, Sauli ndi Jonatani yemwe akuphedwa. Izi zikumvetsa chisoni kwambiri Davide, ndipo akulemba nyimbo yokoma, m’mene iye akuyimba kuti: ‘Ndimva chisoni chifukwa cha iwe, mbale wanga Jonatani. Unalitu wokondedwa kwa ine!’

Pambuyo pake Davide akubwerera ku Israyeli ku mzinda wa Hebroni. Pali nkhondo pakati pa anthu osankha mwana wa Sauli Isiboseti kukhala mfumu ndi anthu ena ofuna Davide kukhala mfumu. Koma potsiriza amuna a Davide akupambana. Davide ali ndi zaka 30 pamene akulongedwa ufumu. Kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi theka iye akulamulira Hebroni. Ena a obadwira kumene’ko akuchedwa Amnoni, Abisalomu ndi Adoniya.

Nthawi ikufika pamene Davide ndi ankhondo ake akumka kukalanda mzinda wokongola wochedwa Yerusalemu. Yoabu, mwana wina wa mlongo wa Davide Zeruya, akutsogolera nkhondo’yo. Chotero Davide akufupa Yoabu mwa kum’panga kukhala mkulu wa gulu lake la nkhondo. Tsopano Davide akuyamba kulamulira mu mzinda wa Yerusalemu.

1 Samueli 26:1-25; 27:1-7; 31:1-6; 2 Samueli 1:26; 3:1-21; 5:1-10; 1 Mbiri 11:1-9.Mafunso

 • Kodi Davide ndi Abisai anachita chiyani pamene Sauli anali kugona mu msasa wake?
 • Kodi Davide akufunsa Sauli mafunso otani?
 • Atasiyana ndi Sauli, kodi Davide akupita kuti?
 • Kodi n’chiyani chikumvetsa chisoni kwambiri Davide, moti mpaka analemba nyimbo yokoma?
 • Kodi Davide ali ndi zaka zingati pamene akulongedwa ufumu ku Hebroni, ndipo ana ake ena mayina awo ndi ndani?
 • Kodi kenaka Davide akulamuliranso kuti monga mfumu?

Mafunso ena

 • Ŵerengani 1 Samueli 26:1-25.

  Mawu a Davide omwe analembedwa pa 1 Samueli 26:11 akusonyeza kuti anali ndi maganizo otani okhudza kakonzedwe ka zinthu ka Mulungu? (Sal. 37:7; Aroma 13:2)

  Ngati tayesetsa kusonyeza kukoma mtima kwachikondi kwa munthu wina, koma munthu amene tamusonyeza zimenezoyo sakuyamikira zimene tachitazo, kodi mawu a Davide opezeka pa 1 Samueli 26:23 angatithandize bwanji kukhalabe ndi maganizo oyenera? (1 Maf. 8:32; Sal. 18:20)

 • Ŵerengani 2 Samueli 1:26

  Kodi Akristu masiku ano angakhale bwanji ndi “chikondano chenicheni” ngati chimene Davide ndi Jonatani anali nacho? (1 Pet. 4:8; Akol. 3:14; 1 Yoh. 4:12)

 • Ŵerengani 2 Samueli 5:1-10.

  Kodi Davide anakhala mfumu kwa zaka zingati, ndipo zaka zimenezi zinagaŵidwa bwanji? (2 Sam. 5:4, 5)

  Kodi Davide anatchuka chifukwa chiyani, ndipo kodi zimenezi zimatikumbutsa chiyani ifeyo masiku ano? (2 Sam. 5:10; 1 Sam. 16:13; 1 Akor. 1:31; Afil. 4:13)

Onaninso

PHUNZITSANI ANA ANU

Davide Sankachita Mantha

Werengani nkhaniyi m’Baibulo kuti mudziwe zimene zinamuthandiza Davide kuti akhale wolimba mtima.

KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

Aisiraeli Anapempha Kuti Akhale ndi Mfumu

Mulungu anasankha Sauli kuti akhale mfumu Aisiraeli atapempha kuti akhale ndi mfumu. N’chifukwa chiyani Mulungu anachotsa Sauli n’kuika Davide kuti akhale mfumu?