Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 59: Chifukwa chake Davide Akuthawa

Nkhani 59: Chifukwa chake Davide Akuthawa

DAVIDE atapha Goliati, mkulu wankhondo wa Israyeli Abineri akumka naye kwa Sauli. Sauli ali wokondwera kwambiri ndi Davide. Akum’panga kukhala mkulu m’gulu lake la nkhondo nam’tengera ku nyumba ya mfumu.

Kenako, pobwera ku nkhondo komenyana ndi Afilisti, akazi akuyimba kuti: ‘Sauli anapha zikwi zochuluka, koma Davide zikwi makumi ambiri.’ Izi zikuchititsa nsanje Sauli, chifukwa Davide akupatsidwa ulemu waukulu koposa iye. Mwana wake Jonatani sali ndi nsanje. Akukonda kwambiri Davide, naye’nso Davide akum’konda. Chotero awiri’wa akupangana pangano la kukhala mabwenzi nthawi zonse.

Mfumu Sauli akuponya mkondo

Davide ngwoimba bwino kwambiri zeze, ndipo Sauli amakonda nyimbo zake. Koma tsiku lina nsanje ya Sauli ikum’chititsa kuchita chinthu choopsya. Davide akuyimba zeze, Sauli akutenga mkondo wake nauponya, nati: ‘Ndidzam’pyoza kum’phatikiza ndi khoma!’ Koma iye akulewa, ndipo mkondo’wo ukulasa padera. Kenako Sauli akuphonya Davide ndi mkondo wake kachiwiri. Tsono Davide akudziwa kuti ayenera kukhala wosamala.

Kodi mukukumbukira lonjezo limene Sauli anapanga? Iye anati akapatsa mwana wake wamkazi kwa munthu amene akapha Goliati. Sauli potsiriza akuuza Davide kuti angatenge mwana wake Mikala, koma choyamba akaphe adani Achifilisti 100. Tazilingalirani! Sauli akulingalira kweni-kweni kuti iwo adzapha Davide. Koma sakutero, chotero akupereka mwana wake wamkazi kukhala mkazi wa Davide.

Tsiku lina Sauli akuuza Jonatani ndi atumiki ake onse kuti akufuna kupha Davide. Koma Jonatani akuti: ‘Musabvulaze Davide. Sanachite choipa chiri chonse kwa inu. M’malo mwake, chiri chonse chimene wachita chakhala chothandiza kwa inu. Iye anaika moyo wake pangozi pamene anapha Goliati, ndipo pochiona, munakondwera.’

Davide akuzinda mkondo

Sauli akumvera mwana wake, nalonjeza kusam’bvulaza. Davide akubwezeredwamo, natumikira Sauli m’nyumba mwake monga kale. Komabe, tsiku lina, Davide akuyimba nyimbo, Sauli akuponya’nso mkondo wake kwa Davide. Iye akuulewa, mkondo’wo nulasa khoma. N’kachitatu aka! Davide akudziwa kuti ayenera kuthawa tsopano!

Usiku womwewo akumka ku nyumba yake. Koma Sauli akutuma anthu kukam’pha. Mikala akudziwa zimene atate wake walinganiza kuchita. Chotero akuuza mwamuna wake kuti: ‘Ngati suchoka usiku uno, udzakhala utafa m’mawa.’ Usiku’wo Mikala akuthandiza Davide kutulukira pa zenera. Kwa zaka zisanu ndi ziwiri Davide ayenera kubisala m’malo osiyana-siyana kuti Sauli asam’peze.

1 Samueli 18:1-30; 19:1-18.Mafunso

  • N’chifukwa chiyani Sauli akuchitira nsanje Davide, koma kodi mwana wa Sauli, Jonatani, ndi wosiyana bwanji ndi Sauli?
  • Kodi chikuchitika n’chiyani tsiku lina pamene Davide akuyimbira Sauli zeze?
  • Kodi Sauli akunena kuti Davide ayenera kuchita chiyani asanam’patse mwana wake wamkazi Mikala kuti akhale mkazi wake, ndipo n’chifukwa chiyani Sauli akunena zimenezi?
  • Pamene Davide akuyimbira Sauli zeze, kodi n’chiyani chikuchitika kachitatu, monga momwe chithunzichi chikusonyezera?
  • Kodi Mikala akuthandiza bwanji kupulumutsa Davide, ndipo kwa zaka zisanu ndi ziŵiri Davide ayenera kuchita chiyani?

Mafunso ena