AFILISTI akudza’nso kudzamenyana ndi Israyeli. Abale atatu akulu a Davide tsopano ali m’gulu lankondo la Sauli. Tsiku lina Jese akuuza Davide kuti: ‘Tengera abale ako tirigu ndi mitanda ya mkate. Kaone m’mene iwo aliri.’

Goliyati

Pofika Davide pa msasa wa magulu ankhondo’wo, akuthamangira ku malo omenyanira kukafuna-funa abale ake. Chimphona Chachifilisti’cho Goliati chikutuluka kudzanyoza Aisrayeli. Chakhala chikuchita izi m’mawa ndi madziulo uli wonse kwa masiku 40. Iye akupfuula kuti: ‘Sankhani mmodzi wa pakati panu kubwera kudzamenyana nane. Ngati apambana nadipha, tidzakhala akapolo anu. Koma ndikapambana nandimupha, mudzakhala akapolo athu. Ndikukutokosani kusankha wina woti ndidzamenyane naye.’

Davide akufunsa mmodzi wa asilikali ankhondo’wo kuti: ‘Kodi wopha Mfilisti’yu nalanditsa Israyeli adzapezanji?’

‘Sauli adzapatsa munthu’yo chuma chochuluka,’ anatero msilikari’yo. ‘Ndipo adzam’patsa mwana wake wamkazi akhale mkazi wake.’

Koma Aisrayeli onse akuopa Goliati chifukwa chakuti iye n’chimphona. Iye ali woposa mapazi 9 pafupi-fupi mamita 3 kutali kwake, ndipo ali ndi msilikari wina wom’nyamulira chishyango.

Asilikari ena akumka nauza Mfumu Sauli kuti Davide akufuna kumenyana ndi Goliati. Koma Sauli akuuza Davide kuti: ‘Sungamenyane ndi Mfilisti uyu. Iwe ndiwe mnyamata chabe, iye wakahala wankhondo kwa moyo wake wonse.’ Davide akuyankha kuti: ‘Ndinapha chimbalangondo ndi mkango zimene zinatenga nkhosa ya atate wanga. Ndipo Mfilisti uyu adzakhala ngati izo. Yehova adzandithandiza.’ Chotero Sauli akuti: ‘Muka, ndipo Yehova akhale nawetu.’

Davide akumka ku mtsinje ndi kupeza miyala yosalala isanu, naiika m’thumba lake. Ndiyeno akutenga legeni yake namuka kukakumana ndi chimphona’cho. Goliati pomuona, sakuzikhulupirira. Akuganiza kuti kukakhala kosabvuta kupha Davide.

Davide akuponya mwala

‘Idza kuno uone,’ akutero Goliati, ‘ndipo ndidzapereka mtembo wako kwa mbalame ndi zinyama ziudye.’ Koma Davide akuti: ‘Iwe ukudza kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikudza kwa iwe m’dzina la Yehova. Lero Yehova adzakupereka m’dzanja langa ndipo ndidzakugwetsa pansi.’

Atatero Davide akuthamangira kuli Goliati. Akutulutsa mwala m’thumba lake, akuuika m’legeni yake, ndipo akuuponya ndi mphamvu yake yonse. Mwala’wo ukuyenda mwachindunji kulowa m’mutu wa Goliati, ndipo akugwa pansi atafa! Afilisti poona kuti ngwazi yao yafa, onse akutembenuka nathawa. Aisrayeli akuwathamangitsa napambana nkhondo’yo.

1 Samueli 17:1-54.Mafunso

  • Kodi Goliati akuputa gulu lankhondo la Aisrayeli kuti lichite chiyani?
  • Kodi Goliati ndi wamkulu bwanji, ndipo kodi Mfumu Sauli ikulonjeza kuti idzapereka mphoto yotani kwa munthu amene aphe Goliati?
  • Kodi Davide akuuza Sauli chiyani atamuuza kuti sangathe kumenyana ndi Goliati chifukwa chakuti Davideyo ndi mnyamata wamng’ono?
  • Kodi mmene Davide akuyankhira Goliati zikusonyeza bwanji kuti akudalira Yehova?
  • Monga momwe mukuonera pachithunzipa, kodi Davide anagwiritsira ntchito chiyani kupha Goliati, ndipo chikuchitika n’chiyani kwa Afilistiwo pambuyo pa zimenezi?

Mafunso ena