Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani 56: Sauli—Mfumu Yoyamba

Nkhani 56: Sauli—Mfumu Yoyamba
Samueli akudzoza Sauli ufumu

ONANI Samueli akutsanulira mafuta pamutu pa munthu’yo. Izi ndizo zimene analinkuchitira munthu kusonyeza kuti wasankhidwa kukhala mfumu. Yehova akuuza Samueli kutsanulira mafuta pamutu pa Sauli. Ndiwo mafuta onunkhira bwino apadera.

Sauli sanalingalire kuti anali woyenerera kwambiri kukhala mfumu. ‘Ndine wa pfuko la Benjamini, laling’ono kopambana mwa Israyeli,’ iye akuuza choncho Samueli. ‘Kodi mukuneneranji kuti ndidzakhala mfumu?’ Yehova akukonda Sauli chifukwa chakuti sakudziyerekezera kukhala wamkulu ndi wofunika. Ndicho chifukwa chake Iye akum’sankha kukhala mfumu.

Koma Sauli si munthu wosauka kapena wamng’ono. Iye ngwa m’banja lolemera, ndipo ngwokongola, wamtali. Iye ndi wamtali kuposa ali yense mu Israyeli ndi phazi limodzi! Iye ndi wothamanga kwambiri, ndipo ndi munthu wamphamvu. Anthu’wo ali okondwa kuti Yehova wasankha Sauli kukhala mfumu. Onse akuyamba kupfuula kuti: ‘Ikhale ndi moyo wautali mfumu’yo!’

Adani a Israyeli akali amphamvube. Iwo akuchititsirabe Aisrayeli bvuto. Posakhalitsa Sauli atapangidwa kukhala mfumu, Aamoni akudza kudzamenyana nawo. Koma Sauli akusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu, ndipo akulaka Aamoni. Izi zikusangalatsa anthu’wo kuti Sauli wakhala mfumu.

M’kupita kwa zaka, Sauli akutsogolera Aisrayeli ku zipambano zambiri za adani ao. Iye ali’nso ndi mwana wolimba mtima wochedwa Jonatani. Jonatani akuthandiza Israyeli kupambana nkhondo zambiri. Afilisti akali chikhalirebe adani oipa kwambiri a Israyeli. Tsiku lina Afilisti zikwi zikwi akudza kudzamenyana ndi Aisrayeli.

Samueli akuuza Sauli kuyembekezera kufikira iye atadza kudzapereka nsembe kwa Yehova. Koma Samueli wachedwa kudza. Sauli akuopa kuti Afilisti adzayamba nkhondo, chotero iye mwini akupereka yekha nsembe. Pamene Samueli potsirizira pake afika, akuuza Sauli kuti iye wakhala wosamvera. ‘Yehova adzasankha munthu wina kukhala mfumu pa Israyeli,’ akutero Samueli.

Kenako Sauli sakumvera’nso. Samueli akumuuza kuti: ‘N’kwabwino kwambiri kumvera Yehova koposa kum’patsa nsembe ya nkhosa yabwino kopambana. Chifukwa chakuti sunamvere Yehova, Yehova sadzalola kuti ukhalebe mfumu ya Israyeli.’

Tingaphunziremo phunziro labwino. Zimatisonyeza m’mene kuliri kofunika kumvera Yehova nthawi zonse. Ndipo’nso, zimasonyeza kuti munthu wabwino, wonga ngati Sauli, angasinthe n’kukhala woipa. Ife sitimafuna konse kukhala oipa, kodi si choncho?

1 Samueli chaputala 9 mpaka 11; 13:5-14; 14:47-52; 15:1-35; 2 Samueli 1:23.Mafunso

  • Pachithunzipa, kodi Samueli akuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani akuchita zimenezi?
  • N’chifukwa chiyani Yehova amakonda Sauli, ndipo kodi iye ndi munthu wotani?
  • Kodi mwana wa Sauli dzina lake ndani, ndipo kodi mwanayo akuchita chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Sauli akupereka nsembe m’malo modikira Samueli kuti adzachite zimenezi?
  • Kodi tingaphunzire maphunziro otani pa nkhani ya Sauli?

Mafunso ena