KODI aka si kamnyamata kokongola? Dzina lake ndi Samueli. Ndipo munthu amene wagwira pamutu pa Samueli’yo ndiye mkulu wa ansembe wa Israyeli Eli. Uyo ndi atate wa Samueli Elikana ndi mai wake Hana amene akupereka Samueli kwa Eli.

Samueli akukumana ndi mkulu wa ansembe Eli

Samueli ali ndi zaka pafupi-fupi zinai kapena zisanu zokha. Koma adzakhala pano pa chihema cha Yehova ndi Eli ndi ansembe ena. Kodi n’chifukwa ninji Elikana ndi Hana akupereka mwana wamng’ono ngati Samueli’yu kutumikira Yehova pa chihema? Tiyeni tione.

N’zaka zowerengeka chabe izi zisanachitike pamene Hana anali wachisoni kwambiri. Chifukwa chake n’chakuti anali wosabala, ndipo anafuna mwana kwambiri. Chotero tsiku lina Hana atakacheza ku chihema cha Yehova, akupemphera kuti: ‘O, Yehova musandiiwaletu! Mukandipatsa mwana wamwamuna, ndikulonjeza kuti ndidzam’pereka kwa inu kuti akutumikireni kwa moyo wake wonse.’

Yehova anayankha pemphero la Hana, pambuyo pa miyezi ingapo iye akubala Samueli. Hana anakonda kamnyamata kake’ko, ndipo anayamba kum’phunzitsa za Yehova akali wamng’ono kwambiri. Iye anauza mwamuna wake kuti: ‘Samueli akangosinkhuka kwakuti sakufunikira’nso kuyamwa, ndidzamka naye ku chihema kukatumikira Yehova kumene’ko.’

Ndizo zimene tikuona Hana ndi Elikana akuchita m’chithunzi’chi. Ndipo chifukwa chakuti Samueli waphunzitsidwa bwino kwambiri ndi makolo ake, ali wokondwa kutumikira Yehova pano pa chihema cha Yehova. Chaka ndi chaka Hana ndi Elikana amadza kudzalambira pa chihema chapadera’chi, ndi kudzazonda kamnyamata kao. Ndipo chaka chiri chonse Hana akudza ndi malaya atsopano opanda mikono amene iye wasokera Samueli.

M’kupita kwa zaka, Samueli akutumikirabe Yehova pa chihema, ndipo Yehova ndi anthu omwe akum’konda. Koma ana a mkulu wansembe Eli Hofeni ndi Pinehasi si abwino. Iwo akuchita zoipa zambiri, ndi kuchititsa ena’nso kusamvera Yehova. Eli ayenera kuwachotsa pa kukhala ansembe, koma sakutero.

Mwana’yo Samueli sakulola chiri chonse cha zoipa zochitika pa chihema kum’chititsa kuleka kutumikira Yehova. Koma chifukwa chakuti anthu owerengeka kwambiri akukonda’di Yehova, papita nthawi yaitali chiyambire pamene Yehova walankhuka ndi munthu ali yense. Pamene Samueli akusinkhukirapo pang’ono nazi zimene zikuchitika:

Samueli ali mtulo m’chihema chokumanako’cho pamene mau akum’dzutsa. Iye akuyankha: ‘Ndiri pano.’ Akudzuka ndi kuthamangira kwa Eli, n’kuti: ‘Mwandiitana, ndipo ndabwera.’

Koma Eli akuyankha kuti: ‘Sindinakuitane; bwerera kagone.’ Chotero Samueli akubwerera kukagona.

Kenako pali kuitana’nso: ‘Samueli!’ Chotero Samueli akudzambatuka ndi kuthamangira kwa Eli. ‘Mwandiitana, ndipo ndabwera,’ akutero. Koma Eli akuyankha kuti: ‘Sindinaitane, mwana wanga. Gona’nso.’ Chotero Samueli akubwerera’nso kukagona.

‘Samuel!’ mau’wo akuitana kachitatu. Chotero Samueli akuthamangira kwa Eli. ‘Ndabwera, pakuti muyenera kukhala mutandiitana pa nthawi ino,’ akutero. Eli akudziwa tsopano, kuti ayenera kukhala Yehova amene akuitana. Chotero akuuza Samueli kuti: ‘Kagone’nso, ndipo ngati aitana’nso, unene kuti: “Nenani, Yehova, pakuti mtumiki wanu akumva.”’

Izi ndizo zimene Samueli akunena pamene Yehova akuitana’nso. Pamenepo Yehova akuuza Samueli kuti akalanga Eli ndi ana ake. Kenako Hofeni ndi Pinehasi akufa m’nkhondo yomenyana ndi Afilisti, ndipo pakumva izi Eli akugwa chagada, nathyola khosi lake nafa. Chotero mau a Yehova anakwaniritsidwa.

Samueli akukula nakhala woweruza wotsiriza wa Israyeli. Atakalamba anthu’wo akum’pempha kuti: ‘Tisankhireni mfumu yotilamulira.’ Samueli sakufuna kuchita izi, chifukwa kweni-kweni Yehova ndiye mfumu yao. Koma Yehova akumuuza kumvera anthu’wo.

1 Samueli 1:1-28; 2:11-36; 4:16-18; 8:4-9.Mafunso

  • Kodi kamnyamata kamene kali pachithunzipa dzina lake ndani, ndipo anthu enawo ndi ndani?
  • Kodi Hana anapemphera motani tsiku lina atapita ku chihema cha Yehova, ndipo kodi Yehova anamuyankha motani?
  • Kodi Samueli ali ndi zaka zingati pamene akutengedwa kukatumikira pa chihema cha Yehova, ndipo kodi mayi ake akumuchitira chiyani chaka chilichonse?
  • Kodi ana a Eli mayina awo ndi ndani, ndipo kodi ndi anthu otani?
  • Kodi Yehova akuitana Samueli motani, ndipo akumupatsa uthenga wotani?
  • Kodi Samueli akukhala ndani atakula, ndipo chikuchitika n’chiyani atakalamba?

Mafunso ena