KODI mukudziwa dzina la munthu wamphamvu kopambana onse? Ndiye woweruza wochedwa Samsoni. Ndiye Yehova amene akupatsa Samsoni nyonga yake. Ngakhale Samsoni asanabadwe, Yehova akuuza amake kuti: ‘Posachedwa udzabala mwana wamwamuna. Adzatsogolera m’kulanditsa Israyeli kwa Afilisti.’

Samisoni akulimbana ndi mkango

Afilisti ndi anthu oipa okhala m’Kanani. Ali ndi ankhondo ambiri, ndipo akukantha Aisrayeli. Pa nthawi ina, Samsoni ali pa ulendo womka kumene Afilisti amakhala, chimkango chikudza kwa iye chikuthuluma. Koma iye akupha mkango’wo ndi manja opanda kanthu. Iye akupha’nso Afilisti mazana ochuluka.

Kenako iye akukondana ndi mkazi wochedwa Delila. Afilisti akulonjeza atsogoleri kuti ali yense wa iwo adzapatsa Delila ndalama za siliva 1,100 ngati awauza chimene chimapatsa nyonga Samsoni. Delila akufuna ndalama’zo. Sali bwenzi leni-leni la Samsoni, kapena wa anthu a Mulungu. Chotero akufunsa-funsabe Samsoni chimene chimam’patsa nyonga.

Delila ndi Samisoni

Potsiriza, Delila akuchititsa Samsoni kumuuza chinsinsi’cho. Iye akuti ‘Tsitsi langa silinametedwe chiyambire.’ Kuyambira pa nthawi imene ndinabadwa, Mulungu anandisankha kukhala mtumiki wake wapadera wochedwa Mnaziri. Ngati nditametedwa tsitsi langa, ndikakhala wopanda nyonga.’

Eya, Delila atamva izi, akugoneka Samsoni pa nchafu pake. Ndiyeno n’kuitana munthu kudzam’meta. Pouka Samsoni, alibe’nso nyonga. Afilisti akudzano nam’gwira. Akum’kolowola maso onse nam’panga kukhala kapolo wao.

Samisoni akugwetsa zipilala

Tsiku lina Afilisti ali ndi phwando lalikulu kulambira mulungu wao Dagoni, ndipo akutulutsa Samsoni m’ndende kudzam’panga kukhala chowaseketsa. Pa nthawi’yi, tsitsi la Samsoni lamera’nso. Iye akuuza mnyamata wom’gwira dzanja kuti: ‘Ndigwiritse mizati ya nyumba’yi.’ Napempherano kwa Yehova kuti am’patse nyonga, ndipo akugwira mizati’yo. Napfuula kuti: ‘Ndife nawotu Afilisti’wa.’ Pali Afilisti 3,000 pa phwandopo, ndipo pamene akukankha mizati’yo nyumba’yo ikugwa ndi kupha anthu onse oipa’wo.

Oweruza chaputala 13 mpaka 16.Mafunso

  • Kodi munthu wamphamvu kopambana onse dzina lake ndi ndani, ndipo ndani anamupatsa mphamvu zimenezo?
  • Panthaŵi ina, kodi Samsoni akuchita chiyani kwa mkango waukulu, monga momwe mukuonera pachithunzipa?
  • Kodi pachithunzipa Samsoni akuuza Delila chinsinsi chotani, ndipo zimenezi zinachititsa bwanji kuti Afilisti am’gwire?
  • Kodi Samsoni akuchititsa bwanji kuti adani ake achifilisti 3,000 afe patsiku limene iye anafa?

Mafunso ena