Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 52: Gideoni ndi Amuna Ake 300

Nkhani 52: Gideoni ndi Amuna Ake 300

KODI mukuona zimene zikuchitika pano? Onsewa ndi amuna ankhondo a Israyeli. Amuna owerama’wo akumwa madzi. Woweruza Gideoni ndiye uyo waima pafupi nawo. Iye akuyang’ana m’mene akumwera madzi.

Yang’anitsitsani kusiyana kwa m’mene akumwera. Ena akuweramira m’madzi mweni-mwenimo. Koma mmodzi akutunga madzi’wo ndi manja, kotero kuti adziona zimene zikuchitika mom’zungulira. Izi n’zofunika, pakuti Yehova anauza Gideoni kusankha amuna okha amene akupenyetsetsa pamene akumwa. Gideoni akunena kuti otsala’wo ayenera kubwezeredwa kunyumba. Tiyeni tione chifukwa chake.

Aisrayeli ali m’bvuto lalikulu kachiwiri’nso. Chifukwa chake n’chakuti sanamvere Yehova. Amidyani akuwaposa mphamvu ndipo akuwapweteka. Chotero Aisrayeli akupfuulira kwa Yehova kaamba ka chithandizo, ndipo Yehova akumva mfuu zao.

Yehova akuuza Gideoni kusonkhanitsa ankhondo, chotero Gideoni akusonkhanitsa amuna ankhondo 32,000. Koma pali gulu lankondo la amuna 135,000 lomenyana ndi Israyeli. Ndipo komabe Yehova akuuza Gideoni kuti: ‘Uli ndi amuna ochulukitsitsa.’ Kodi Yehova ananeneranji zimene’zo?

N’chifukwa chakuti ngati Israyeli atapambana nkhondo’yo, iwo angaganize kuti iwo apambana mwa iwo okha. Iwo angaganize kuti sanafunikire chithandizo cha Yehova kuti apambane. Chotero Yehova akuti kwa Gideoni: ‘Uza amuna onse amantha kubwerera kwao.’ Pamene Gideoni akuchita izi, 22,000 anabwerera kwao. Zimene’zo zikum’siyira amuna ankhondo 10,000 okha okalimbana ndi asilikari ankhondo 135,000 onse’wo.

Gideoni akuyesa asilikali ake

Koma, imvani! Yehova akuti: ‘Ukali ndi ochulukitsitsabe.’ Chotero akuuza Gideoni kuchititsa amuna’wo kumwa madzi pa mtsinje’wu ndi kubwezera kunyumba anthu onse amene akuika nkhope zao pansi pomwa madzi’wo. ‘Ndidzakupatsa chipambano ndi amuna 300 amene anali openyetsetsa pakumwa,’ akulonjeza motero Yehova.

Nthawi ya nkhondo’yo ikukwana. Gideoni akugawa amuna ake 300 kukhala magulu atatu. Iye akupatsa mwamuna ali yense lipenga, ndi mtsuko wokhala ndi nyali m’kati mwake. Pofika pakati pa usiku, iwo onse akusonkhana mozinga msasa wa adani’wo. Ndiyeno. pa nthawi imodzi-modzi’yo, iwo onse akuomba malipenga ao ndi kuswa mitsuko yao, napfuula kuti: ‘Lupanga la Yehova ndi la Gideoni!’ Pouka ankhondo audani’wo, iwo asokonezeka maganizo ndipo akuopa. Onse akuyamba kuthawa, Aisrayeli napambana nkhondo’yo.

Oweruza chaputala 6 mpaka 8.Mafunso

 • N’chifukwa chiyani Aisrayeli ali m’vuto lalikulu, ndipo ali m’vuto lotani?
 • N’chifukwa chiyani Yehova akuuza Gideoni kuti ali ndi amuna ankhondo ochulukitsitsa?
 • Kodi ndi amuna angati amene akutsala Gideoni atauza amuna amantha kuti abwerere kwawo?
 • Kuchokera pa chithunzichi, fotokozani mmene Yehova akuchepetsera amuna ankhondo a Gideoni kufika pa amuna 300 okha basi.
 • Kodi Gideoni akukonzekeretsa bwanji amuna ake 300, ndipo kodi Aisrayeli akupambana bwanji nkhondoyo?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Oweruza 6:36-40.

  Kodi Gideoni anachita chiyani kuti atsimikizire zimene Yehova anali kufuna?

  Kodi ifeyo masiku ano timadziŵa bwanji zimene Yehova akufuna? (Miy. 2:3-6; Mat. 7:7-11; 2 Tim. 3:16, 17)

 • Ŵerengani Oweruza 7:1-25.

  Kodi tingaphunzire phunziro lotani kwa amuna 300 amene anakhala tcheru mosiyana ndi amene anali osasamala? (Ower. 7:36; Aroma 13:11, 12; Aef. 5:15-17)

  Mofanana ndi mmene amuna 300 aja anaphunzirira mwa kutsanzira Gideoni, kodi ifeyo timaphunzira bwanji mwa kutsanzira Gideoni Wamkulu, Yesu Kristu? (Ower. 7:17; Mat. 11:29, 30; 28:19, 20; 1 Pet. 2:21)

  Kodi lemba la Oweruza 7:21 limatithandiza bwanji kukhala okhutira kutumikira m’njira iliyonse m’gulu la Yehova? (1 Akor. 4:2; 12:14-18; Yak. 4:10)

 • Ŵerengani Oweruza 8:1-3.

  Tikafuna kuthetsa kusiyana maganizo kumene kwabuka ndi mbale kapena mlongo, kodi tingaphunzire chiyani pa mmene Gideoni anathetsera mkangano umene unabuka ndi Aefraimu? (Miy. 15:1; Mat. 5:23, 24; Luka 9:48)