Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 49: Dzuwa Liima

Nkhani 49: Dzuwa Liima

ONANI Yoswa. Akunena kuti: ‘Dzuwa, ima!’ Ndipo dzuwa likuima. Likuima pa malo amodzi kumwamba’ko pakati kwa tsiku lathunthu. Yehova akuzipangitsa kuchitika! Koma tiyeni tione chifukwa chake Yoswa akufuna kuti dzuwa likhala chiwalire.

Dzuwa

Pamene mafumu asanu oipa’wo m’dziko la Kanani anayamba kumenyana ndi Agibeoni, akutumiza munthu kukapempha chithandizo kwa Yoswa. ‘Idzani kwa ife msanga!’ iye akutero. ‘Tipulumutseni! Mafumu onse a ku dziko la mapiri adza kudzalimbana ndi atumiki anu.’

Pa nthawo yomweyo Yoswa ndi ankhondo ake onse akupita. Usiku wonse iwo akuyenda. Pofika ku Gibeoni, asilikali ankhondo a mafumu asanu’wo akuopa ndi kuyamba kuthawa. Pamenepo akubvumbitsa matalala kuchokera kumwamba, ndipo ankhondo ambiri akufa nawo koposa amene akuphedwa ndi ankhondo a Yoswa.

Yoswa

Yoswa akuona kuti posapita nthawi dzuwa lidzalowa. Kudzakhala mdima, ndipo ambiri a asilikari ankhondo a mafumu asanu oipa’wo adzathawa. Ndicho chifukwa chake Yoswa akupemphera kwa Yehova nati: ‘Dzuwa, ima!’ Ndipo pamene dzuwa likuwala chiwalire, Aisrayeli akukhoza kumaliza kupambana nkhondo’yo.

Muli mafumu ena oipa m’Kanani oda anthu a Mulungu. Kukutengera Yoswa ndi ankhondo ake zaka zisanu ndi chimodzi kugonjetsa mafumu 31 a dziko’lo. Pamene zimene’zi zikuchitidwa, Yoswa akutsimikizira kuti dziko la Kanani likugawidwa pakati pa mafuko’wo ofuna chigawo.

Zaka zambiri zikupitapo, ndipo Yoswa potsiriza akufa pa usinkhu wa zaka 110. Kwa utali wonse umene iye ndi mabwenzi ake ali moyo, anthu’wo akumvera Yehova. Koma pa kufa anthu abwino’wa, anthu’wo akuyamba kuchita zoipa nalowa m’bvuto. Ndipo pamene amafuna’di chithandizo cha Mulungu.

Yoswa 10:6-15; 12:7-24; 14:1-5; Oweruza 2:8-13.Mafunso

  • M’chithunzichi, kodi Yoswa akunena kuti chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani akutero?
  • Kodi Yehova akuthandiza bwanji Yoswa ndi amuna ake ankhondo?
  • Kodi Yoswa akugonjetsa mafumu angati, ndipo zikumutengera nthaŵi yaitali bwanji?
  • N’chifukwa chiyani Yoswa akugaŵa dziko la Kanani?
  • Kodi Yoswa akufa ali ndi zaka zingati, ndipo n’chiyani chikuchitikira anthuwo pambuyo pake?

Mafunso ena