Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 48: Agibeoni Anzeru

Nkhani 48: Agibeoni Anzeru

MIZINDA yambiri tsopano m’Kanani ikukonzekera kumenyana ndi Israyeli. Iyo ikuganiza kuti ingapambane. Koma anthu a mzinda wapafupi wa Gibeoni sakuganiza choncho. Akukhulupirira kuti Mulungu akuthandiza Israyeli, ndipo sakufuna kumenyana ndi Mulungu. Chotero kodi mukudziwa chimene iwo akuchita?

Iwo akudzipangitsa kukhala ngati amakhala kutali kwambiri. Chotero ena a amuna’wo akubvala ziguduli ndi nsapato zakutha. Iwo akuika pa abulu ao ziguduli zakutha, ndipo ali ndi mikate yakale youma. Ndiyeno n’kupita kwa Yoswa n’kuti: ‘Tachokera kutali kwambiri, chifukwa tamva za Mulungu wanu wamkulu, Yehova. Tinamva za zinthu zonse zimene anakuchitirani m’Igupto. Tsono atsogoleri athu anatiuza kukonza kamba ndi kudza kudzanena nanu kuti: “Ife ndife atumiki anu. Lonjezani kuti simudzamenyana nafe.” Mungaone kuti zobvala zathu n’zong’ambika chifukwa cha ulendo wautali’wu n’kuti mkate wathu wakhala wakale ndi wouma.’

Yoswa ndi atsogoleri ena akukhulupirira kuti Agibeoni akunena zoona. Chotero akulonjeza kusamenyana nawo. Komano masiku atatu pambuyo pake iwo akumva kuti Agibeoni amakhala’di pafupi.

‘Kodi munatiuziranji kuti mwachokera kutali?’ anafunsa motero Yoswa.

Agibeoni anayankha kuti: ‘Tinatero chifukwa tinauzidwa kuti Mulungu wanu Yehova walonjeza kukupatsani dziko la Kanani’li. Chotero tinaopa kuti mudzatipha.’ Koma Aisrayeli akusunga lonjezo lao, ndipo sakupha Agibeoni. M’malo mwake akuwapanga kukhala atumiki ao.

Mfumu ya Yerusalemu yakwiya chifukwa chakuti Agibeoni apangana mtendere ndi Israyeli. Chotero akuuza mafumu ena anai’wo kuti: ‘Idzani mundithandize kumenyana ndi Gibeoni.’ Ndipo izi ndizo zimene mafumu asanu’wo anachita. Kodi Agibeoni’wo anali anzeru kupangana za mtendere ndi Israyeli, kumene tsopano kukupangitsa mafumu’wa kudza kudzamenya nawo? Tidzaona.

Yoswa 9:1-27; 10:1-5.

Yoswa ndi Agibeoni


Mafunso

  • Kodi anthu a mu mzinda wa Gibeoni ndi osiyana motani ndi Akanani a m’mizinda yoyandikana nawo?
  • Monga momwe asonyezera pachithunzipa, kodi Agibeoni anachita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani anachita zimenezo?
  • Kodi Yoswa ndi atsogoleri a Aisrayeli akuwalonjeza chiyani Agibeoniwo, koma n’chiyani chimene akuzindikira patatha masiku atatu?
  • Kodi chikuchitika n’chiyani mafumu a mizinda ina atamva zoti Agibeoni apangana mtendere ndi Israyeli?

Mafunso ena