Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 43: Yoswa Akhala M’tsogoleri

Nkhani 43: Yoswa Akhala M’tsogoleri

MOSE akufuna kulowa m’Kanani ndi Aisrayeli. Chotero akufunsa kuti: ‘Ndiloleni ndioloke Mtsinje wa Yordano, Yehova, ndi kuona dziko lokoma’li. Koma Yehova akuti: ‘Zakwanira, usaonjeze’nso kunena za izi ndi ine!’ Kodi mukudziwa chifukwa chake Yehova anatero?

N’chifukwa cha zimene zinachitika pamene Mose anamenya thanthwe. Pajatu, iye ndi Aroni sanalemekeze Yehova. Sanauze anthu kuti anali Yehova amene anali kutulutsa madzi m’thanthwe’lo. Chifukwa cha ichi Yehova anati sakawalola kulowa m’Kanani.

Chotero patapita miyezi yowerengeka pambuyo pa imfa ya Aroni, Yehova akuuza Mose kuti: ‘Tenga Yoswa, numuimike pamaso pa Eliezara wansembe ndi anthu. Ndipo pamenepo pamaso pa onse, uuze ali yense kuti Yoswa ndiye m’tsogoleri watsopano.’ Mose akuchita monga momwe’di Yehova akunenera, monga momwe mukuonera m’chithunzi’chi.

Mose akulengeza kuti Yoswa ndi mtsogoleri watsopano

Ndiyeno Yehova akuuza Yoswa kuti: ‘Khala wamphamvu, nulimbe mtima; pakuti udzalowa nao ana a Israyeli m’dziko la Kanani limene ndiwalonjeza, ndipo ndidzakhala nawe.’

Kenako Yehova akuuza Mose kukwera pa Phiri la Nebo m’dziko la Moabu. Ali pamenepo Mose akutha kuona patsidya pa Mtsinje wa Yordano ndi kuona dziko la Kanani lokongola’lo. Yehova akuti: ‘Iri ndiro dziko limene ndinalonjeza kuninkha ana a Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Ndakuonetsa iri, koma sindidzakulola kulowamo.’

Mose akufera pa Phiri la Nebo pamenepo. Iye anali ndi zaka 120. Iye anali wamphamvube, ndipo maso ake anali kuonabe bwino. Anthu ali achisoni kwambiri ndipo akulira chifukwa chakuti Mose wafa. Koma ali okondwa kukhala ndi Yoswa monga m’tsogoleri wao watsopano.

Numeri 27:12-23; Deuteronomo 3:23-29; 31:1-8, 14-23; 32:45-52; 34:1-12.Mafunso

  • M’chithunzichi, kodi anthu aŵiri amene ali ndi Mosewo ndi ndani?
  • Kodi Yehova akuuza Yoswa chiyani?
  • N’chifukwa chiyani Mose akukwera pamwamba pa Phiri la Nebo, ndipo kodi Yehova akumuuza chiyani?
  • Kodi Mose akufa ali ndi zaka zingati?
  • N’chifukwa chiyani anthuwo ali ndi chisoni, koma kodi ali ndi chifukwa chotani chokhalira okondwa?

Mafunso ena