Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Langa la Nkhani za M'baibulo

Nkhani 42: Bulu Alankhula

Nkhani 42: Bulu Alankhula

KODI munayamba mwamva kuti bulu analankhula? ‘Ai,’ mungatero. ‘Zinyama sizingalankhule.’ Koma Baibulo limasimba za bulu amene analankhula. Tiyeni tione m’mene zinachitikira.

Mngelo

Aisrayeli atsala pang’ono kulowa m’Kanani. Balaki, mfumu ya Moabu, ikuopa Aisrayeli. Chotero akutumiza munthu wochenjera wochedwa Balamu kukatemberera Aisrayeli. Balaki akulonjeza kupatsa Balamu ndalama zochuluka, chotero Balamu akukwera pa bulu wake namka ulendo wokaonana ndi Balaki.

Yehova sakufuna kuti Balamu atemberere anthu Ake. Chotero akutumiza mngelo wokhala ndi lupanga kukatsekereza Balamu. Balamu sakuona mngelo’yo koma bulu wake akuona. Chotero bulu’yo akuyesa kupewa mngelo’yo ndipo potsiriza akungogona pansi pa mseu. Balamu wapsya mtima kwambiri, ndipo akupanda bulu’yo ndi ndodo.

Kenako Yehova akuchititsa Balamu kumva bulu’yo akulankhula naye. ‘Ndakuchitanji kuti wandipanda katatu?’ akufunsa motero bulu’yo.

Balamu atakwera bulu

‘Wandiputsitsa,’ akutero Balamu. ‘N’kadakhala ndi lupanga n’kadakupha!’

‘Kodi n’dakuchitirapo zotere n’kale lonse?’ akufunsa tero bulu’yo.

Balamu akuyankha kuti, ‘Ai.’

Ndiyeno Yehova akuonetsa Balamu mngelo wokhala ndi lupanga woima pa njira’yo. Mngelo’yo akuti: ‘Wapandiranji bulu wako? Ndabwera kudzatsekereza njira yako, chifukwa suyenera kumka kukatemberera Israyeli. Bulu wako akadapanda kundipatukira, n’kadakukantha, koma sin’kadabvulaza bulu wako.’

Balamu akuti: ‘Ndachimwa. Sindinadziwe kuti mwaima panjira.’ Mngelo’yo akulola Balamu kupita, ndipo iye akupita kukaonana ndi Balaki. Iye akuyesabe kutemberera Israyeli, koma m’malo mwake, Yehova akum’chititsa kudalitsa Israyeli katatu.

Numeri 21:21-35; 22:1-40; 23:1-30; 24:1-25.Mafunso

 • Kodi Balaki ndi ndani, ndipo n’chifukwa chiyani akuitanitsa Balamu?
 • N’chifukwa chiyani bulu wa Balamu akugona pa msewu?
 • Kodi Balamu akumva buluyo akunena kuti chiyani?
 • Kodi m’ngelo akunena chiyani kwa Balamu?
 • Kodi chikuchitika n’chiyani pamene Balamu akuyesera kutemberera Aisrayeli?

Mafunso ena

 • Ŵerengani Numeri 21:21-35.

  N’chifukwa chiyani Aisrayeli anagonjetsa Mfumu Sihoni ya Aamori ndi Mfumu Ogi ya ku Basana? (Num. 21:21, 23, 33, 34)

 • Ŵerengani Numeri 22:1-40.

  Kodi cholinga cha Balamu poyesera kutemberera Aisrayeli chinali chotani, ndipo kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimenezi? (Num. 22:16, 17; Miy. 6:16, 18; 2 Pet. 2:15; Yuda 11)

 • Ŵerengani Numeri 23:1-30.

  Ngakhale kuti Balamu ankalankhula ngati kuti amalambira Yehova, kodi zochita zake zinasonyeza bwanji kuti sanali wolambira Yehova? (Num. 23:3, 11-14; 1 Sam. 15:22)

 • Ŵerengani Numeri 24:1-25.

  Kodi nkhani ya m’Baibulo imeneyi imalimbitsa bwanji chikhulupiriro chathu choti zolinga za Yehova zidzakwaniritsidwa? (Num. 24:10; Yes. 54:17)